Onani zimene zilipo

Kukaona Malo pa Beteli

Tikuitanani kuti mudzaone maofesi athu a nthambi, amene timayacha kuti Beteli. Maofesi ena a nthambi ali na ma miziyamu yakuti munthu akhoza kudzionela yekha zinthu popanda wina kumutsogolela.

Kuyambilanso Kukayendela Maofesi a Nthambi: Pa June 1, 2023, m'maiko ambili tinayambilanso kulola anthu kukayendela maofesi athu a nthambi. Kuti mumve zambili, funsilani ku ofesi ya nthambi imene mufuna kukayendela. Koma conde, osapitako ngati munapezeka na COVID-19, ngati muli na cimfine, kapena ngati caposacedwa munakhalako pafupi na munthu wodwala COVID-19.

Japan

Watch Tower Bible and Tract Society

4-7-1 Nakashinden

EBINA CITY

KANAGAWA-PREF

243-0496

JAPAN

+81 46-233-0005

Kuona Malo

Pa Mande mpaka pa Cisanu

8:00hrs mpaka 11:00hrs ndi 13:00hrs mpaka 16:00hrs.

Nthawi yoona malo: Maola aŵili

Zimene Timacita

Timasindikiza zofalitsa monga Mabaibulo, tumabuku ndi mabuku zokwanila 15 miliyoni ndiponso magazini oposa 100 miliyoni pa caka. Timatumiza magazini ndi mabuku olemela matani 5,700 a m’zinenelo 150.

Tengani kapepala koonetsa malo.