Onani zimene zilipo

OCTOBER 15, 2024
N’CIANI CATSOPANO

Cilengezo ca Kusintha kwa Zaka Zofunikila Kuti Munthu Ayenelele Kuwonjezela Utumiki Wake Cinapelekedwa pa Miting’i ya Pacaka

Cilengezo ca Kusintha kwa Zaka Zofunikila Kuti Munthu Ayenelele Kuwonjezela Utumiki Wake Cinapelekedwa pa Miting’i ya Pacaka

Pa miting’i ya pacaka ya bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania imene inacitika pa October 5, 2024, panapelekedwa cilengezo cakuti zaka zofunikila kuti munthu ayenelele kufunsila utumiki wa pa Beteli kapena wa zomangamanga m’gulu zacepetsedwa. M’malo moyambila pa zaka 19 ziziyambila pa 18. Nazonso zaka zofunikila kuti munthu ayenelele kufunsila kulowa Sukulu ya Alengezi a Ufumu zacepetsedwa kucoka pa 23 kufika pa 21.

Masinthidwe okondweletsa amenewa ayamba kugwila nchito pompano. Masinthidwe amenewa akupeleka mwayi woculukilapo woti abale ndi alongo acinyamata atumikile Yehova m’mautumiki ofunika amenewa.