Onani zimene zilipo

NOVEMBER 6, 2020
UNITED STATES

Cimphepo Camkuntho Cocedwa Hurricane Zeta Casakaza Kum’mwela Cakum’mawa kwa America

Cimphepo Camkuntho Cocedwa Hurricane Zeta Casakaza Kum’mwela Cakum’mawa kwa America

Malo

Kumwela Cakum’mawa kwa America

Tsoka la Zacilengedwe

  • Cimphepo camphamvu kwambili ca m’gulu laciŵili cinasakaza mzinda wa Louisiana pa October 28, 2020, cikalibe kucepa mphamvu. Cimphepoci cinakhudzanso madela ena a kum’mwela cakum’mawa kwa dziko la America.

  • Cimphepo camkuntho cinakantha madela amene ali mbali mwa nyanja. Ndipo cinawononga manyumba na kupititsa magetsi m’madela ambili.

Mmene abale na alongo athu akhudzidwila

  • ofalitsa okwana 324 asamukila ku malo ena

  • wofalitsa mmodzi anavulazika pang’ono

Kuwonongeka kwa katundu

  • Nyumba zokwanila 291, komanso Nyumba za Ufumu 14 zinawonongeka pang’ono

  • Nyumba zokwanila 8 na Nyumba za Ufumu zitatu zinawonongeka kwambili

  • Nyumba imodzi inawonongekelatu

Cithandizo

  • Akulu a mu mzindawu, komanso oyang’anila madela akucita ubusa na kupeleka cithandizo kwa abale na alongo amene akhudzidwa na tsokali. Ma Komiti Othandizila Pakagwa Tsoka amene anasankhidwa kuti apeleke cithandizo pa mlili wa COVID-19 ndiponso Cimphepo ca Hurricane Laura mu dela limenelo, ndiwonso amene akuthandizila abale amene akhudzidwa na cimphepo ca Hurricane Zeta. Pocita zimenezi Abale athuwa akutsatila ndondomeko za citetezo za mlili wa COVID-19.

N’zoticititsa cisoni kuti cifukwa ca cimphepo camkuntho cimeneci, abale na alongo athu ambili akhudzidwa. Ngakhale n’telo, cikondi cokhulupilika ca Yehova kwa alambili ake, caonekela mwa cithandizo cimene capelekedwa na abale athu.—Salimo 89:1.