Onani zimene zilipo

Makhalidwe Oipa

N’cosavuta kuyamba makhalidwe oipa, koma n’covuta kuwaleka! Cigawo cino cikamba za makhalidwe oipa ambili komanso zimene mungacite kuti muwathetse na kuyamba kucita zabwino.

Kukambitsana

Ningacite Ciani Kuti Nileke Mijedo?

Mukaona kuti makambilano anu asintha n’kukhala mijedo, citamponi kanthu mwansanga!

Mankhwala Osokoneza Bongo

Musawononge Moyo Wanu Mwa Kukoka Fodya

Anthu ambili amakoka fodya kapena kuvepa. Komabe ena analeka ndipo enanso akufunitsitsa kuleka. N’cifukwa ciyani akucita zimenezi? Kodi kukoka fodya kungawonongedi moyo wanu?

Kuseŵenzetsa Bwino Nthawi

Zimene Acinyamata Amakamba Zokhuza Kuzengeleza

Onani zimene acinyamata amakamba zomwe zingapangitse munthu kuzengeleza komanso onani mapindu oseŵenzetsa nthawi yanu mwanzelu.