Onani zimene zilipo

Tukadoli Tojambula Pamanja

Mavidiyo aafupi atukadoli amenewa amaphunzitsa nkhani zikulu-zikulu m’njila yokondweletsa!

 

Musawononge Moyo Wanu Mwa Kukoka Fodya

Anthu ambili amakoka fodya kapena kuvepa. Komabe ena analeka ndipo enanso akufunitsitsa kuleka. N’cifukwa ciyani akucita zimenezi? Kodi kukoka fodya kungawonongedi moyo wanu?

Maseŵela a pa Vidiyo: Kodi Mukupambanadi?

Kuseŵela magemu a pa vidiyo kungakhale kokondweletsa koma kulinso na mavuto ake. Kodi mungatani kuti mupewe mavuto ake n’kumacita zinthu zopindulitsadi?

Zimene Mufunika Kudziŵa Zokhudza Maseŵela

Maseŵela angakuthandizeni kukhala na maluso ena ake, monga kucita zinthu mogwilizana na anthu ena. Kodi maseŵela muyenela kuwaika m’gulu la zinthu zofunika kwambili pa moyo wanu?

Ganizilani Zotulukapo za Kumwa Moŵa

Kucita zinthu cifukwa ca moŵa, anthu ambili amakamba kapena kucita zinthu zimene pambuyo pake amaziimba nazo mlandu. Kodi mungatani kuti mupewe mavuto amene amakhalapo cifukwa comwa kwambili moŵa?

Ningakambe Nawo Bwanji Makolo Anga?

Kodi mungatani kuti mulankhulane ndi makolo anu pamene mukuona ngati simufuna kulankhula?

Kodi Zipangizo Zanu Zimakulamulilani?

Masiku ano anthu ambili akugwilitsa nchito zipangizo zamakono, musamalole kuti zizilamulila moyo wanu. Nanga mungadziŵe bwanji kuti mwayamba kukonda kwambili zipangizo zanu? Ngati mulidi na vutoli kodi mungatani kuti mulithetse?

Kodi Ningacite Ciani kuti Makolo Anga Anipatse Ufulu Wowonjezeleka?

Muona kuti mwakula ndipo makolo anu ayenela kucita namwe zinthu monga wamkulu, koma mwina iwo saona conco. Mungacite ciani kuti iwo ayambe kukudalilani?

Ningacite Ciani Kuti Nileke Mijedo?

Mukaona kuti makambilano anu asintha n’kukhala mijedo, citamponi kanthu mwansanga!

Ndi Cikondi Ceni-ceni Kapena Kutengeka Maganizo Cabe?

Tambani vidiyoyi kuti mudziŵe tanthauzo la kutengeka maganizo ndiponso cikondi ceniceni.

Musagonje Anzanu Pokunyengelelani!

Zinthu 4 zimene zingakuthandizeni kuti muzisankha nokha zocita mwanzelu.

Muzisamala Poceza na Anthu pa Intaneti

Kondwelani koma muzikhala osamala poceza na anthu pa intaneti.

Kodi Bwenzi Leni-leni Limakhala Lotani?

N’zosavuta kupeza anzanu amene sangakuthandizeni, koma kodi mungapeze bwanji mnzanu weniweni?

Kugonjetsa Munthu Amene Akukuvutitsani Popanda Kumenyana Naye

Dziŵani cifukwa cake anthu ena amavutitsa anzawo komanso mmene mungadzitetezele.