Kufotokoza Mavesi a m’Baibo
Dziŵani tanthauzo lenileni la mavesi komanso mawu ena odziŵika bwino a m’Baibo. Ŵelengani mawuwo m’nkhani yake yonse na kudziŵa zimene zinapangitsa kuti alembedwe. Mbaliyi ikuthandizani kumvetsa mozama mawu a Mulungu pogwilitsa nchito mawu am’munsi komanso malifalensi.
Kufotokoza Salimo 37:4—“Udzikondweretsenso mwa Yehova”
Kodi salimoyi imatithandiza bwanji kukhala anthu anzelu komanso kukhala na makhalidwe amene Mulungu amavomeleza?
Salimo 46:10—“Khalani Chete, Ndipo Dziŵani Kuti Ine Ndine Mulungu”
Kodi vesili litanthauze kungokhala chete m’chalichi?
Miyambo 3:5, 6 Lafotokozedwa—“Usamadalile Luso Lako Lomvetsa Zinthu”
Mungaonetse bwanji kuti mumakhulupilila kwambili Mulungu kuposa inu mwini?
Kufotokoza Aroma 10:13—”Adzaitana pa Dzina la Ambuye”
Mulungu anapatsa anthu onse mwayi wopulumuluka na kupeza moyo wosatha. Koma kuti tikapulumuke, tifunika kuitana pa la Mulungu Wamphamvuyonse.