KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBO
Aroma 10:13—”Adzaitana pa Dzina la Ambuye”
“Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”—Aroma 10:13, Baibulo la Dziko Latsopano.
“Pakuti amene ali yense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”—Aroma 10:13, Buku Lopatulika.
Tanthauzo la Aroma 10:13
Mulungu alibe tsankho. Conco anapatsa anthu onse mwayi wopulumuluka na kupeza moyo wosatha mosasamala kanthu za dziko lawo, fuko lawo, kapena udindo umene ali nawo. Koma kuti tikapulumuke, tifunika kuitana pa dzina la Yehova, lomwe ndilo dzina la Mulungu Wamphamvuyonse. a—Salimo 83:18.
M’Baibo, mawu akuti ‘kuitana pa dzina la Yehova’ amatanthauza zambili osati cabe kudziŵa dzina la Mulungu na kuliseŵenzetsa pomulambila. (Salimo 116:12-14) Mawuwa amatanthauzanso kuti tiyenela kukhulupilila Mulungu na kumudalila kuti adzatithandiza.—Salimo 20:7; 99:6.
Yesu Khristu anali kuona kuti dzina la Mulungu n’lofunika kwambili. Mawu ake oyamba m’pemphelo la citsanzo anali akuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.” (Mateyu 6:9) Yesu anaphunzitsanso kuti tiyenela kum’dziŵa Yehova, kumumvela, na kum’konda kuti tikapeze moyo wosatha.—Yohane 17:3, 6, 26.
N’cifukwa ciyani tingakambe kuti Yehova ndiye “Ambuye” wochulidwa pa Aroma 10:13 m’Baibo la Buku Lopatulika? Cifukwa mawu a pa vesili anacokela pa Yoweli 2:32, pamene m’cilankhulo coyambilila ca Ciheberi pali dzina la Mulungu, osati dzina laudindo lakuti “Ambuye.” b
Mavesi ozungulila Aroma 10:13
Pa Aroma caputala 10, Baibo imaonetsa kuti munthu ayenela kukhulupilila Yesu Khristu kuti akhale wovomelezeka kwa Mulungu. (Aroma 10:9) Mfundo imeneyi ikugwilizana na Malemba ambili opezeka m’Cipangano Cakale. Munthu amaonetsa kuti ali na cikhulupililo ngati “amalengeza poyela” uthenga wabwino wa cipulumutso kwa anthu osakhulupilila. Mwa kutelo, anthu ena amakhala na mwayi wokulitsa cikhulupililo cimene cidzaŵathandiza kukapeza moyo.—Aroma 10:10, 14, 15, 17.
Ŵelengani Aroma caputala 10 limodzi na mawu a m’munsi ofotokozela malemba komanso malifalensi ake.
a Dzina la Mulungu limapezeka nthawi pafupifupi 7,000 m’mipukutu yakale ya Baibo. M’Ciheberi, dzinali linalembedwa na zilembo zinayi. M’Cinyanja, dzinali nthawi zambili limamasulidwa kuti Yehova, koma anthu ena amati “Yahweh.”
b Zioneka kuti Akhristu amene analembako Baibo anali kuseŵenzetsa dzina la Mulungu akagwila mawu a “M’cipangano Cakale” okhala na dzinalo. Buku lina lakuti The Anchor Bible Dictionary linati: “Pali umboni woonetsa kuti poyamba, pamene Cipangano Catsopano cinali kulembedwa, zilembo zinayi zoimila dzina la Mulungu, Yahweh, zinali kupezeka pafupifupi m’malemba onse amene anagwila mawu cipangano cakale.” (Volume 6, tsamba 392) Kuti mudziŵe zambili onani nkhani yakuti “Dzina la Mulungu MʼMalemba a Chigiriki” pa Zakumapeto A5 mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika. M’Baibo yophunzilila yacingelezi pa Zakumapeto C2 pali mndandanda wa Mabaibo amene anaseŵenzetsa dzina la Mulungu pa Aroma 10:13.