KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBO
Salimo 37:4—“Udzikondweretsenso mwa Yehova”
“Uzisangalala cifukwa ca Yehova, Ndipo adzakupatsa zimene mtima wako umalakalaka.”—Salimo 37:4, Baibulo la Dziko Latsopano.
“Udzikondweretsenso mwa Yehova; Ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.”—Salimo 37:4, Buku Lopatulika.
Tanthauzo la Salimo 37:4
Wamasalimo akulimbikitsa alambili a Mulungu kupeza cimwemwe mwa kukhala paubale wolimba na Mulungu. Onse amene amakondwela cifukwa cokhala paubale na Yehova a Mulungu angakhale na cidalilo cakuti iye azaŵapatsa zonse zimene iwo amalaka-laka.
“Uzisangalala cifukwa ca Yehova.” Mawuwa angamasulidwenso kuti “pezani cimwemwe cacikulu cifukwa ca Yehova,” “pezani cimwemwe potumikila AMBUYE,” kapena “pezani cimwemwe pa zimene AMBUYE walonjeza.” Mfundo yake ni yakuti, tizipeza “cimwemwe [cathu] cacikulu” polambila Mulungu woona. (Salimo 37:4,) Cifukwa ciyani takamba conco?
Anthu amene amalambila Yehova amaona zinthu mmene iye amazionela, malinga na zimene Baibo imanena. Iwo amamudziŵadi Mulungu ndipo amaona kuti ni nzelu kumumvela. Kucita zimenezi, kumaŵathandiza kukhala na cikumbumtima coyela na kupewa mavuto obwela cifukwa copanga zisankho zolakwika. (Miyambo 3:5, 6) Mwacitsanzo, alambili a Mulungu sakwiya kapena kucitila nsanje anthu adyela kapena osaona mtima amene amaoneka kuti zinthu zikuŵayendela bwino. (Salimo 37:1, 7-9) Anthu a Mulungu amakhala okondwela podziŵa kuti posacedwa iye adzathetsa zinthu zonse zopanda cilungamo, komanso kuti adzadalitsa anthu okhulupilika amene ali na makhalidwe abwino. (Salimo 37:34) Iwo amakhalanso acimwemwe podziŵa kuti ni oyanjidwa na Atate wawo Wakumwamba.—Salimo 5:12; Miyambo 27:11.
“Adzakupatsa zimene mtima wako umalakalaka.” Mawu awa angamasulidwenso kuti “adzayankha mapemphelo anu” kapena kuti “adzakupatsani zimene mumafunitsitsa.” Koma Yehova sadzangotipatsa ciliconse cimene tamupempha. Mofanana na kholo labwino, Yehova amadziŵa zabwino koposa zimene ana ake amafunikila. Kuwonjezela apo, zopempha zathu na zocita zathu ziyenela kugwilizana na miyezo yake komanso cifunilo cake. (Miyambo 28:9; Yakobo 4:3; 1 Yohane 5:14) Tikacita zimenezi tingapemphele kwa “Wakumva pemphelo” tili na cikhulupililo camphamvu cakuti adzatiyankha.—Salimo 65:2; Mateyu 21:22.
Mavesi Ozungulila Salimo 37:4
Salimo 37 inalembedwa na Mfumu Davide wa ku Isiraeli wakale. Analemba Salimoli potsatila ndondomeko ya alifabeti. b
Davide anacitidwa zinthu zambili zopanda cilungamo. Anali kusakidwa na Mfumu Sauli komanso anthu ena amene anali kufuna kumupha. (2 Samueli 22:1) Koma nthawi zonse Davide anali kudalila Mulungu wake na mtima wonse. Davide anali kudziŵa kuti tsiku lina Yehova adzalanga anthu oipa. (Salimo 37:10, 11) Ngakhale aoneke kuti zinthu zikuwayendela bwino mofanana na “msipu wobiliwila,” nthawi idzafika pamene iwo adzawonongedwa.—Salimo 37:2, 20, 35, 36.
Salimo 37 imaonetsa zimene zidzacitikila anthu amene amatsatila malamulo a Mulungu, komanso zimene zidzacitikila amene amanyalanyaza malamulo amenewa. (Salimo 37:16, 17, 21, 22, 27, 28) Conco salimo imeneyi imatithandiza kukhala anthu anzelu komanso kukhala na makhalidwe amene Mulungu amakondwela nawo.
Tambani vidiyo yaifupi iyi imene ifotokoza mfundo za m’buku la Masalimo.
a Yehova ndilo dzina lodziŵika la Mulungu m’Cinyanja likamasulidwa kucoka m’Ciheberi. Kuti mudziŵe cifukwa cake Mabaibo ambili anagwilitsa nchito dzina laudindo lakuti Ambuye m’malo moseŵenzetsa dzina lenileni la Mulungu, onani nkhani yakuti “Kodi Yehova N’ndani?”
b M’kalembedwe kameneka, vesi loyamba kapena mavesi angapo oyambilila amayamba na cilembo coyamba mu alifabeti ya Ciheberi. Ndipo mavesi ena otsatila amayamba na zilembo zina potsatila alifabeti. Kalembedwe kameneka kayenela kuti kanathandiza anthu kukumbukila salimoli.