KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBO
Salimo 46:10—“Khalani Chete, Ndipo Dziŵani Kuti Ine Ndine Mulungu”
“Gonjelani ndipo mudziŵe kuti ine ndine Mulungu. Ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu, ndidzakwezedwa padziko lapansi.”—Salimo 46:10, Baibulo la Dziko Latsopano.
“Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu: ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka pa dziko lapansi.”—Salimo 46:10, Buku Lopatulika.
Tanthauzo la Salimo 46:10
Mulungu amalimbikitsa anthu onse kuti azimulambila na kuvomeleza kuti iye ndiye woyenela kulamulila dziko lonse lapansi. Aliyense amene afuna kudzakhala kwamuyaya ayenela kuvomeleza mfundo yosatsutsika yakuti iye ali na mphamvu komanso ulamulilo.—Chivumbulutso 4:11.
“Gonjelani ndipo mudziwe kuti ine ndine Mulungu.” Mabaibo ena anamasulila mbali yoyamba ya vesili kuti “khalani chete.” Zimenezi zacititsa anthu ambili kumva vesili molakwika, n’kumaganiza kuti limeneli ni lamulo lakuti azicita zinthu mwamantha kapena azikhala cete m’chalichi. Komabe, mawu a Ciheberi omasulidwa kuti “gonjelani ndipo mudziŵe kuti ine ndine Mulungu” ni pempho locokela kwa Yehova a Mulungu kuti anthu amitundu yonse asiye kumutsutsa ndipo avomeleze kuti iye yekha ndiye woyenela kulambilidwa.
Pempho lofanana na limeneli limapezekanso pa Salimo 2. Pa lembali, Mulungu analonjeza kuti adzawononga anthu onse amene amamutsutsa. Koma anthu onse amene amavomeleza ulamulilo wa Mulungu amamudalila kuti aziwatsogolela, kuŵapatsa mphamvu komanso nzelu. Iwo akakhala pa mavuto, amakhala acimwemwe komanso otetezeka cifukwa “amathaŵila kwa iye.”—Salimo 2:9-12.
“Ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu, ndidzakwezedwa padziko lapansi.” M’nthawi zakale, Yehova Mulungu anali kukwezedwa kapena kuti kutamandidwa akaseŵenzetsa mphamvu zake zazikulu poteteza anthu ake. (Ekisodo 15:1-3) M’tsogolomu, iye adzakwezedwa kwambili pa nthawi imene anthu onse padziko lapansi adzagonjela ulamulilo wake na kumulambila—Salimo 86:9, 10; Yesaya 2:11.
Mavesi ozungulila Salimo 46:10
Buku lina linati Salimo 46 ni “nyimbo yotamanda mphamvu za Mulungu, mpulumutsi wamkulu wa anthu ake.” Poimba Salimo 46, anthu a Mulungu anali kuonetsa cidalilo cawo cakuti Yehova ali na mphamvu zowateteza na kuwathandiza. (Salimo 46:1, 2) Mawu a mu Salimoli anali kuŵakumbutsa kuti nthawi zonse Yehova anali nawo.—Salimo 46:7, 11.
Salimoli linalimbikitsa anthu a Mulungu kuti azidalila kwambili mphamvu za Yehova Mulungu zowateteza, komanso kuti aziganizila mphamvu zake zodabwitsa. (Salimo 46:8) Kwakukulu-kulu, lionetsa kuti iye ali na mphamvu zothetselatu nkhondo. (Salimo 46:9) Ndipo m’mbuyomu Yehova anathetsapo nkhondo mwa kuteteza anthu ake kwa adani awo. Komabe, Baibo imalonjeza kuti Mulungu adzacita zimenezi pa mlingo waukulu pa nthawi imene adzathetsa nkhondo padziko lonse lapansi.—Yesaya 2:4.
Kodi Yehova akali kuthandiza atumiki ake masiku ano? Inde. Ndipo mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kudalila Yehova kuti adzaŵathandiza. (Aheberi 13:6) Mfundo za mu Salimo 46 zimalimbitsa cidalilo cathu cakuti Mulungu ali na mphamvu zotiteteza. Zimatithandiza kuona kuti Mulungu ni “pothaŵila pathu komanso mphamvu yathu.”—Salimo 46:1.
Tambani vidiyo yaifupi iyi imene ifotokoza mfundo za m’buku la Masalimo.
a Yehova ndilo dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova N’ndani?”