Onani zimene zilipo


KUPHUNZILA BAIBO MOTHANDIZIDWA NA MUNTHU WINA

Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!

Maphunzilo a Baibo okambilana amenewa ni aulele. Pamene muphunzila mudzapeza mayankho a mafunso ngati awa:

  • Ningacite ciyani kuti nizikhala wokondwela?

  • Kodi mavuto na zinthu zoipa zidzathadi?

  • Kodi ningadzaŵaonenso okondedwa anga omwe anamwalila?

  • Kodi Mulungu amasamaladi za ine?

  • Ningapemphele bwanji kuti Mulungu azimva mapemphelo anga?

Sitilipilitsa

Pa nthawi yonse yomwe mudzakhala mukuphunzila simudzalipila ndalama iliyonse. Buku lophunzilila la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! komanso Baibo ni zaulele.

Potengela Zimene Mungakonde

Muzikumana na mphunzitsi wanu pamasom’pamaso kapena muziphunzilila pafoni, panthawi na malo omwe mungakonde.

Simudzakakamizidwa

Mungathe kusintha nthawi na malo ophunzilila. Mukafuna kuleka kuphunzila, ndinu omasuka kutelo.

Kodi phunzilo la Baibo limacitika bwanji?

Mphunzitsi wanu adzakuthandizani kudziŵa zomwe Baibo imaphunzitsa, mwa kuphunzila mutu uliwonse pawokha-pawokha. Poseŵenzetsa buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!, mwa pang’ono-pang’ono mudzaphunzila zimene Baibo imakamba komanso mmene ingakuthandizileni. Kuti mudziŵe zambili, tambani vidiyoyi kapena onani mafunso omwe anthu amafunsa kaŵili-kaŵili pa nkhani ya maphunzilo amenewa.

Mungakonde kuonako nkhani zina zili m’bukuli?

Onani maphunzilo oyambilila a m’bukuli.

Mwakonzeka kuyamba kuphunzila?

Dinizani mawu ali m’munsiwa kuti mupemphe munthu amene mungayambe kuphunzila naye.