Kodi Baibo Ingathandize Anthu Odwala Matenda Osathelapo?
Yankho la m’Baibo
Inde. Mulungu amasamalila atumiki ake amene akudwala. Ponena za mtumiki wokhulupilika wina, Baibo imati: “Yehova adzacilikiza wonyozekayo pamene akudwala pabedi lake.” (Salimo 41:3) Conco, ngati muli na matenda osathelapo, njila zitatu zotsatilazi zingakuthandizeni:
Pemphelelani mphamvu kuti mupilile. “Mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse,” ungakuthandizeni kucepetsa nkhawa. Ndipo mungakondwele na umoyo ngakhale muli na mavuto.—Afilipi 4:6, 7.
Muzikhalako na maganizo wosangalala. Baibo imati: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ocilitsa, koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.” (Miyambo 17:22) Kukhalako wosangalala kungakuthandizeni kucepetsa cisoni, komanso zingakhale zopindulitsa ku thanzi lanu.
Khalani na cikhulupililo m’malonjezo a Mulungu a kutsogolo. Kukhala na ciyembekezo cabwino ca zamtsogolo, kungakuthandizeni kukhala wokondwela olo kuti muli na matenda osathelapo. (Aroma 12:12) Baibo inakambilatu za nthawi pamene “Palibe munthu adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’” (Yesaya 33:24) Mulungu adzacotsapo matenda onse amene anthu alephela kuthetsa. Mwacitsanzo, Baibo imakamba kuti okalamba adzabwelela kuunyamata. Imati: “Mnofu wake usalale kuposa mmene unalili ali mnyamata. Abwelele ku masiku ake aunyamata pamene anali ndi mphamvu.”—Yobu 33:25.
Dziŵani izi: Ngakhale kuti Mboni za Yehova zimadalila thandizo la Yehova, zimafunanso cithandizo ca cipatala pa matenda osathelapo. (Maliko 2:17) Komabe, sitikakamiza anthu kulandila cithandizo cinacake ca cipatala, cifukwa munthu aliyense ayenela kupanga yekha cosankha pa nkhani zimenezi.