Kodi Nkhondo ya Aramagedo N’ciyani?
Yankho la m’Baibo
Aramagedo ni nkhondo yothela ya pakati pa maboma a anthu na Mulungu. Ngakhale panopa, maboma amenewa pamodzi na otsatila awo amatsutsa Mulungu pokana kugonjela ulamulilo wake. (Salimo 2:2) Conco, nkhondo ya Aramagedo idzathetsa ulamulilo uliwonse wa anthu.—Danieli 2:44.
Mawu akuti “Aramagedo” amapezeka kamodzi kokha m’Baibo, pa Chivumbulutso 16:16. Ulosi wa m’buku la Chivumbulutso umaonetsa kuti “mafumu a dziko lonse lapansi” adzasonkhanitsidwa “pamodzi kumalo amene m’Ciheberi amachedwa Aramagedo,” “kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.”—Chivumbulutso 16:14.
Ndani adzamenya nkhondo ya Aramagedo? Yesu Khristu adzatsogolela gulu lankhondo la kumwamba pokagonjetsa adani a Mulungu. (Chivumbulutso 19:11-16, 19-21) Adani amenewa ni amene amatsutsa ulamulilo wa Mulungu komanso amene samulemekeza.—Ezekieli 39:7.
Kodi nkhondo ya Aramagedo idzacitikila kumaiko a ku Middle East? Ayi. Nkhondo ya Aramagedo sidzamenyedwa m’dela limodzi. M’malo mwake, nkhondoyi idzacitika padziko lonse lapansi.—Yeremiya 25:32-34; Ezekieli 39:17-20.
Mawu akuti Aramagedo, amene nthawi zina amalembedwa kuti “Haramagedo” (m’Ciheberi Har Meghiddohnʹ), amatanthauza “Phiri la Megido.” Kale kwambili, Megido unali mzinda ku Isiraeli. Mbili yakale imaonetsa kuti nkhondo zoopsa kwambili zinali kucitikila m’dela limenelo, kuphatikizapo zina zimene zimachulidwa m’Baibo. (Oweruza 5:19, 20; 2 Mafumu 9:27; 23:29) Komabe, mawu akuti Aramagedo satanthauza malo enieni pafupi na mzinda wakale wa Megido. Kudela limenelo kulibe phili lalikulu limene adani onse a Mulungu angakwanepo, olo titaphatikiza malo onse a m’cigwa ca Yezereeli. M’malo mwake, mawu akuti Aramagedo atanthauza zimene zidzacitike padziko lonse, anthu a mitundu yonse akadzasonkhana pofuna kulimbana komaliza na ulamulilo wa Mulungu.
Kodi zinthu zidzakhala bwanji pa nkhondo ya Aramagedo? Ngakhale kuti sitidziŵa mmene Mulungu adzaseŵenzetsela mphamvu zake poononga adani ake, tidziŵa kuti ali na zida zimene anazigwilitsapo nchito m’mbuyomo, monga matalala, zivomezi, mvula yoopsa, moto na sulufule, mphenzi, komanso milili. (Yobu 38:22, 23; Ezekieli 38:19, 22; Habakuku 3:10, 11; Zekariya 14:12) Tidziŵanso kuti adani ena a Mulungu adzaphana okha-okha cifukwa cosokonezeka. Koma pamapeto pake adzadziŵa kuti Mulungu ni amene akucititsa zimenezo.—Ezekieli 38:21, 23; Zekariya 14:13.
Kodi dziko lidzatha pa Aramagedo? Sikuti Aramagedo idzawononga kapena kuthetsa dziko lapansili ayi. Dzikoli ni malo okhalamo anthu mpaka kale-kale. (Salimo 37:29; 96:10; Mlaliki 1:4) Ndipo nkhondo ya Aramagedo sikuti idzawononga anthu onse, koma idzathandiza kuti anthu ena apulumuke. Anthuwo ni “khamu lalikulu” la atumiki a Mulungu.—Chivumbulutso 7:9, 14; Salimo 37:34.
M’Baibo mawu kuti “dziko” nthawi zambili amatanthauza dziko lapansi leni-leni. Koma nthawi zina mawuwa amatanthauzanso anthu ocita zoipa osamvela Mulungu. (1 Yohane 2:15-17) Conco, tingakambe kuti nkhondo ya Aramagedo idzabweletsa “mapeto a dziko,” kutanthauza anthu ocita zoipa.—Mateyu 24:3.
Kodi Aramagedo idzacitika liti? Pofotokoza za “cisautso cacikulu” cimene cidzatha pa nkhondo ya Aramagedo, Yesu anati: “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziŵa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyu 24:21, 36) Ngakhale zili conco, Baibo imaonetsa kuti nkhondo ya Aramagedo idzacitika pa nthawi imene Yesu adzakhala pampando wacifumu koma mosaonekela kwa anthu. Nthawi imeneyi inayamba mu 1914.—Mateyu 24:37-39.