Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Russia

 

2017-07-21

RUSSIA

Akuluakulu a Boma ku Russia Anathokoza Mwapadera a Mboni za Yehova Kuphatikizapo Nzika ya ku Denmark Yomwe ili M’ndende

Akuluakulu mumzinda wa Oryol anathokoza a Mboni za Yehova kuphatikizapo nzika ina ya ku Denmark yomwe ili m’ndende. Iwo anathokoza Amboniwo chifukwa chogwira nawo ntchito yoyeretsa mumzindawo yomwe imachitika chaka chilichonse.

2017-07-25

RUSSIA

A Mboni za Yehova Ochokera M’mayiko Osiyanasiyana Analimbikitsa Abale Awo a ku Russia pa Nthawi Yozenga Mlandu wa Apilo

Bungwe Lolamulira linatumiza abale ochokera m’mayiko osiyanasiyana kupita ku Moscow.

2017-07-21

RUSSIA

Vidiyo Yosonyeza Apolisi ku Russia Akusokoneza Misonkhano ya Mboni za Yehova

Vidiyo yomwe bungwe lina lofalitsa nkhani ku Russia linatulutsa inasonyeza apolisi a Federal Security Service omwe anali ndi zida akusokoneza misonkhano imene a Mboni za Yehova ankapanga mumzinda wa Oryol ku Russia.

2017-07-21

RUSSIA

Vidiyo Yosonyeza Apolisi ku Russia Akusokoneza Misonkhano ya Mboni za Yehova

Pa 25 May 2017, apolisi a Federal Security Service (FSB) omwe anali ndi zida anasokoneza misonkhano imene a Mboni za Yehova ankachita mwamtendere mumzinda wa Oryol ku Russia.

2017-03-22

RUSSIA

A Mboni za Yehova Padziko Lonse Akulimbikitsidwa Kulemba Makalata Opempha Kuti Boma la Russia Lisaletse Ntchito Yawo M’dzikolo

Boma la Russia laopseza kuti liletsa ntchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo. Choncho a Mboni za Yehova padziko lonse aganiza zolemba makalata opita ku boma la Russia ndiponso kwa akuluakulu a Khoti Lalikulu m’dzikolo. Pali malangizo omwe angathandize aliyense amene akufuna kulemba nawo makalatawa.