Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto 4:1-21

  • Atumiki ayenera kukhala okhulupirika (1-5)

  • Atumiki a Chikhristu ayenera kukhala odzichepetsa (6-13)

    • ‘Musapitirire zolembedwa’ (6)

    • Akhristu akuonetsedwa mʼbwalo lamasewera (9)

  • Paulo ankasamalira ana ake auzimu (14-21)

4  Anthu azitha kuona kuti ndife atumiki a Khristu ndiponso atumiki a zinsinsi zopatulika za Mulungu.+  Pa nkhani imeneyi, chofunika kwa atumiki ndi kukhala okhulupirika.  Zoti ndiweruzidwe ndi inu kapena ndi khoti* lililonse la anthu si nkhani kwa ine. Ndipotu ngakhale ineyo sindidziweruza ndekha.  Mumtima mwanga sindikudzitsutsa pa nkhani iliyonse. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti basi ndine wolungama, chifukwa Yehova* ndi amene amandifufuza.+  Choncho musaweruze+ chilichonse nthawi isanakwane, mpaka Ambuye adzafike. Iye adzachititsa kuti zinsinsi zamumdima zionekere komanso adzaonetsa poyera zimene zili mumtima. Ndiyeno aliyense payekha adzayamikiridwa ndi Mulungu.+  Tsopano abale, ndanena zinthu zimenezi zokhudza ineyo ndi Apolo+ kuti mumvetse mfundo yake nʼcholinga choti muphunzire kwa ife lamulo lakuti: “Musapitirire zinthu zolembedwa.” Sitikufuna kuti aliyense wa inu akhale wodzikuza+ nʼkumachita zinthu mokondera.  Kodi akukupangitsa kukhala wosiyana ndi ena ndi ndani? Ndipo uli ndi chiyani chimene sunachite kulandira?+ Ndiye ngati unachita kulandira zinthu zimenezo, nʼchifukwa chiyani ukudzitama ngati kuti sunachite kulandira?  Kodi mwakhuta kale? Mwalemera kale eti? Kodi mwayamba kale kulamulira ngati mafumu+ popanda ife? Ndikanakondadi mukanayamba kulamulira ngati mafumu, kuti ifenso tizilamulira nanu limodzi ngati mafumu.+  Ndikuona ngati Mulungu waika atumwife kumapeto pachionetsero ngati anthu okaphedwa,+ chifukwa zili ngati tili mʼbwalo lamasewera ndipo tikuonetsedwa kudziko,+ kwa angelo ndiponso kwa anthu. 10  Takhala opusa+ chifukwa cha Khristu, koma inu mwakhala ochenjera mwa Khristu. Ife ndife ofooka, inu ndinu amphamvu. Inu mukulemekezedwa, koma ifeyo tikunyozedwa. 11  Mpaka pano tikadali anjala,+ aludzu+ ndiponso ausiwa. Tikumenyedwabe,+ tikusowabe pokhala 12  ndipo tikugwirabe ntchito mwakhama ndi manja athu.+ Akamatinenera zachipongwe, timadalitsa+ ndipo akamatizunza, timapirira moleza mtima.+ 13  Akamatinenera zoipa, timayankha mofatsa.+ Mpaka pano, tikuonedwa ngati zinyalala za dziko ndiponso nyansi za zinthu zonse. 14  Sindikulemba zinthu zimenezi kuti ndikuchititseni manyazi, koma kuti ndikulangizeni ngati ana anga okondedwa. 15  Ngakhale mutakhala ndi anthu okuyangʼanirani 10,000 mwa Khristu, mulibe abambo ambiri. Ine ndine bambo anu mwa Khristu Yesu chifukwa ndinakubweretserani uthenga wabwino.+ 16  Choncho ndikukulimbikitsani kuti muzitsanzira ineyo.+ 17  Nʼchifukwa chake ndikukutumizirani Timoteyo, popeza iye ndi mwana wanga wokondedwa ndiponso wokhulupirika mwa Ambuye. Iye adzakukumbutsani mmene ndimachitira zinthu potumikira Khristu Yesu+ komanso mmene ndimaphunzitsira kulikonse, mumpingo uliwonse. 18  Ena amadzikuza ngati kuti sindidzabwera kwanuko. 19  Koma Yehova* akalola ndibwera posachedwapa, ndipo sindidzafuna kumva mawu awo odzikuzawo, koma ndidzafuna ndione mphamvu zawo. 20  Chifukwa Ufumu wa Mulungu si nkhani ya mawu, koma mphamvu. 21  Kodi mungasankhe chiyani? Ndibwere kwa inu ndi chikwapu,+ kapena ndibwere mwachikondi komanso mofatsa?

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “bwalo.”