Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto 5:1-13

  • Nkhani ya munthu yemwe anachita chiwerewere (1-5)

  • Zofufumitsa zochepa zimafufumitsa mtanda wonse (6-8)

  • Munthu woipa anayenera kuchotsedwa (9-13)

5  Mbiri yamvekatu kuti pakati panu pakuchitika chiwerewere*+ ndipo chiwerewere chake ndi choti ngakhale anthu a mitundu ina sachita. Akuti mwamuna wina watengana ndi mkazi wa bambo ake.+  Kodi mukunyadira zimenezi mʼmalo momva chisoni,+ kuti munthu amene wachita zimenezi achotsedwe pakati panu?+  Ngakhale kuti sindili kumeneko, mumzimu ndili komweko, ndipo ndamuweruza kale munthu amene wachita zimenezi, ngati kuti ndili nanu komweko.  Mukasonkhana mʼdzina la Ambuye wathu Yesu, mudziwe kuti ndili nanu limodzi mumzimu komanso mumphamvu ya Ambuye wathu Yesu.  Choncho mupereke munthu ameneyu kwa Satana+ kuti thupilo liwonongedwe, nʼcholinga choti mzimuwo* upulumutsidwe mʼtsiku la Ambuye.+  Kudzitama kwanu si kwabwino. Kodi simukudziwa kuti zofufumitsa zapangʼono zimafufumitsa mtanda wonse wa ufa wokandakanda?+  Chotsani zofufumitsa zakalezo, kuti mukhale mtanda watsopano, popeza ndinu opanda zofufumitsa. Chifukwa Khristu waperekedwa ngati nsembe+ yathu ya Pasika.+  Choncho tiyeni tichite Chikondwerero cha Pasikachi,+ osati ndi zofufumitsa zakale, kapena zofufumitsa zoimira zoipa ndi uchimo, koma ndi mkate wopanda zofufumitsa woimira kuona mtima ndi choonadi.  Mʼkalata yanga, ndinakulemberani kuti musiye kugwirizana ndi anthu achiwerewere.* 10  Sindikutanthauza kuti muzipeweratu anthu achiwerewere* amʼdzikoli+ kapenanso adyera, olanda ndi opembedza mafano. Kuti muchite zimenezo, ndiye mungafunike kutuluka mʼdzikoli.+ 11  Koma tsopano ndikukulemberani kuti musiye kugwirizana+ ndi aliyense wotchedwa mʼbale, amene ndi wachiwerewere* kapena wadyera,+ wopembedza mafano, wolalata, chidakwa+ kapenanso wolanda,+ ngakhale kudya naye munthu wotereyu ayi. 12  Nanga ndi udindo wanga kuweruza anthu amene ali kunja?* Kodi inu si paja mumaweruza anthu amene ali mkati, 13  ndipo Mulungu amaweruza amene ali kunja?+ “Mʼchotseni munthu woipayo pakati panu.”+

Mawu a M'munsi

MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kutanthauza mzimu wabwino wa mpingo.
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Amenewa ndi anthu amene sali mumpingo wa Chikhristu.