Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto 6:1-20

  • Akhristu ankatengerana kukhoti (1-8)

  • Anthu amene sadzalowa mu Ufumu (9-11)

  • Lemekezani Mulungu ndi matupi anu (12-20)

    • “Thawani chiwerewere” (18)

6  Kodi wina wa inu akakhala ndi mlandu ndi mnzake,+ amalimba mtima kupita kukhoti kwa anthu osalungama, osati kwa oyerawo?  Kodi simukudziwa kuti oyerawo adzaweruza dziko?+ Ndipo ngati mudzaweruza dziko, kodi simungathe kuzenga milandu yaingʼono kwambiri ngati imeneyo?  Kodi simukudziwa kuti tidzaweruza angelo?+ Ndiye tingalephere bwanji kuweruza nkhani zamʼmoyo uno?  Choncho, ngati muli ndi nkhani zamʼmoyo uno zofunika kuweruza,+ kodi mukupereka udindo woweruza kwa anthu amene mpingo sungawadalire?  Ndikulankhula zimenezi kuti ndikuchititseni manyazi. Kodi pakati panu palibe wanzeru ndi mmodzi yemwe amene angaweruze milandu ya abale ake?  Kodi mʼbale azitengera mʼbale wake kukhoti, kwa anthu osakhulupirira?  Kunena zoona, ngati mukutengerana kukhoti ndiye mwalepheratu. Bwanji osangolola kulakwiridwa?+ Bwanji osalola kuberedwa?  Mʼmalomwake, inuyo mumachita zolakwika ndiponso mumabera ena ndipo mumachitira zimenezi abale anu.  Kodi zoonadi inu simukudziwa kuti anthu osalungama sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu?+ Musapusitsidwe.* Achiwerewere,*+ olambira mafano,+ achigololo,+ amuna amene amalola kugonedwa ndi amuna anzawo,+ amuna ogona amuna anzawo,+ 10  akuba, adyera,+ zidakwa,+ olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu.+ 11  Ndipo ena a inu munali otero. Koma mwasambitsidwa kukhala oyera,+ mwapatulidwa,+ mukuonedwa ngati olungama+ mʼdzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, komanso ndi mzimu wa Mulungu wathu. 12  Zinthu zonse ndi zololeka kwa ine, koma si zonse zimene zili zaphindu.+ Zinthu zonse ndi zololeka kwa ine, koma sindidzalola kuti chinthu china chizindilamulira. 13  Chakudya ndi cha mimba, ndipo mimba ndi ya chakudya, koma Mulungu adzawononga mimba ndi chakudya chomwe.+ Thupi si lochitira chiwerewere,* koma ndi la Ambuye+ ndipo Ambuye ndi amene amapereka zofunika mʼthupi. 14  Koma Mulungu anaukitsa Ambuye+ ndipo adzaukitsanso ifeyo+ pogwiritsa ntchito mphamvu zake.+ 15  Kodi simukudziwa kuti matupi anu ndi ziwalo za Khristu?+ Ndiye kodi ine nditenge ziwalo za Khristu nʼkuzichititsa kukhala ziwalo za hule? Zosatheka zimenezo! 16  Kodi inu simukudziwa kuti amene wagonana ndi hule amakhala thupi limodzi ndi huleyo? Chifukwa anati, “Awiriwo adzakhala thupi limodzi.”+ 17  Koma amene wagwirizana ndi Ambuye amakhala naye limodzi mumzimu.+ 18  Thawani chiwerewere.*+ Tchimo lililonse limene munthu angachite ndi la kunja kwa thupi lake, koma amene amachita chiwerewere amachimwira thupi lake.+ 19  Kodi inu simukudziwa kuti thupi lanu ndi kachisi+ wa mzimu woyera umene uli mwa inu, womwe munapatsidwa ndi Mulungu?+ Ndiponso mwiniwake wa inuyo si inu,+ 20  chifukwa munagulidwa pa mtengo wokwera.+ Mulimonse mmene zingakhalire, lemekezani Mulungu+ ndi matupi anu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Musasocheretsedwe.”
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.