Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto 8:1-13

  • Chakudya choperekedwa kwa mafano (1-13)

    • Kwa ife kuli Mulungu mmodzi (5, 6)

8  Tsopano ponena za zakudya zoperekedwa kwa mafano,+ tikudziwa kuti tonse ndife odziwa zinthu.+ Kudziwa zinthu kumachititsa munthu kukhala wodzikuza, koma chikondi chimalimbikitsa.+ 2  Ngati wina akuganiza kuti akudziwa zinazake, sanazidziwebe mokwanira. 3  Koma ngati munthu amakonda Mulungu, ameneyo amadziwika kwa Mulungu. 4  Ndiyeno pa nkhani ya kudya zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano si kanthu+ ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+ 5  Anthu amati pali milungu yambiri, kaya kumwamba kapena padziko lapansi.+ Choncho kwa anthu amenewo palidi milungu yambiri ndi ambuye ambiri. 6  Koma kwa ife Mulungu alipo mmodzi yekha,+ amene ndi Atate.+ Zinthu zonse zinachokera kwa iye, ndipo ifeyo ndife ake.+ Palinso Ambuye mmodzi, Yesu Khristu, amene zinthu zonse zinakhalapo kudzera mwa iye,+ ndipo ifeyo kudzera mwa iyeyo. 7  Komabe si onse amene amadziwa zimenezi.+ Ena, chifukwa choti poyamba ankalambira mafano, akamadya chakudya choperekedwa kwa mafano amachiona ngati choperekedwadi kwa mafano.+ Kenako chikumbumtima chawo chimawavutitsa popeza nʼchofooka.+ 8  Koma chakudya sichingatithandize kuyandikira Mulungu.+ Ngati sitinadye chakudyacho, sikuti talakwa, ndipo ngati tadya, sikuti ndife abwino kwambiri kwa iyeyo.+ 9  Koma muzisamala kuti ufulu wanu wosankhawo usakhale chopunthwitsa kwa anthu ofooka.+ 10  Ngati wina angaone iweyo wodziwa zinthuwe ukudya chakudya mʼkachisi wa mafano, kodi chikumbumtima cha munthu wofookayo sichidzamulimbikitsa kudya zakudya zoperekedwa kwa mafano? 11  Choncho kudziwa zinthu kwako kungachititse kuti uwononge munthu wofookayo, yemwe ndi mʼbale wako amene Khristu anamufera.+ 12  Koma inu mukamalakwira abale anu chonchi nʼkumavulaza chikumbumtima chawo chofookacho,+ mukuchimwira Khristu. 13  Choncho ngati chakudya chikukhumudwitsa mʼbale wanga, sindidzadyanso nyama ngakhale pangʼono, kuti ndisakhumudwitse mʼbale wanga.+

Mawu a M'munsi