Kalata Yoyamba Yopita kwa Atesalonika 1:1-10

  • Moni (1)

  • Kuthokoza chifukwa cha chikhulupiriro cha Atesalonika (2-10)

1  Ine Paulo ndili limodzi ndi Silivano*+ komanso Timoteyo+ ndipo ndikulembera mpingo wa Atesalonika, womwe ndi wogwirizana ndi Mulungu Atate komanso Ambuye Yesu Khristu kuti: Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zikhale nanu.  Nthawi zonse timathokoza Mulungu tikamakutchulani nonsenu mʼmapemphero athu.+  Timachita zimenezi chifukwa nthawi zonse timakumbukira ntchito zanu zachikhulupiriro, ntchito zanu zachikondi komanso kupirira kwanu chifukwa cha chiyembekezo chimene muli nacho+ mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu amene ndi Atate wathu.  Chifukwa tikudziwa, inu abale okondedwa ndi Mulungu, kuti iye ndi amene anakusankhani.  Tikutero chifukwa pamene tinkalalikira uthenga wabwino kwa inu, sitinkangolankhula basi, koma uthengawo unali wamphamvu, unabwera ndi mzimu woyera komanso tinalalikira motsimikiza mtima kwambiri. Inunso mukudziwa zimene tinakuchitirani pofuna kukuthandizani.  Munalandira mawuwo ndi chimwemwe chimene mzimu woyera+ umapereka ngakhale kuti munali pamavuto aakulu. Pamenepa munatsanzira ifeyo+ komanso munatsanzira Ambuye,+  moti munakhala chitsanzo kwa okhulupirira onse ku Makedoniya ndi ku Akaya.  Sikuti mawu a Yehova* ochokera kwa inu amveka ku Makedoniya ndi ku Akaya kokha, koma kwina kulikonse chikhulupiriro chanu mwa Mulungu chafalikira,+ moti ife sitikufunika kunenapo kanthu.  Chifukwa iwo akunenabe za mmene ife tinakumanirana ndi inu koyamba komanso mmene inu munasiyira mafano anu nʼkutembenukira kwa Mulungu,+ kuti muzitumikira Mulungu wamoyo ndi woona. 10  Munatembenukiranso kwa Mulungu kuti muziyembekezera Mwana wake kuchokera kumwamba,+ amene anamuukitsa kwa akufa. Mwanayo ndi Yesu, amene akutipulumutsa ku mkwiyo umene ukubwerawo.+

Mawu a M'munsi

Amene ankadziwikanso kuti Sila.