Kalata Yoyamba Yopita kwa Atesalonika 3:1-13

  • Paulo anapitiriza kukhala ku Atene podikira lipoti lochokera ku Tesalonika (1-5)

  • Timoteyo anabweretsa lipoti lolimbikitsa (6-10)

  • Anapempherera Atesalonika (11-13)

3  Choncho pamene sitinathenso kupirira, tinaona kuti ndi bwino kuti tipitirize kukhala ku Atene.+  Ndiye tinatumiza Timoteyo+ mʼbale wathu, yemwe ndi mtumiki wa Mulungu* amene akulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu. Tinamutumiza kuti adzakulimbikitseni ndi kukutonthozani nʼcholinga choti chikhulupiriro chanu chikhale cholimba.  Tinachita zimenezi kuti pasapezeke aliyense amene chikhulupiriro chake chafooka* ndi masautso amenewa. Chifukwa inunso mukudziwa kuti sitingapewe kukumana ndi mavuto ngati amenewa.*+  Chifukwa pamene tinali nanu limodzi, tinkakuuziranitu kuti tidzakumana ndi mavuto ndipo monga mmene mukudziwira, zimene tinkakuuzanizo ndi zimene zachitikadi.+  Nʼchifukwa chake pamene sindinathenso kupirira, ndinatuma Timoteyo kwa inu kuti ndidziwe za kukhulupirika kwanu.+ Ndimadera nkhawa kuti mwina Woyesayo+ anakuyesani ndipo nʼkutheka kuti ntchito imene tinagwira mwakhama inangopita pachabe.  Koma Timoteyo wangofika kumene kuno kuchokera kumeneko+ ndipo watiuza nkhani yabwino yokhudza kukhulupirika kwanu ndi chikondi chanu. Watiuza kuti mukupitiriza kutikumbukira ndipo mumatikonda komanso kuti mukulakalaka kutiona ngati mmene ifenso tikulakalakira kukuonani.  Nʼchifukwa chake abale, mʼmavuto athu onse* komanso mʼmasautso athu onse tatonthozedwa chifukwa cha inu komanso chifukwa cha kukhulupirika kumene mukusonyeza.+  Chifukwa ife timapeza mphamvu* inu mukakhala olimba mwa Ambuye.  Kodi Mulungu tingamuthokoze bwanji kuti timubwezere chifukwa cha chimwemwe chachikulu chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu chifukwa cha inu? 10  Usiku ndi masana timapemphera mopembedzera kuchokera pansi pamtima kuti tidzakuoneni pamasomʼpamaso* nʼkukupatsani zimene zikufunika kuti chikhulupiriro chanu chikhale cholimba.+ 11  Tsopano Mulungu amenenso ndi Atate wathu komanso Ambuye wathu Yesu, atithandize kuti zitheke kubwera kwa inu. 12  Komanso, Ambuye akuthandizeni kuti muzikondana kwambiri ndiponso kuti muzikonda anthu ena+ ngati mmene ife timakukonderani. 13  Achite zimenezi kuti alimbitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera pamaso pa Mulungu+ amene ndi Atate wathu, pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu,+ limodzi ndi oyera ake onse.

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “yemwe ndi wantchito mnzake wa Mulungu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene wasochera.”
Kapena kuti, “mukudziwa kuti tikuyenera kukumana ndi zimenezi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pa zosowa zathu zonse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “timakhala ndi moyo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti tidzaone nkhope zanu.”