1 Mafumu 13:1-34

  • Ulosi wonena za guwa la ku Beteli (1-10)

    • Guwa linagumuka (5)

  • Munthu wa Mulungu sanamvere (11-34)

13  Panali munthu wa Mulungu+ amene anatumidwa ndi Yehova kuchokera ku Yuda kupita ku Beteli. Kumeneko iye anapeza Yerobowamu ataimirira pambali pa guwa lansembe+ kuti apereke nsembe yautsi.  Ndiyeno anafuula mawu ochokera kwa Yehova otemberera guwalo, kuti: “Guwa lansembe iwe! Guwa lansembe iwe! Yehova wanena kuti, ‘Mwana wamwamuna adzabadwa mʼnyumba ya Davide, dzina lake Yosiya.+ Iye adzatenga ansembe a malo okwezeka amene akupereka nsembe yautsi pa iwe nʼkuwapereka nsembe pa iwe. Ndipo adzawotcha mafupa a anthu pa iwe.’”+  Kenako munthu wa Mulunguyo anapereka chizindikiro. Iye anati: “Chizindikiro chimene Yehova wapereka ndi ichi: Guwa lansembeli lingʼambika pakati ndipo phulusa* limene lili paguwali litayika.”  Mfumu Yerobowamu atangomva mawu otemberera guwa lansembe la ku Beteli amene munthu wa Mulunguyo ananena, anasiya zimene ankachita paguwa lansembe nʼkumuloza ndipo ananena kuti: “Mʼgwireni uyu!”+ Nthawi yomweyo, dzanja limene analozera munthu wa Mulunguyo linauma ndipo sanathe kulibweza.+  Kenako guwa lansembelo linangʼambika ndipo phulusa linatayika mogwirizana ndi chizindikiro chimene munthu wa Mulungu woonayo anapereka, malinga ndi mawu a Yehova.  Mfumuyo inauza munthu wa Mulungu woonayo kuti: “Chonde, pemphani Yehova Mulungu wanu kuti andichitire chifundo ndipo mundipempherere kuti dzanja langa libwerere mwakale.”+ Choncho munthu wa Mulungu woonayo anapempha Yehova kuti achitire chifundo mfumuyo, moti dzanjalo linabwerera mwakale.  Kenako mfumuyo inauza munthuyo kuti: “Tiyeni kunyumba mukadye chakudya komanso ndikakupatseni mphatso.”  Koma munthu wa Mulungu woonayo anayankha mfumuyo kuti: “Ngakhale mutandipatsa hafu ya nyumba yanu sindingapite nanu ndipo sindingadye chakudya kapena kumwa madzi kuno.  Chifukwa Yehova anandilamula kuti: ‘Usakadye chakudya kapena kumwa madzi ndipo pobwerera usakadzere njira imene udutse popita.’” 10  Choncho iye ananyamuka nʼkudutsa njira ina. Sanadutse njira imene anadzera popita ku Beteliko. 11  Ndiyeno panali mneneri wina wokalamba yemwe ankakhala ku Beteli. Ana ake anabwera nʼkumufotokozera zonse zimene munthu wa Mulungu woona uja anachita ku Beteli komanso zomwe anauza mfumu. Atamufotokozera zimenezi, 12  bamboyo anafunsa anawo kuti: “Munthuyo wadzera njira iti?” Anawo analozera bamboyo njira imene munthu wa Mulungu woona wochokera ku Yuda uja anadzera. 13  Kenako bamboyo anauza anawo kuti: “Ndimangireni chishalo pabulu.” Anawo anamangiradi bambo awowo chishalo ndipo iwo anakwera buluyo. 14  Atatero, anatsatira munthu wa Mulungu woona uja ndipo anamʼpeza atakhala pansi pa mtengo waukulu. Ndiyeno anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe munthu wa Mulungu woona amene wachokera ku Yuda?”+ Munthuyo anayankha kuti: “Inde, ndi ineyo.” 15  Kenako anamuuza kuti: “Tiye kunyumba ukadye chakudya.” 16  Koma munthuyo anati: “Sindingabwerere nanu kapena kuchita zomwe mwandiuzazi ndipo sindingadye nanu chakudya kapena kumwa madzi kuno. 17  Chifukwa Yehova anandiuza kuti, ‘Usakadye chakudya kapena kumwa madzi kumeneko ndipo pobwerera usakadzere njira imene udutse popita.’” 18  Mneneri wokalambayo atamva zimenezi anati: “Inenso ndine mneneri ngati iweyo. Mngelo wandiuza mawu ochokera kwa Yehova akuti, ‘Kamʼbweze upite naye kunyumba kwako kuti akadye chakudya ndi kumwa madzi.’” (Anamunamiza.) 19  Choncho anabwerera naye kuti akadye chakudya ndi kumwa madzi kunyumba kwake. 20  Akudya patebulo, mawu a Yehova anafika kwa mneneri yemwe anabweza munthu wa ku Yuda uja. 21  Ndiyeno anauza munthu wa Mulungu woona wochokera ku Yuda uja kuti: “Yehova wanena kuti: ‘Chifukwa chakuti sunamvere zimene Yehova anakulamula ndipo sunatsatire lamulo limene Yehova Mulungu wako anakupatsa, 22  koma wabwerera kuti udye chakudya ndi kumwa madzi kumalo amene iye anakuuza kuti: “Usakadye chakudya kapena kumwa madzi,” mtembo wako sudzaikidwa mʼmanda a makolo ako.’”+ 23  Munthu wa Mulungu woona uja atamaliza kudya ndi kumwa, mneneri wokalambayo anamanga chishalo pabulu kuti mneneri wa ku Yuda, yemwe anamʼbwezayo akwerepo. 24  Kenako mneneri wa ku Yudayo ananyamuka nʼkumapita. Koma mkango unamupeza panjira nʼkumupha,+ ndipo mtembo wake unali pamsewu. Bulu ndi mkangowo zinaima pambali pa mtembowo. 25  Anthu ena amene ankadutsa, anaona mtembowo uli pamsewupo, mkango utaima pambali pake. Anthuwo atafika mumzinda womwe mneneri wokalamba uja ankakhala, anafotokoza zomwe anaonazo. 26  Mneneri amene anakabweza munthu uja atamva nkhaniyi, nthawi yomweyo anati: “Ndi munthu wa Mulungu woona amene sanamvere lamulo la Yehova uja.+ Choncho Yehova wamupereka kwa mkango kuti umugwire nʼkumupha, mogwirizana ndi mawu amene Yehova anamuuza.”+ 27  Ndiyeno anauza ana ake kuti: “Ndimangireni chishalo pabulu.” Ndipo anamʼmangiradi. 28  Mneneri wokalambayo ananyamuka nʼkukapeza mtembo wa munthu uja uli pamsewu, bulu ndi mkango zitaima pambali pake. Mkangowo sunadye mtembowo kapena kupha buluyo. 29  Ndiyeno mneneriyo ananyamula mtembo wa munthu wa Mulungu woonayo nʼkuukweza pabulu ndipo anabwerera nawo mumzinda wa mneneri wokalambayo kuti akamulire ndi kumuika mʼmanda. 30  Mneneri wokalambayo anakaika mtembowo mʼmanda ake. Ndipo anthu ankamulira kuti: “Mayo ine, mʼbale wanga!” 31  Atamuika mʼmanda, mneneri wokalambayo anauza ana ake kuti: “Ndikadzamwalira mudzandiike mʼmanda amene taika munthu wa Mulungu woonayu. Mudzaike mafupa anga pambali pa mafupa ake.+ 32  Mawu a Yehova amene munthu wa Mulunguyu ananena otemberera guwa lansembe limene lili ku Beteli ndiponso akachisi onse amʼmalo okwezeka+ amene ali mʼmizinda ya ku Samariya, adzakwaniritsidwa ndithu.”+ 33  Ngakhale kuti zimenezi zinachitika, Yerobowamu sanasiye kuchita zoipa. Iye anapitiriza kuika anthu wamba kuti akhale ansembe a malo okwezeka.+ Aliyense wofuna unsembewo, iye ankamʼpatsa ponena kuti: “Uyu akhale wansembe wa malo okwezeka.”+ 34  Tchimo la nyumba ya Yerobowamuli,+ linachititsa kuti anthu onse amʼnyumba yake awonongedwe nʼkufafanizidwa padziko lapansi.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “phulusa losakanikirana ndi mafuta a nsembe.”