1 Mafumu 14:1-31

  • Ulosi wa Ahiya wotsutsa Yerobowamu (1-20)

  • Rehobowamu anayamba kulamulira ku Yuda (21-31)

    • Sisaki anaukira Yerusalemu (25, 26)

14  Pa nthawiyo, Abiya mwana wamwamuna wa Yerobowamu anadwala.  Choncho Yerobowamu anauza mkazi wake kuti: “Nyamuka upite ku Silo ndipo udzisinthe kuti anthu asadziwe kuti ndiwe mkazi wa Yerobowamu. Mneneri Ahiya ali kumeneko. Iye ndi amene anandiuza kuti ndidzakhala mfumu ya anthuwa.+  Utenge mikate 10, makeke ndi botolo la uchi, upite kwa iyeyo ndipo akakuuza zimene zichitikire mnyamatayu.”  Mkazi wa Yerobowamu anachitadi zimenezo. Ananyamuka kupita ku Silo+ nʼkukafika kunyumba kwa Ahiya. Ahiyayo sankatha kuona chifukwa maso ake anali atachita khungu ndi ukalamba.  Koma Yehova anali atauza Ahiya kuti: “Kukubwera mkazi wa Yerobowamu kudzakufunsa za mwana wake chifukwa mwanayo akudwala. Ndikuuza zoti umuuze.* Akafika adzisintha kuti asadziwike.”  Ahiya atangomva phokoso la mapazi a mkazi wa Yerobowamu pamene ankafika pakhomo anati: “Lowa mkazi wa Yerobowamu. Nʼchifukwa chiyani ukudzisintha kuti usadziwike? Ine ndatumidwa kuti ndikuuze uthenga wopweteka.  Pita ukauze Yerobowamu kuti, ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ine ndinakukweza pakati pa anthu a mtundu wako kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli.+  Kenako ndinangʼamba ufumu kuuchotsa kunyumba ya Davide nʼkukupatsa.+ Koma iwe sunakhale ngati Davide mtumiki wanga amene anasunga malamulo anga, kunditsatira ndi mtima wake wonse ndiponso kuchita zinthu zoyenera zokhazokha pamaso panga.+  Koma wachita zinthu zoipa kwambiri kuposa onse amene anakhalapo iwe usanakhale. Unadzipangiranso mulungu wina komanso zifaniziro zachitsulo kuti undikwiyitse+ ndipo wandisiya.+ 10  Pa chifukwa chimenechi, ndikubweretsa tsoka panyumba ya Yerobowamu ndipo ndidzapha mwamuna* aliyense wamʼnyumba ya Yerobowamu, ngakhale ooneka onyozeka ndi ofooka mu Isiraeli. Komanso ndidzaseseratu nyumba ya Yerobowamu+ ngati mmene munthu amasesera ndowe mpaka zonse zitachoka. 11  Munthu wa mʼbanja la Yerobowamu wofera mumzinda, agalu adzamudya ndipo wofera kutchire, mbalame zidzamudya chifukwa Yehova wanena zimenezi.”’ 12  Iweyo nyamuka, uzipita kunyumba kwanu ndipo mapazi ako akakangoponda mumzinda, mwanayo akamwalira. 13  Aisiraeli onse akamulira nʼkumuika mʼmanda ndipo mʼbanja lonse la Yerobowamu, uyu yekha ndi amene adzaikidwe mʼmanda chifukwa mʼnyumba yonse ya Yerobowamu, Yehova Mulungu wa Isiraeli wapeza chinachake chabwino mwa yekhayu. 14  Yehova adzaika yekha mfumu ina yolamulira Isiraeli, yomwe idzafafanize nyumba ya Yerobowamu+ kuyambira tsiku limenelo, ndipo akhoza kuchitanso zimenezi pompano. 15  Yehova adzawononga Isiraeli ngati bango limene likugwedezeka mʼmadzi ndipo adzazula Aisiraeli mʼdziko labwinoli limene anapatsa makolo awo.+ Ndiyeno adzawabalalitsira kutsidya lina la Mtsinje,*+ chifukwa anapanga mizati* yawo yopatulika+ nʼkukwiyitsa Yehova. 16  Iye adzasiya Aisiraeli chifukwa cha machimo amene Yerobowamu anachita ndiponso amene Aisiraeli anachita chifukwa cha iyeyo.”+ 17  Atamva zimenezi, mkazi wa Yerobowamu ananyamuka nʼkumapita ndipo anafika ku Tiriza. Atangofika pakhomo la nyumba yawo, mnyamatayo anamwalira. 18  Choncho anamuika mʼmanda ndipo Aisiraeli onse anamulira, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena kudzera mwa mtumiki wake, mneneri Ahiya. 19  Nkhani zina zokhudza Yerobowamu, mmene anamenyera nkhondo+ ndiponso ulamuliro wake, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 20  Yerobowamu analamulira zaka 22, kenako mofanana ndi makolo ake anamwalira.+ Ndiyeno mwana wake, dzina lake Nadabu, anayamba kulamulira mʼmalo mwake.+ 21  Pa nthawiyi, Rehobowamu mwana wa Solomo anali mfumu ku Yuda. Rehobowamu anali ndi zaka 41 pamene ankayamba kulamulira, ndipo analamulira kwa zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Yehova anasankha+ pa mafuko onse a Isiraeli kuti aikeko dzina lake.+ Mayi ake anali Naama, mbadwa ya Amoni.+ 22  Ayuda ankachita zoipa pamaso pa Yehova+ ndipo anamukwiyitsa kwambiri ndi machimo awo kuposa mmene makolo awo anachitira.+ 23  Nawonso anapitiriza kumanga malo okwezeka, zipilala zopatulika ndi mizati yopatulika*+ pamwamba pa phiri lililonse lalitali+ ndiponso pansi pa mtengo uliwonse waukulu wamasamba obiriwira.+ 24  Mʼdzikomo munkapezekanso mahule aamuna apakachisi.+ Anthuwo anachita zinthu zonse zonyansa zimene ankachita anthu a mitundu imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa Aisiraeli. 25  Mʼchaka cha 5 cha Mfumu Rehobowamu, Sisaki mfumu ya Iguputo+ anaukira Yerusalemu.+ 26  Iye anatenga chuma chamʼnyumba ya Yehova ndi chuma chamʼnyumba ya mfumu.+ Anatenga chilichonse kuphatikizapo zishango zonse zagolide zimene Solomo anapanga.+ 27  Choncho Mfumu Rehobowamu anapanga zishango zakopa* mʼmalomwake ndipo anazipereka kwa akulu a asilikali* olondera pakhomo la nyumba ya mfumu kuti aziziyangʼanira. 28  Nthawi iliyonse imene mfumuyo ikupita kunyumba ya Yehova, asilikaliwo ankanyamula zishangozo ndipo kenako ankazibwezera kuchipinda cha alonda. 29  Nkhani zina zokhudza Rehobowamu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda.+ 30  Pakati pa Rehobowamu ndi Yerobowamu pankachitika nkhondo nthawi zonse.+ 31  Kenako Rehobowamu, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake mu Mzinda wa Davide.+ Mayi ake anali Naama ndipo anali a Chiamoni.+ Kenako Abiyamu*+ mwana wa Rehobowamu anayamba kulamulira mʼmalo mwake.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Umuuze zakutizakuti.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “aliyense wokodzera khoma.” Amenewa ndi mawu onyoza a Chiheberi otanthauza mwamuna.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Kapena kuti, “zamkuwa.”
Kapena kuti, “asilikali othamanga.”
Ankadziwikanso kuti Abiya.