1 Mafumu 15:1-34

  • Abiyamu, mfumu ya Yuda (1-8)

  • Asa, mfumu ya Yuda (9-24)

  • Nadabu, mfumu ya Isiraeli (25-32)

  • Basa, mfumu ya Isiraeli (33, 34)

15  Mʼchaka cha 18 cha Mfumu Yerobowamu+ mwana wa Nebati, Abiyamu anakhala mfumu ya Yuda.+  Iye analamulira zaka zitatu ku Yerusalemu. Mayi ake anali Maaka,+ mdzukulu wa Abishalomu.  Abiyamu anapitiriza kuchita machimo onse amene bambo ake anachita. Sanatumikire Yehova Mulungu wake ndi mtima wonse ngati mmene anachitira Davide kholo lake.  Komabe, chifukwa cha kukhulupirika kwa Davide,+ Yehova Mulungu wake anamʼpatsa nyale mu Yerusalemu+ pokweza mwana wake pambuyo pake ndiponso pochititsa kuti Yerusalemu akhalepobe.  Anatero popeza Davide anachita zoyenera pamaso pa Yehova, ndipo anatsatira chilichonse chimene Mulungu anamulamula masiku onse a moyo wake, kupatulapo pa nkhani ya Uriya Muhiti.+  Masiku onse a Rehobowamu, pankachitika nkhondo pakati pa iyeyo ndi Yerobowamu.+  Nkhani zina zokhudza Abiyamu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda.+ Pakati pa Abiyamu ndi Yerobowamu, panachitikanso nkhondo.+  Kenako Abiyamu, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide. Ndiyeno mwana wake Asa+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.+  Mʼchaka cha 20 cha Yerobowamu mfumu ya Isiraeli, Asa anayamba kulamulira ku Yuda. 10  Analamulira ku Yerusalemu zaka 41. Agogo ake aakazi dzina lawo linali Maaka,+ mdzukulu wa Abishalomu. 11  Asa anachita zabwino pamaso pa Yehova+ ngati mmene anachitira Davide kholo lake. 12  Iye anachotsa mahule aamuna apakachisi mʼdzikolo+ komanso mafano onse onyansa* amene makolo ake anapanga.+ 13  Anachotsa ngakhalenso agogo ake aakazi a Maaka+ pa udindo wawo wokhala mayi wa mfumu, chifukwa anapanga fano lonyansa kwambiri lolambirira mzati wopatulika.* Asa anagwetsa fanolo+ nʼkukalitentha mʼchigwa cha Kidironi.+ 14  Koma sanachotse malo okwezeka.+ Ngakhale zinali choncho, Asa anatumikira Yehova ndi mtima wonse kwa moyo wake wonse. 15  Iye anabweretsa kunyumba ya Yehova zinthu zimene bambo ake komanso iyeyo anaziyeretsa. Zinthuzo zinali siliva, golide ndiponso ziwiya zina zosiyanasiyana.+ 16  Pakati pa Asa ndi Basa+ mfumu ya Isiraeli pankachitika nkhondo. 17  Choncho Basa mfumu ya Isiraeli anapita kukaukira Yuda ndipo anayamba kumanganso mzinda wa Rama+ kuti ukhale wolimba. Anachita zimenezi kuti anthu asamalowe kapena kutuluka mʼdera la Asa mfumu ya Yuda.+ 18  Zitatero, Asa anatenga siliva ndi golide yense amene anatsala pa chuma chamʼnyumba ya Yehova ndi pa chuma chamʼnyumba ya mfumu nʼkumupereka kwa atumiki ake. Kenako Mfumu Asa anatumiza atumiki akewo kwa Beni-hadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Hezioni, mfumu ya Siriya,+ amene ankakhala ku Damasiko. Anawatuma kuti akamuuze Beni-hadadi kuti: 19  “Pali pangano pakati pa ine ndi iwe ndiponso pakati pa bambo anga ndi bambo ako. Ndakutumizira mphatso ya siliva ndi golide. Bwera udzaphwanye pangano lako ndi Basa mfumu ya Isiraeli kuti achoke mʼdera langa.” 20  Beni-hadadi anamvera Mfumu Asa ndipo anatumiza akuluakulu a asilikali ake kuti akamenyane ndi anthu amʼmizinda ya Isiraeli. Iwo analanda Iyoni,+ Dani,+ Abele-beti-maaka ndi Kinereti yense komanso dera lonse la Nafitali. 21  Basa atamva zimenezi, nthawi yomweyo anasiya kumanga Rama* ndipo anapitiriza kukhala ku Tiriza.+ 22  Ndiyeno Mfumu Asa inaitanitsa Ayuda onse moti palibe amene anatsala, ndipo iwo anatenga miyala ndi matabwa za ku Rama zimene Basa ankamangira. Mfumu Asa anatenga zinthu zimenezi nʼkukamangira mzinda wa Geba+ ku Benjamini ndi wa Mizipa+ kuti mizindayi ikhale yolimba. 23  Nkhani zina zonse zokhudza Asa, mphamvu zake, mizinda imene anamanga* ndiponso zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda. Koma atakalamba anadwala matenda akumapazi.+ 24  Kenako Asa, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake mu Mzinda wa Davide kholo lake. Ndiyeno mwana wake Yehosafati+ anakhala mfumu mʼmalo mwake. 25  Nadabu+ mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Isiraeli mʼchaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, ndipo analamulira Isiraeli zaka ziwiri. 26  Iye ankachita zoipa pamaso pa Yehova, ndipo anatsatira njira ya bambo ake+ komanso machimo amene Aisiraeli anachita chifukwa cha bambo akewo.+ 27  Ndiyeno Basa mwana wa Ahiya wa nyumba ya Isakara, anakonzera chiwembu Nadabu ndipo anamupha mumzinda wa Gibitoni,+ womwe unali mʼmanja mwa Afilisiti. Anamupha pa nthawi imene Nadabuyo ndi Aisiraeli onse ankaukira Gibitoni. 28  Basa anapha Nadabu mʼchaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda ndipo anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 29  Basa atangokhala mfumu, anapha anthu onse a mʼnyumba ya Yerobowamu. Sanasiye munthu aliyense wa mʼbanja la Yerobowamu ali ndi moyo. Anapha onse mogwirizana ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa mtumiki wake Ahiya wa ku Silo.+ 30  Izi zinachitika chifukwa cha machimo amene Yerobowamu anachita, machimo amene Aisiraeli anachita chifukwa cha iye komanso chifukwa choti Yerobowamuyo anakwiyitsa kwambiri Yehova Mulungu wa Isiraeli. 31  Nkhani zina zokhudza Nadabu ndi zonse zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 32  Pakati pa Asa ndi Basa mfumu ya Isiraeli pankachitika nkhondo.+ 33  Mʼchaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, Basa mwana wa Ahiya anakhala mfumu ya Isiraeli yense ku Tiriza ndipo analamulira kwa zaka 24.+ 34  Koma iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ ndipo ankayenda mʼnjira ya Yerobowamu ndiponso mʼmachimo amene Aisiraeli anachita chifukwa cha Yerobowamuyo.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake a Chiheberi amatanthauzanso “ndowe,” ndipo amagwiritsidwa ntchito ngati mawu onyoza.
Kapena kuti, “kumanganso mzinda wa Rama kuti ukhale wolimba.”
Kapena kuti, “imene anaimanganso kuti ikhale yolimba.”