1 Mafumu 19:1-21

  • Eliya anathawa Yezebeli (1-8)

  • Yehova anaonekera kwa Eliya ku Horebe (9-14)

  • Eliya anadzoza Hazaeli, Yehu ndi Elisa (15-18)

  • Elisa anadzozedwa kuti alowe mʼmalo mwa Eliya (19-21)

19  Kenako Ahabu+ anauza Yezebeli+ zonse zimene Eliya anachita ndiponso mmene anaphera aneneri onse ndi lupanga.+  Yezebeli atamva zimenezo, anatuma munthu kwa Eliya kukamuuza kuti: “Milungu yanga indilange mowirikiza, ngati pofika nthawi ino mawa sindidzakhala nditakupha ngati mmene waphera aneneriwo.”  Choncho Eliya anachita mantha moti ananyamuka nʼkuyamba kuthawa kuti apulumutse moyo wake.+ Atafika ku Beere-seba+ wa ku Yuda,+ anasiya mtumiki wake kumeneko.  Ndipo iyeyo analowa mʼchipululu nʼkuyenda ulendo wa tsiku limodzi. Kenako anafika pa kamtengo kenakake nʼkukhala pansi pake. Ndiyeno anapempha kuti afe ponena kuti: “Basi ndatopa nazo. Tsopano chotsani moyo wanga Yehova,+ chifukwa siine woposa makolo anga.”  Kenako anagona pansi pa kamtengo kaja mpaka tulo tinamʼpeza. Mwadzidzidzi kunabwera mngelo ndipo anamukhudza+ nʼkumuuza kuti: “Dzuka udye.”+  Atayangʼana, anaona kuti kumutu kwake kuli mkate wozungulira pamiyala yotentha komanso jagi* ya madzi. Eliya anadya nʼkumwa ndipo anagonanso.  Patapita kanthawi, mngelo wa Yehova uja anabweranso nʼkumukhudza ndipo anamuuza kuti: “Dzuka udye, popeza ulendowu ukhala wautali.”  Choncho anadzuka ndipo anadya ndi kumwa. Atatero, anapeza mphamvu zokwanira moti anayenda masiku 40, masana ndi usiku, mpaka anakafika kuphiri la Mulungu woona la Horebe.+  Atafika kumeneko, analowa mʼphanga+ nʼkugona mmenemo usiku wonse. Kenako anamva mawu a Yehova akufunsa kuti: “Ukudzatani kuno Eliya?” 10  Iye anayankha kuti: “Ine ndakutumikirani modzipereka kwambiri inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba,+ koma Aisiraeli asiya pangano lanu.+ Agwetsa maguwa anu ansembe ndipo apha aneneri anu ndi lupanga,+ moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti andiphe.”+ 11  Koma Mulungu anati: “Tuluka, kaime paphiri pamaso pa Yehova.” Kenako Yehova anadutsa,+ ndipo kunawomba chimphepo champhamvu chomwe chinkangʼamba mapiri ndi kuphwanya matanthwe pamaso pa Yehova+ koma Yehova sanali mumphepoyo. Mphepoyo itatha kunachita chivomerezi,+ koma Yehova sanali mʼchivomerezicho. 12  Chivomerezicho chitatha kunabuka moto,+ koma Yehova sanali mʼmotowo. Motowo utatha, panamveka mawu achifatse apansipansi.+ 13  Eliya atangomva mawuwo, anaphimba nkhope yake ndi chovala chake+ ndipo anatuluka nʼkukaima pakhomo la phangalo. Kenako anamva mawu akuti: “Ukudzatani kuno Eliya?” 14  Iye anayankha kuti: “Ine ndakutumikirani modzipereka kwambiri inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, koma Aisiraeli asiya pangano lanu.+ Agwetsa maguwa anu ansembe ndipo apha aneneri anu ndi lupanga, moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti andiphe.”+ 15  Kenako Yehova anamuuza kuti: “Bwerera ndipo upite kuchipululu cha Damasiko. Ukakafika ukadzoze Hazaeli+ kuti akhale mfumu ya Siriya. 16  Ukadzozenso Yehu+ mdzukulu wa Nimusi kuti akhale mfumu ya Isiraeli ndipo Elisa,* mwana wa Safati wa ku Abele-mehola, ukamudzoze kuti adzakhale mneneri mʼmalo mwako.+ 17  Aliyense wothawa lupanga la Hazaeli,+ adzaphedwa ndi Yehu+ ndipo wothawa lupanga la Yehu, adzaphedwa ndi Elisa.+ 18  Ine ndasiya anthu 7,000 mu Isiraeli,+ amene mawondo awo sanagwadirepo Baala+ ndipo pakamwa pawo sipanakisepo Baala.”+ 19  Choncho Eliya anachoka kumeneko nʼkupita kwa Elisa mwana wa Safati, ndipo anamʼpeza akulima ndi pulawo yokokedwa ndi ngʼombe ziwiri zamphongo. Panali mapulawo 12 ndipo pulawo yake inali kumbuyo. Choncho Eliya anapita pamene panali Elisa nʼkumuponyera chovala chake chauneneri.+ 20  Zitatero, Elisa anasiya ngʼombe zamphongozo nʼkuthamangira Eliya ndipo anamuuza kuti: “Ndiloleni ndipite ndikakise kaye bambo anga ndi mayi anga, kenako ndidzakutsatirani.” Eliya anamuyankha kuti: “Pita, sindingakuletse.” 21  Choncho anabwerera nʼkutenga ngʼombe zamphongo ziwiri zija nʼkuzipha.* Anatenga mitengo ya pulawoyo nʼkuphikira nyama ya ngʼombezo. Kenako anapatsa anthu kuti adye. Atatero, iye ananyamuka nʼkutsatira Eliya ndipo anayamba kumʼtumikira.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “chikho.”
Kutanthauza “Mulungu Ndi Chipulumutso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkuzipereka nsembe.”