1 Mafumu 22:1-53

  • Yehosafati anachita mgwirizano ndi Ahabu (1-12)

  • Mikaya analosera kuti Ahabu agonjetsedwa (13-28)

    • Mzimu wabodza unapusitsa Ahabu (21, 22)

  • Ahabu anaphedwa ku Ramoti-giliyadi (29-40)

  • Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda (41-50)

  • Ahaziya mfumu ya Isiraeli (51-53)

22  Kwa zaka zitatu, panalibe nkhondo pakati pa Siriya ndi Isiraeli.  Mʼchaka chachitatucho, Yehosafati+ mfumu ya Yuda anapita kwa mfumu ya Isiraeli.+  Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inafunsa atumiki ake kuti: “Kodi mukudziwa kuti mzinda wa Ramoti-giliyadi+ ndi wathu? Koma tikuzengereza kuulanda mʼmanja mwa mfumu ya Siriya.”  Kenako inafunsa Yehosafati kuti: “Kodi tipita limodzi kunkhondo ku Ramoti-giliyadi?” Yehosafati anayankha mfumu ya Isiraeliyo kuti: “Inu ndi ine ndife amodzi. Anthu anga ndi anthu anu ndi amodzi ndipo mahatchi anga nʼchimodzimodzi ndi mahatchi anu.”+  Koma Yehosafati anauza mfumu ya Isiraeli kuti: “Choyamba, mufunsire kaye+ kwa Yehova.”+  Choncho mfumu ya Isiraeli inasonkhanitsa aneneri. Analipo amuna pafupifupi 400 ndipo inawafunsa kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi, kapena ndisapite?” Iwo anayankha kuti: “Pitani ndipo Yehova akapereka mzindawo kwa inu mfumu.”  Kenako Yehosafati anati: “Kodi kuno kulibe mneneri wina wa Yehova? Ngati alipo, tiyeni tifunsirenso kwa Mulungu kudzera mwa iyeyo.”+  Mfumu ya Isiraeli inayankha Yehosafati kuti: “Patsala munthu mmodzi amene tingathe kufunsira kwa Yehova+ kudzera mwa iye, koma ndimadana naye kwambiri,+ chifukwa salosera zabwino zokhudza ine, koma zoipa zokhazokha.+ Dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imula.” Koma Yehosafati anati: “Mfumu siyenera kulankhula choncho.”  Choncho mfumu ya Isiraeli inaitana nduna yapanyumba ya mfumu nʼkuiuza kuti: “Kamutenge Mikaya mwana wa Imula, ndipo ubwere naye mwamsanga.”+ 10  Mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala pabwalo* lapageti lolowera mumzinda wa Samariya. Aliyense anakhala pampando wake wachifumu atavala zovala zachifumu ndipo aneneri onse ankalosera pamaso pawo.+ 11  Ndiyeno Zedekiya mwana wa Kenaana anapanga nyanga zachitsulo nʼkunena kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ndi nyanga izi mudzagunda Asiriya mpaka kuwapha onse.’” 12  Aneneri ena onse ankaloseranso zofanana ndi zimenezi. Ankanena kuti: “Pitani ku Ramoti-giliyadi ndipo mukapambana. Yehova akapereka mzindawo kwa inu mfumu.” 13  Munthu amene anatumidwa kukaitana Mikaya anauza Mikayayo kuti: “Aneneri onse alankhula zabwino kwa mfumu. Nawenso ukalankhule zabwino.”+ 14  Koma Mikaya anati: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, zimene Yehova angandiuze nʼzimene ndikanene.” 15  Kenako anafika kwa mfumu ndipo mfumuyo inamufunsa kuti: “Mikaya, kodi tipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi kapena tisapite?” Nthawi yomweyo Mikaya anayankha kuti: “Pitani mukapambana ndipo Yehova akapereka mzindawo kwa inu mfumu.” 16  Ndiyeno mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi ndikulumbiritse kangati kuti uzindiuza zoona zokhazokha mʼdzina la Yehova?” 17  Choncho Mikaya anati: “Ndikuona Aisiraeli onse atabalalika mʼmapiri+ ngati nkhosa zopanda mʼbusa. Ndipo Yehova anati: ‘Amenewa alibe mtsogoleri. Aliyense abwerere kunyumba kwake mwamtendere.’” 18  Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati kuti: “Paja ndinakuuzani kuti, ‘Sadzalosera zabwino za ine, koma zoipa.’”+ 19  Mikaya anati: “Choncho imvani mawu a Yehova: Ndinaona Yehova atakhala pampando wake wachifumu+ ndipo gulu lonse lakumwamba linaimirira kumanja ndi kumanzere kwake.+ 20  Ndiyeno Yehova anati, ‘Ndani akapusitse Ahabu, kuti apite ku Ramoti-giliyadi nʼkukafa?’ Choncho angelo osiyanasiyana ankanena maganizo awo, wina izi, wina izi. 21  Kenako mngelo*+ wina anabwera kudzaima pamaso pa Yehova nʼkunena kuti, ‘Ine ndikamʼpusitsa.’ Yehova anamufunsa kuti, ‘Ukamʼpusitsa bwanji?’ 22  Iye anayankha kuti, ‘Ndipita kukakhala mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri ake onse.’+ Ndiyeno Mulungu anati, ‘Ukamʼpusitsadi ndipo zikakuyendera bwino. Pita ukachite zimenezo.’ 23  Choncho Yehova waika mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri anu onsewa,+ koma Yehovayo wanena kuti inuyo muona tsoka.”+ 24  Zedekiya mwana wa Kenaana anapita pomwe panali Mikaya nʼkumumenya mbama ndipo ananena kuti: “Zingatheke bwanji kuti mzimu wa Yehova undidutse nʼkukalankhula ndi iwe?”+ 25  Mikaya anayankha kuti: “Udzadziwa zimenezo tsiku limene udzalowe mʼchipinda chamkati kukabisala.” 26  Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inati: “Mtengeni Mikaya mupite naye kwa Amoni mkulu wa mzinda ndi Yowasi mwana wa mfumu. 27  Mukawauze kuti, ‘Mfumu yanena kuti: “Mʼtsekereni munthu uyu.+ Muzimʼpatsa chakudya chochepa ndi madzi ochepa, mpaka nditabwerako mwamtendere.”’” 28  Koma Mikaya anati: “Mukakabwerakodi mwamtendere ndiye kuti Yehova sanalankhule nane.”+ Ananenanso kuti: “Anthu inu, mawu angawa muwakumbukire.” 29  Choncho mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda ananyamuka kupita ku Ramoti-giliyadi.+ 30  Mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati kuti: “Ine ndidzisintha kuti ndisadziwike ndipo ndimenya nawo nkhondo. Koma inuyo muvale zovala zanu zachifumu.” Choncho mfumu ya Isiraeli inadzisintha+ nʼkuyamba kumenya nawo nkhondo. 31  Mfumu ya Siriya inali italamula akuluakulu 32 oyangʼanira asilikali okwera magaleta kuti:+ “Musakamenyane ndi wina aliyense, wamngʼono kapena wamkulu, koma mfumu ya Isiraeli yokha basi.” 32  Akuluakulu oyangʼanira asilikali okwera magaleta aja atangomuona Yehosafati, anaganiza kuti: “Mfumu ya Isiraeli ija ndi imeneyi.” Choncho anatembenuka kuti amenyane naye ndipo Yehosafati anayamba kukuwa kuti anthu amuthandize. 33  Akuluakulu oyangʼanira asilikali okwera magaletawo atangozindikira kuti si mfumu ya Isiraeli, anasiya kumuthamangitsa nʼkubwerera. 34  Koma munthu wina anaponya muvi wake chiponyeponye ndipo unakabaya mfumu ya Isiraeli pamalo olumikizira a chovala chake chokhala ndi mamba achitsulo. Choncho mfumuyo inauza woyendetsa galeta lake kuti: “Bwera udzanditulutse mʼbwalo lankhondoli chifukwa ndavulala kwambiri.”+ 35  Nkhondoyo inafika poopsa tsiku limenelo ndipo mfumuyo anaiimiritsa mʼgaleta nʼkuitsamiritsa kugaletalo moyangʼanizana ndi Asiriya. Magazi ochokera pamene anaibaya paja ankayenderera mʼgaletamo ndipo kenako inafa madzulo.+ 36  Dzuwa litatsala pangʼono kulowa, mumsasamo analengeza kuti: “Aliyense azipita mumzinda wake ndi kudziko lake!”+ 37  Choncho mfumuyo inafa ndipo anaibweretsa ku Samariya nʼkuiika mʼmanda ku Samariyako. 38  Atayamba kutsuka galeta lankhondolo padziwe la ku Samariya, lomwe mahule ankasambapo, agalu anayamba kunyambita magazi a mfumuyo mogwirizana ndi mawu amene Yehova ananena.+ 39  Nkhani zina zokhudza Ahabu, zonse zimene anachita, nyumba yaminyanga ya njovu+ imene anamanga komanso mizinda yonse imene anamanga, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Isiraeli. 40  Choncho Ahabu, mofanana ndi makolo ake, anamwalira+ ndipo mwana wake Ahaziya+ anakhala mfumu mʼmalo mwake. 41  Yehosafati+ mwana wa Asa anakhala mfumu ya Yuda mʼchaka cha 4 cha Ahabu mfumu ya Isiraeli. 42  Yehosafati anali ndi zaka 35 pamene ankakhala mfumu ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 25. Mayi ake dzina lawo linali Azuba mwana wa Sili. 43  Yehosafati anapitiriza kuyenda mʼnjira zonse za Asa,+ bambo ake. Sanasiye kuyenda mʼnjirazo ndipo anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova.+ Koma sanachotse malo okwezeka ndipo anthu ankaperekabe nsembe zautsi komanso nsembe zina mʼmalo okwezekawo.+ 44  Yehosafati ankakhala mwamtendere ndi mfumu ya Isiraeli.+ 45  Nkhani zina zokhudza Yehosafati, mphamvu zake ndiponso mmene anamenyera nkhondo, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda. 46  Yehosafati anachotsanso mʼdzikolo mahule aamuna apakachisi+ amene anatsala pa nthawi ya Asa bambo ake.+ 47  Pa nthawiyo ku Edomu+ kunalibe mfumu. Nduna ndi imene inkalamulira ngati mfumu.+ 48  Yehosafati anapanga zombo* za ku Tarisi kuti zizipita ku Ofiri kukatenga golide.+ Koma sizinapite chifukwa zinasweka ku Ezioni-geberi.+ 49  Pa nthawi imeneyi mʼpamene Ahaziya mwana wa Ahabu anapempha Yehosafati kuti: “Bwanji antchito anga apite limodzi ndi antchito anu mʼzombozo?” Koma Yehosafati anakana. 50  Kenako Yehosafati, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake+ mu Mzinda wa Davide kholo lake. Ndiyeno mwana wake Yehoramu+ anakhala mfumu mʼmalo mwake. 51  Ahaziya+ mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya mʼchaka cha 17 cha Yehosafati mfumu ya Yuda ndipo analamulira Isiraeli zaka ziwiri. 52  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova ndipo anayenda mʼnjira ya bambo ake+ ndi mayi ake+ ndiponso mʼnjira ya Yerobowamu mwana wa Nebati, amene anachititsa kuti Aisiraeli achimwe.+ 53  Ahaziya anapitiriza kutumikira Baala+ komanso kumugwadira. Anapitiriza kukwiyitsa Yehova Mulungu wa Isiraeli+ ngati mmene anachitira bambo ake.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “popunthira mbewu.”
Kapena kuti, “mzimu.”