1 Mafumu 6:1-38

  • Solomo anamanga kachisi (1-38)

    • Chipinda chamkati (19-22)

    • Akerubi (23-28)

    • Zogoba, zitseko, bwalo lamkati (29-36)

    • Anamanga kachisi zaka pafupifupi 7 (37, 38)

6  Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova*+ mʼchaka cha 480 kuchokera pamene Aisiraeli anatuluka mʼdziko la Iguputo,+ mwezi wa Zivi*+ (womwe ndi mwezi wachiwiri). Ichi chinali chaka cha 4 kuchokera pamene Solomoyo anakhala mfumu ya Isiraeli.  Nyumba imene Mfumu Solomo inamangira Yehova, inali mikono* 60 mulitali, mikono 20 mulifupi ndiponso mikono 30 kupita mʼmwamba.+  Khonde+ lakutsogolo kwa kachisi* linali mikono 20 mulitali ndipo linkafanana ndi mulifupi mwa nyumbayo. Khondelo linali kutsogolo kwa nyumbayo ndipo linali mikono 10 mulifupi.  Mawindo a nyumbayo anali aakulu mkati, aangʼono kunja.+  Komanso anamanga zipinda kuzungulira khoma lonse la nyumbayo, kuzungulira makoma onse akunja a kachisi* ndi chipinda chamkati.+ Anamanganso zipinda zamʼmbali zosanjikizana kuzungulira nyumbayo.+  Chipinda chamʼmbali chapansi chinali mikono 5 mulifupi mwake, chapakati chinali mikono 6 mulifupi mwake ndipo chachitatu chinali mikono 7 mulifupi mwake. Makoma onse akunja a nyumbayo anangowagoba nʼcholinga choti asawaboole.+  Nyumbayo anaimanga ndi miyala yosema kale,+ ndipo phokoso la hamala, nkhwangwa kapena zida zilizonse zachitsulo silinkamveka pamene ankaimanga.  Khomo lolowera kuchipinda chamʼmbali chapansi linali kumʼmwera* kwa nyumbayo,+ ndipo ankakwera masitepe oyenda mokhotakhota kukafika kuchipinda chapakati, kenako kukafika kuchipinda chachitatu.  Anapitiriza kumanga nyumbayo mpaka kuimaliza.+ Denga la nyumbayo analipanga ndi matabwa komanso mitengo ya mkungudza.+ 10  Anamanga zipinda zamʼmbali zosanjikizana kuzungulira nyumbayo+ ndipo chipinda chilichonse chinali chachitali mikono 5. Zipindazo anazilumikiza kunyumbayo ndi matabwa a mkungudza. 11  Pa nthawiyo, Yehova anauza Solomo kuti: 12  “Ponena za nyumba ukumangayi, ukamatsatira malamulo anga ndiponso kusunga ziweruzo zanga zonse,+ inenso ndidzakwaniritsa zimene ndinalonjeza Davide bambo ako.+ 13  Komanso ndidzakhala pakati pa Aisiraeli+ ndipo sindidzasiya Aisiraeli, omwe ndi anthu anga.”+ 14  Solomo anapitiriza kumanga nyumbayo mpaka kuimaliza. 15  Makoma a mkati mwa nyumbayo anawamanga ndi matabwa akuluakulu a mkungudza. Mkati mwa nyumbayo, kuchokera pansi mpaka kudenga anakutamo ndi matabwa. Komanso pansi pa nyumbayo anaikapo matabwa akuluakulu a mitengo ya junipa.*+ 16  Anagawanso chipinda cha mikono 20 kumbuyo kwa nyumbayo pogwiritsa ntchito matabwa akuluakulu a mkungudza, kuchokera pansi mpaka kudenga. Ndipo mʼchipindamo anamangamo chipinda chamkati+ chotchedwa Malo Oyera Koposa.+ 17  Komanso kachisi,*+ yemwe anali mbali ya nyumbayi ndipo anali kutsogolo kwake, kutalika kwake kunali mikono 40. 18  Pamatabwa a mkungudza a mkati mwa nyumbayo anajambulapo mochita kugoba zokongoletsera zooneka ngati zipanda+ ndiponso maluwa.+ Mkati monse munali matabwa a mkungudza ndipo simunkaoneka mwala uliwonse. 19  Iye anakonza chipinda chamkati+ cha nyumbayo kuti aikemo likasa la pangano la Yehova.+ 20  Chipinda chamkaticho chinali mikono 20 mulitali, mikono 20 mulifupi ndi mikono 20 kupita mʼmwamba.+ Chipindachi anachikuta ndi golide woyenga bwino, komanso anakuta guwa lansembe+ ndi matabwa a mkungudza. 21  Solomo anakuta mkati mwa nyumba yonseyo ndi golide woyenga bwino.+ Kutsogolo kwa chipinda chamkati+ anaikako matcheni agolide ndipo anakuta chipindacho ndi golide. 22  Nyumba yonseyo anaikuta ndi golide mpaka kuimaliza, ndipo guwa lansembe lonse, lomwe linali pafupi ndi chipinda chamkati, analikuta ndi golide.+ 23  Mʼchipinda chamkati Solomo anapangamo akerubi awiri+ pogwiritsa ntchito mtengo wa paini.* Kerubi aliyense anali wamtali mikono 10.+ 24  Phiko limodzi la kerubi linali lalitali mikono 5 ndipo phiko lina, linalinso lalitali mikono 5. Kuchokera kunsonga kwa phiko kukafika kunsonga kwa phiko lina kutalika kwake kunali mikono 10. 25  Kerubi wachiwiri analinso wamtali mikono 10. Akerubiwa anali ofanana kukula kwake ndiponso kapangidwe kake. 26  Kerubi mmodzi anali wamtali mikono 10, chimodzimodzinso winayo. 27  Kenako akerubiwo+ anawaika mʼchipinda chamkati.* Mapiko awo anali otambasula moti phiko la kerubi mmodzi linagunda khoma ndipo phiko la kerubi wina linagundanso khoma lina. Mapiko awo anafika pakati pa nyumbayo, ndipo anagundana. 28  Solomo anakuta akerubiwo ndi golide. 29  Pamakoma onse a nyumbayo a zipinda zonse ziwiri, zomwe ndi Malo Oyera Koposa komanso Malo Oyera, anajambulapo mochita kugoba akerubi,+ mitengo ya kanjedza+ ndi maluwa.+ 30  Pansi pa zipinda ziwirizo anakutapo ndi golide. 31  Pakhomo la chipinda chamkati anaikapo zitseko za mtengo wa paini, zipilala zamʼmbali ndiponso mafelemu, ngati mbali ya 5. 32  Zitseko ziwirizo zinali zamatabwa a mtengo wa paini ndipo anajambulapo mochita kugoba akerubi, mitengo ya kanjedza ndi maluwa. Zitsekozo anazikuta ndi golide. Akerubi ndi mitengo ya kanjedza zomwe anazilemba mochita kugoba pazitsekozo anazikutanso ndi golide. 33  Anapanganso chimodzimodzi ndi khomo la kachisi,* pamafelemu ake a mtengo wa paini omwe anali mbali ya 4. 34  Anapanga zitseko ziwiri zamatabwa a mitengo yofanana ndi mkungudza. Chitseko choyamba chinali ndi mbali ziwiri ndipo hafu inkatsegukira mbali ina, hafu ina inkatsegukira mbali ina. Chitseko chachiwiri chinalinso ndi mbali ziwiri ndipo hafu inkatsegukira mbali ina, hafu ina inkatsegukira mbali ina.+ 35  Pazitsekopo anajambulapo mochita kugoba akerubi, mitengo ya kanjedza komanso maluwa ndipo anakuta zojambulazo ndi golide. 36  Anamanga bwalo lamkati+ la mizere itatu ya miyala yosema komanso mzere umodzi wa matabwa a mkungudza.+ 37  Mʼchaka cha 4 cha ulamuliro wa Solomo, mwezi wa Zivi,* anamanga maziko a nyumba ya Yehova.+ 38  Ndipo mʼchaka cha 11, mwezi wa Buli,* (womwe ndi mwezi wa 8), anamaliza zinthu zonse panyumbayo mogwirizana ndi pulani yake.+ Choncho Solomo anamanga nyumbayo zaka 7.

Mawu a M'munsi

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira,“kachisi wa nyumba.”
Apa akunena za Malo Oyera.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumanja.”
Mitengo ya junipa ndi yofanana ndi mitengo ya mkungudza.
Amenewa ndi Malo Oyera amene anali kutsogolo kwa Malo Oyera Koposa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mtengo wa mafuta.”
Amenewa anali Malo Oyera Koposa.
Apa akunena za Malo Oyera.