1 Mafumu 9:1-28

  • Yehova anaonekeranso kwa Solomo (1-9)

  • Mphatso zimene Solomo anapatsa Hiramu (10-14)

  • Zinthu zimene Solomo anamanga (15-28)

9  Solomo atangomaliza kumanga nyumba ya Yehova, nyumba yachifumu+ ndiponso zinthu zonse zimene anafuna kupanga,+  Yehova anaonekera kwa iye kachiwiri, ngati mmene anachitira ku Gibiyoni.+  Yehova anamuuza kuti: “Ndamva pemphero lako ndi pempho lako lopempha chifundo. Ndayeretsa nyumba imene wamangayi poikamo dzina langa mpaka kalekale+ ndipo maso anga ndi mtima wanga zidzakhala mmenemo nthawi zonse.+  Iweyo ukayenda mʼnjira zanga ngati mmene bambo ako Davide anachitira,+ yemwe anali ndi mtima wokhulupirika+ komanso ankachita zoyenera,+ ukachita zonse zimene ndinakulamula,+ ndiponso ukamamvera malangizo anga ndi ziweruzo zanga,+  ndidzakhazikitsa mpando wako wachifumu mu Isiraeli mpaka kalekale, ngati mmene ndinalonjezera bambo ako Davide kuti, ‘Munthu wa mʼbanja lako sadzachoka pampando wachifumu wa Isiraeli.’+  Koma inuyo ndi ana anu mukadzasiya kunditsatira nʼkusiyanso kutsatira malamulo anga amene ndakupatsani komanso mukadzapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira,+  ndidzachotsa Aisiraeli mʼdziko limene ndawapatsa+ ndipo nyumba imene ndaiyeretsa chifukwa cha dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga.+ Aisiraeli adzatonzedwa ndi kunyozedwa pakati pa mitundu yonse ya anthu.+  Nyumbayi idzakhala bwinja.+ Aliyense wodutsa pafupi adzayangʼana modabwa ndipo adzaimba mluzu nʼkunena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova anachitira zimenezi dzikoli komanso nyumbayi?’+  Ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chakuti anasiya Yehova Mulungu wawo amene anatulutsa makolo awo mʼdziko la Iguputo ndipo anatenga milungu ina nʼkumaigwadira ndi kuitumikira. Nʼchifukwa chake Yehova anawabweretsera tsoka lonseli.’”+ 10  Solomo anamanga nyumba ziwiri, nyumba ya Yehova ndi nyumba yachifumu, ndipo anazimanga kwa zaka 20.+ 11  Hiramu+ mfumu ya Turo anathandiza Solomo ndi matabwa a mkungudza, matabwa a mitengo yofanana ndi mkungudza komanso golide yense amene Mfumu Solomo ankafuna.+ Choncho Mfumu Solomo anapatsa Hiramu mizinda 20 mʼdera la Galileya. 12  Ndiyeno Hiramu anachoka ku Turo nʼkupita kukaona mizinda imene Solomo anamupatsa, koma ataiona sinamusangalatse. 13  Ndipo anati: “Mʼbale wanga, mizinda imene wandipatsayi ubwino wake uli pati?” Choncho mizindayo anaitchula kuti Dziko la Kabulu* mpaka lero. 14  Pa nthawiyo, Hiramu anatumiza kwa mfumuyo golide wokwana matalente* 120.+ 15  Mfumu Solomo inagwiritsa ntchito anthu ogwira ntchito yokakamiza+ kuti amange nyumba ya Yehova,+ nyumba* yake, Chimulu cha Dothi,*+ mpanda wa Yerusalemu ndiponso mzinda wa Hazori,+ wa Megido+ ndi wa Gezeri.+ 16  (Mʼmbuyomo, Farao mfumu ya Iguputo anabwera nʼkulanda mzinda wa Gezeri ndipo anautentha ndi moto. Komanso anapha Akanani+ okhala mumzindawo. Kenako anaupereka kwa mwana wake wamkazi+ monga mphatso pamene ankakwatiwa ndi Solomo.) 17  Solomo anamanganso Gezeri, Beti-horoni Wakumunsi,+ 18  Baalati+ ndi Tamara mʼchipululu cha mʼdzikolo. 19  Anamanganso mizinda yake yonse yosungirako zinthu, mizinda yosungirako magaleta,+ mizinda ya amuna okwera pamahatchi ndiponso zilizonse zimene iye anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi mʼmadera onse amene ankalamulira. 20  Panalinso Aamori onse otsala, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi,+ amene sanali Aisiraeli,+ 21  komanso mbadwa zawo zimene zinatsala mʼdzikomo, zomwe Aisiraeli analephera kuzipha. Anthu onsewa Solomo ankawagwiritsa ntchito yaukapolo ndipo akupitiriza kugwira ntchito yaukapoloyi mpaka lero.+ 22  Koma palibe Aisiraeli amene Solomo anawasandutsa akapolo,+ chifukwa iwo anali asilikali ake, atumiki ake, akalonga ake, asilikali othandiza pa magaleta ndiponso atsogoleri a asilikali ake oyendetsa magaleta ndi amuna okwera pamahatchi. 23  Panali akuluakulu oyangʼanira nduna okwana 550 amene ankayangʼanira ntchito ya Solomo. Iwowa ankayangʼanira anthu ogwira ntchito.+ 24  Mwana wamkazi+ wa Farao anachoka mu Mzinda wa Davide+ nʼkukakhala kunyumba yake imene Solomo anamʼmangira. Kenako Solomo anamanga Chimulu cha Dothi.*+ 25  Katatu pachaka,+ Solomo ankapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano paguwa lansembe limene anamangira Yehova.+ Ankaperekanso nsembe zautsi paguwa lansembe lomwe linali pamaso pa Yehova. Choncho anamaliza kumanga nyumbayo.+ 26  Mfumu Solomo inapanganso zombo ku Ezioni-geberi+ pafupi ndi Eloti, pagombe la Nyanja Yofiira, mʼdziko la Edomu.+ 27  Mʼzombomo, Hiramu ankatumizamo antchito ake odziwa bwino zapanyanja+ kuti akagwire ntchito limodzi ndi antchito a Solomo. 28  Iwo ankapita ku Ofiri+ nʼkukatenga golide wokwana matalente 420 nʼkubwera naye kwa Mfumu Solomo.

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “Dziko Lopanda Pake.”
Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “Milo.” Amenewa ndi mawu a Chiheberi otanthauza “kudzaza.”
Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
Kapena kuti, “Milo.” Amenewa ndi mawu a Chiheberi otanthauza “kudzaza.”