1 Mbiri 10:1-14

  • Imfa ya Sauli ndi ana ake (1-14)

10  Afilisiti anayamba kumenyana ndi Aisiraeli ndipo asilikali a Isiraeli ankathawa moti ambiri anaphedwa mʼphiri la Giliboa.+  Afilisiti anayandikira kwambiri Sauli ndi ana ake ndipo anapha Yonatani, Abinadabu ndi Malikisuwa,+ ana a Sauli.  Nkhondo inamukulira kwambiri Sauli, moti kenako oponya mivi ndi uta anamupeza nʼkumuvulaza.+  Kenako Sauli anauza womunyamulira zida kuti: “Solola lupanga lako undibaye kuti anthu osadulidwawa asandipeze nʼkundipha mwankhanza.”+ Koma womunyamulira zidayo sankafuna chifukwa ankachita mantha kwambiri. Choncho Sauli anatenga lupanga lake nʼkuligwera.+  Womunyamulira zidayo ataona kuti Sauli wafa, nayenso anagwera lupanga lake nʼkufa.  Choncho Sauli ndi ana ake atatu anafa ndipo anthu onse amʼnyumba yake anafera limodzi.+  Aisiraeli onse amene anali mʼchigwa ataona kuti aliyense wathawa komanso Sauli ndi ana ake afa, anayamba kuthawa mʼmizinda yawo. Kenako Afilisiti anabwera nʼkuyamba kukhala mʼmizindayo.  Tsiku lotsatira, Afilisiti atabwera kudzatenga zinthu za anthu amene anaphedwa, anapeza Sauli ndi ana ake atafa paphiri la Giliboa.+  Iwo anamuvula Sauli zida zake nʼkumudula mutu. Kenako anauza anthu mʼdziko lonse la Afilisiti kuti afalitse uthengawu kwa mafano awo+ ndiponso kwa anthu onse. 10  Kenako anakaika zida zakezo mʼnyumba* ya mulungu wawo ndipo mutu wake anaumangirira kunyumba ya Dagoni.+ 11  Anthu onse a ku Yabesi+ ku Giliyadi anamva zonse zimene Afilisiti anamuchita Sauli.+ 12  Ndiyeno asilikali onse anapita kukanyamula mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake nʼkupita nayo ku Yabesi. Atatero anakwirira mafupa a anthuwo pansi pa mtengo waukulu ku Yabesiko.+ Kenako anasala kudya masiku 7. 13  Choncho Sauli anafa chifukwa chakuti anasonyeza kuti ndi wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Iye sanamvere mawu a Yehova+ komanso anapita kukafunsa kwa wolankhula ndi mizimu+ 14  mʼmalo mofunsa kwa Yehova. Choncho iye anamupha nʼkupereka ufumuwo kwa Davide mwana wa Jese.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mʼkachisi.”