1 Mbiri 12:1-40
-
Anthu amene anali kumbali ya ufumu wa Davide (1-40)
12 Awa ndi anthu amene anapita kwa Davide ku Zikilaga+ pa nthawi imene iye sankayenda momasuka chifukwa choopa Sauli+ mwana wa Kisi. Iwowa anali ena mwa asilikali amphamvu amene anamuthandiza pankhondo.+
2 Amuna amenewa anali onyamula mauta ndipo ankatha kugwiritsa ntchito mkono wamanja ndi wamanzere+ poponya miyala ndi gulaye+ kapena poponya mivi ndi uta. Amenewa anali abale ake a Sauli, a fuko la Benjamini.+
3 Mtsogoleri wawo anali Ahiyezeri limodzi ndi Yowasi. Amenewa anali ana a Semaa wa ku Gibeya.+ Panalinso Yezieli ndi Peleti, ana a Azimaveti,+ Beraka, Yehu wa ku Anatoti
4 ndiponso Isimaya wa ku Gibiyoni,+ mwamuna wamphamvu pa amuna 30+ komanso mtsogoleri wa amuna 30 amenewo. Panalinso Yeremiya, Yahazieli, Yohanani, Yozabadi wa ku Gedera,
5 Eluzai, Yerimoti, Bealiya, Semariya ndi Sefatiya wa ku Harifi.
6 Komanso panali Elikana, Isiya, Azareli, Yoezeri ndi Yasobeamu. Amenewa anali mbadwa za Kora.+
7 Panalinso Yoela ndi Zebadiya, ana a Yerohamu wa ku Gedori.
8 Anthu ena a fuko la Gadi anapita kumbali ya Davide pamene iye anali kumalo ovuta kufikako mʼchipululu.+ Amenewa anali asilikali amphamvu, ophunzitsidwa bwino nkhondo ndipo ankakhala okonzeka ndi zishango zawo zazikulu ndiponso mikondo yawo ingʼonoingʼono. Nkhope zawo zinali ngati za mikango ndipo anali aliwiro ngati mbawala mʼmapiri.
9 Mtsogoleri wawo anali Ezeri, wachiwiri anali Obadiya, wachitatu Eliyabu,
10 wa 4 Misimana, wa 5 Yeremiya,
11 wa 6 Atai, wa 7 Elieli,
12 wa 8 Yohanani, wa 9 Elizabadi,
13 wa 10 Yeremiya ndipo wa 11 anali Makibanai.
14 Amenewa anali a fuko la Gadi,+ atsogoleri a asilikali. Wamngʼono akanatha kulimbana ndi asilikali 100 ndipo wamkulu akanatha kulimbana ndi asilikali 1,000.+
15 Awa ndi amene anawoloka mtsinje wa Yorodano mʼmwezi woyamba* pamene mtsinjewo unasefukira. Ndipo anathamangitsira kumʼmawa ndi kumadzulo anthu onse amene ankakhala mʼzigwa.
16 Nawonso amuna ena a fuko la Benjamini ndi la Yuda anapita kwa Davide kumalo ovuta kufikako.+
17 Ndiyeno Davide anatuluka kukakumana nawo ndipo anawauza kuti: “Ngati mwabwerera mtendere komanso kudzandithandiza, mtima wanga ugwirizana nanu. Koma ngati mwabwera kudzandipereka kwa adani anga, pamene manja anga ndi osalakwa, Mulungu wa makolo athu aone zimenezo ndipo aweruze.”+
18 Kenako Amasai, mkulu wa asilikali 30, anayankha mothandizidwa ndi mzimu+ kuti:
“Ife ndife anthu anu, inu a Davide ndipo tili kumbali yanu inu mwana wa Jese.+
Mtendere ukhale nanu ndiponso mtendere ukhale ndi amene akukuthandizani,Chifukwa Mulungu wanu akukuthandizani.”+
Choncho Davide anawalandira nʼkuwaika mʼgulu la atsogoleri a asilikali.
19 Panalinso anthu ena a fuko la Manase amene anapita kwa Davide pamene iye anabwera ndi Afilisiti kudzamenyana ndi Sauli. Koma Davide sanathandize Afilisitiwo chifukwa olamulira awo atakambirana,+ anamʼbweza poganiza kuti: “Ameneyu akhoza kukatitembenukira nʼkugwirizana ndi mbuye wake Sauli, nʼkutipha.”+
20 Davide atapita ku Zikilaga,+ anthu ena a fuko la Manase anapita kumbali yake. Anthuwo anali Adinala, Yozabadi, Yediyaeli, Mikayeli, Yozabadi, Elihu ndi Ziletai. Aliyense anali mtsogoleri wa asilikali 1,000, a fuko la Manase.+
21 Iwo anathandiza Davide kulimbana ndi gulu la achifwamba, chifukwa onsewa anali amuna amphamvu ndi olimba mtima ndipo anakhala atsogoleri a asilikali.+
22 Tsiku lililonse anthu ankabwera kwa Davide+ kudzamuthandiza, mpaka anachuluka nʼkukhala gulu lalikulu lankhondo, ngati gulu lankhondo la Mulungu.+
23 Awa ndi manambala a atsogoleri a anthu okonzekera kumenya nkhondo amene anabwera kwa Davide ku Heburoni,+ kudzamʼpatsa ufumu wa Sauli mogwirizana ndi lamulo la Yehova.+
24 Anthu a fuko la Yuda, onyamula zishango zazikulu ndi mikondo ingʼonoingʼono, okonzekera kumenya nkhondo, analipo 6,800.
25 Anthu a fuko la Simiyoni, omwe anali asilikali amphamvu ndi olimba mtima, analipo 7,100.
26 A fuko la Levi analipo 4,600.
27 Yehoyada+ anali mtsogoleri wa ana a Aroni+ ndipo ankayangʼanira anthu 3,700.
28 Panalinso Zadoki, mnyamata wamphamvu ndi wolimba mtima ndiponso atsogoleri 22 amʼnyumba ya makolo ake.+
29 A fuko la Benjamini, abale ake a Sauli,+ analipo 3,000 ndipo ambiri mwa anthu amenewa, poyamba ankalondera nyumba ya Sauli.
30 A fuko la Efuraimu analipo 20,800, amuna amphamvu, olimba mtima ndiponso otchuka pa anthu amʼnyumba za makolo awo.
31 A hafu ya fuko la Manase, analipo 18,000, amene anatchulidwa mayina kuti adzaveke Davide ufumu.
32 A fuko la Isakara, amene anali ndi nzeru zotha kudziwa nthawi ndi zimene Aisiraeli ayenera kuchita, analipo atsogoleri 200 ndipo ankalamulira abale awo onse.
33 A fuko la Zebuloni, analipo 50,000, okonzeka kumenya nkhondo ndipo anali ndi zida zonse zomenyera nkhondo. Onsewa anapita kwa Davide ndipo sanapite ndi mtima wachinyengo.
34 A fuko la Nafitali analipo atsogoleri 1,000 ndipo anali ndi onyamula zishango zazikulu ndi mikondo, okwana 37,000.
35 A fuko la Dani, analipo 28,600 ndipo anali okonzeka kumenya nkhondo.
36 A fuko la Aseri oyenera kupita kunkhondo, omwe anali okonzeka kumenya nkhondo, analipo 40,000.
37 Kutsidya lina la Yorodano+ kunachokera asilikali a fuko la Rubeni, a fuko la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase okwana 120,000, okhala ndi zida zonse zankhondo.
38 Onsewa anali asilikali okonzeka kumenya nkhondo. Iwo anapita ndi mtima wonse ku Heburoni kukaveka Davide ufumu wa Isiraeli yense. Aisiraeli ena onse otsala nawonso ankagwirizana nazo ndi mtima wonse zoti Davide avekedwe ufumu.+
39 Anthuwa anakhala kumeneko ndi Davide masiku atatu ndipo ankadya ndi kumwa zimene abale awo anawakonzera.
40 Ndiponso anthu onse apafupi ndi kumeneko, mpaka kumadera a Isakara, Zebuloni ndi Nafitali, ankabweretsa chakudya pa abulu, ngamila, nyulu* ndi ngʼombe. Anabweretsa zakudya zophikidwa ndi ufa. Anabweretsanso makeke a nkhuyu, makeke a mphesa, vinyo, mafuta, ngʼombe ndi nkhosa. Anabweretsa zambirimbiri chifukwa anthu mu Isiraeli anasangalala kwambiri.