1 Mbiri 13:1-14

  • Likasa linatengedwa ku Kiriyati-yearimu (1-14)

13  Davide anakambirana ndi atsogoleri a anthu 1,000 ndi a anthu 100 ndiponso mtsogoleri aliyense.+  Kenako anauza gulu lonse la Isiraeli kuti: “Ngati mukuona kuti ndi bwino ndiponso ngati zili zovomerezeka kwa Yehova Mulungu wathu, tiyeni titumize uthenga kwa abale athu mʼmadera onse a Isiraeli. Uthengawu upitenso kwa ansembe ndi Alevi mʼmizinda yawo yonse+ yokhala ndi malo odyetserako ziweto, kuti abwere kuno.  Ndiyeno tikatenge Likasa+ la Mulungu wathu nʼkubwera nalo kuno.” Ananena zimenezi chifukwa mʼmasiku a Sauli likasalo silinkasamalidwa.+  Gulu lonse linagwirizana nazo, chifukwa onse anaona kuti ndi bwino kutero.  Choncho Davide anasonkhanitsa Aisiraeli onse kuchokera kumtsinje* wa Iguputo mpaka kukafika polowera ku Lebo-hamati,*+ kuti akatenge Likasa la Mulungu woona ku Kiriyati-yearimu.+  Davide ndi Aisiraeli onse anapita ku Baala,+ ku Kiriyati-yearimu, amene ali mʼdera la Yuda kukatenga Likasa la Mulungu woona, Yehova, amene amakhala pamwamba* pa akerubi.+ Pa Likasa limeneli, anthu amaitanirapo dzina lake.  Koma iwo ananyamulira Likasa la Mulungu woonalo pangolo yatsopano+ kuchokera kunyumba ya Abinadabu. Uza ndi Ahiyo ndi amene ankatsogolera ngoloyo.+  Davide ndi Aisiraeli onse ankasangalala kwambiri pamaso pa Mulungu woona. Iwo ankaimba nyimbo ndi azeze, zoimbira zina za zingwe, maseche,+ zinganga+ ndi malipenga.+  Koma atafika kumalo opunthira mbewu a Kidoni, Uza anatambasula dzanja lake nʼkugwira Likasalo, chifukwa ngʼombe zinatsala pangʼono kuligwetsa. 10  Zitatero Yehova anakwiyira kwambiri Uza ndipo anamupha chifukwa anatambasula dzanja lake nʼkugwira Likasa,+ moti Uza anafera pomwepo pamaso pa Mulungu.+ 11  Koma Davide anakwiya* chifukwa Yehova anakwiyira kwambiri Uza. Malo amenewa amadziwika ndi dzina lakuti Perezi-uza* mpaka lero. 12  Choncho Davide anachita mantha kwambiri ndi Mulungu woona tsiku limenelo ndipo anati: “Ndiye ndilitenga bwanji Likasa la Mulungu woona nʼkupita nalo kumene ine ndikukhala?”+ 13  Davide sanatenge Likasalo kupita nalo kumene ankakhala, ku Mzinda wa Davide. Mʼmalomwake iye analamula kuti lipite kunyumba ya Obedi-edomu wa ku Gati.* 14  Likasa la Mulungu woona linakhala kunyumba ya Obedi-edomu kwa miyezi itatu ndipo Yehova ankadalitsa banja la Obedi-edomu komanso zonse zimene anali nazo.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kuchokera ku Sihori.”
Kapena kuti, “polowera ku Hamati.”
Mabaibulo ena amati, “pakati.”
Kapena kuti, “anakhumudwa.”
Kutanthauza “Kukwiyira kwambiri Uza.”
Mawu akuti “Gati” mwina akunena za mzinda wa Gati-rimoni.