1 Mbiri 17:1-27

  • Davide anauzidwa kuti sadzamanga kachisi (1-6)

  • Pangano la ufumu ndi Davide (7-15)

  • Pemphero la Davide loyamika (16-27)

17  Davide atangoyamba kukhala mʼnyumba* yake, anauza Natani+ mneneri kuti: “Ine ndikukhala mʼnyumba ya mitengo ya mkungudza,+ pamene likasa la pangano la Yehova likukhala mutenti.”+  Natani anauza Davide kuti: “Chitani chilichonse chimene mtima wanu ukufuna, chifukwa Mulungu woona ali nanu.”  Usiku wa tsiku lomwelo, Mulungu analankhula ndi Natani kuti:  “Pita ukauze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Si iweyo amene udzandimangire nyumba yoti ndizikhalamo.+  Kuchokera tsiku limene ndinatulutsa Aisiraeli mpaka lero, sindinakhalepo mʼnyumba koma nthawi zonse ndinkayendayenda kuchoka mutenti kupita mutenti ndiponso kuchoka muchihema chopatulika kupita muchihema china.*+  Pa nthawi yonse imene ndinkayenda ndi Aisiraeli, kodi ndinayamba ndafunsapo oweruza a Isiraeli amene ndinawasankha kuti azitsogolera anthu anga kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’”’  Tsopano mtumiki wanga Davide ukamuuze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ine ndinakutenga kubusa kumene unkaweta nkhosa kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli.+  Ine ndidzakhala nawe kulikonse kumene ungapite+ ndipo ndidzagonjetsa adani ako onse pamaso pako.+ Ndidzachititsa kuti dzina lako lidziwike ngati mmene zimakhalira ndi anthu otchuka mʼdzikoli.+  Anthu anga Aisiraeli ndidzawasankhira malo nʼkuwakhazika pamalowo. Iwo adzakhala pamenepo ndipo sadzasokonezedwanso. Anthu oipa sadzawaponderezanso ngati mmene ankachitira kale,+ 10  pa nthawi imene ndinasankha oweruza kuti azitsogolera anthu anga Aisiraeli.+ Ndipo ndidzagonjetsa adani ako onse.+ Kuwonjezera pamenepo, ndikukuuza kuti: ‘Yehova adzakumangira nyumba.’* 11  Ukadzamwalira nʼkugona mʼmanda ndi makolo ako, ndidzachititsa kuti mbadwa* yako, mmodzi wa ana ako,+ akhale mfumu ndipo ndidzachititsa kuti ufumu wake ukhazikike.+ 12  Iye ndi amene adzandimangire nyumba+ ndipo ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mpaka kalekale.+ 13  Ine ndidzakhala bambo ake ndipo iye adzakhala mwana wanga.+ Sindidzamuchotsera chikondi changa chokhulupirika+ ngati mmene ndinachitira kwa munthu yemwe analipo iwe usanakhalepo.+ 14  Ndidzamuchititsa kuti akhale woyangʼanira nyumba yanga ndi ufumu wanga mpaka kalekale,+ ndipo mpando wake wachifumu udzakhalapo mpaka kalekale.”’”+ 15  Natani anauza Davide mawu onsewa ndiponso masomphenya onse amene anaona. 16  Kenako Mfumu Davide anakhala pansi pamaso pa Yehova ndipo anati: “Ndine ndani ine, inu Yehova Mulungu? Ndipo banja lathu* nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndili pano?+ 17  Inu Mulungu, kuwonjezeranso pamenepa mwandiuza kuti nyumba ya ine mtumiki wanu idzakhazikika mpaka mʼtsogolo kwambiri+ ndipo inu Yehova Mulungu, mwanditenga ine ngati munthu woyenera kukwezedwa.* 18  Ndiyeno ine Davide mtumiki wanu ndinganene chiyani kwa inu poona ulemu umene mwandipatsa chonsecho inu mumandidziwa bwino ine mtumiki wanu?+ 19  Inu Yehova, chifukwa cha ine mtumiki wanu, komanso mogwirizana ndi zofuna za mtima wanu,* mwachita zazikulu zonsezi pondidziwitsa kuti mumachita zazikulu.+ 20  Inu Yehova, palibe amene angafanane ndi inu+ komanso palibe Mulungu wina koma inu nokha.+ Zonse zimene tamva zikutsimikizira zimenezi. 21  Ndi mtundu uti padziko lapansi umene ungafanane ndi mtundu wa anthu anu Aisiraeli?+ Inu Mulungu woona munapita kukawombola anthu anu.+ Komanso munadzipangira dzina pamene munawachitira zinthu zazikulu ndi zochititsa mantha,+ pothamangitsa mitundu ina pamaso pa anthu anu+ amene munawawombola ku Iguputo. 22  Munachititsa Aisiraeli kuti akhale anthu anu nthawi zonse.+ Ndipo inu Yehova munakhala Mulungu wawo.+ 23  Choncho inu Yehova, chitani zimene mwalonjeza zokhudza mtumiki wanu ndi nyumba yake ndipo muchite zimenezi mpaka kalekale. Muchite mogwirizana ndi zimene mwalonjeza.+ 24  Dzina lanu likhalepobe ndipo likwezeke+ mpaka kalekale kuti anthu anene kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndi Mulungu wa Isiraeli.’ Ndipo nyumba ya ine mtumiki wanu Davide ikhazikike pamaso panu.+ 25  Chifukwa inu, Mulungu wanga, mwandiululira ine mtumiki wanu cholinga chanu choti mukufuna kundimangira nyumba.* Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera kwa inu pempheroli. 26  Inu Yehova ndinu Mulungu woona ndipo mwalonjeza zinthu zabwinozi zokhudza ine mtumiki wanu. 27  Choncho dalitsani nyumba ya ine mtumiki wanu kuti ikhazikike pamaso panu mpaka kalekale. Chifukwa inu Yehova mwadalitsa nyumba ya ine mtumiki wanu ndipo yadalitsika mpaka kalekale.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
Nʼkutheka kuti akutanthauza “kuchoka pamalo amene amanga tenti kupita pamalo ena komanso kuchoka pamalo amene anakhala kupita pamalo ena.”
Kapena kuti, “mzere wa mafumu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nyumba yanga.”
Kapena kuti, “woyenera kukhala pamalo apamwamba.”
Kapena kuti, “mogwirizana ndi chifuniro chanu.”
Kapena kuti, “mzere wa mafumu.”