1 Mbiri 18:1-17

  • Davide anapambana nkhondo zosiyanasiyana (1-13)

  • Ulamuliro wa Davide (14-17)

18  Patapita nthawi, Davide anagonjetsa Afilisiti+ nʼkuwalanda mzinda wa Gati+ ndi midzi yake yozungulira.  Kenako anagonjetsa Amowabu+ moti Amowabuwo anakhala atumiki a Davide ndipo ankapereka msonkho kwa iye.+  Davide anagonjetsa Hadadezeri+ mfumu ya Zoba+ pafupi ndi Hamati,+ pamene Hadadezeriyo ankapita kukakhazikitsa ulamuliro wake kumtsinje wa Firate.+  Davide analanda Hadadezeri magaleta 1,000 komanso anagwira amuna 7,000 okwera pamahatchi ndi asilikali 20,000 oyenda pansi.+ Kenako Davide anapundula* mahatchi onse a magaleta nʼkungosiya mahatchi 100.+  Asiriya a ku Damasiko atabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya Zoba, Davide anapha Asiriya 22,000.+  Kenako Davide anamanga midzi ya asilikali mʼdera la Asiriya a ku Damasiko ndipo Asiriyawo anakhala akapolo a Davide moti ankapereka msonkho kwa iye. Yehova ankathandiza Davide kuti apambane kulikonse kumene wapita.+  Komanso Davide anatenga zishango zozungulira zagolide za atumiki a Hadadezeri nʼkupita nazo ku Yerusalemu.  Komanso Davide anatenga kopa* wambiri ku Tibati ndi ku Kuni, mizinda ya Hadadezeri. Solomo anagwiritsa ntchito kopa ameneyu kupangira thanki yosungira madzi,+ zipilala ndi ziwiya zina.+  Toi, mfumu ya Hamati, atamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezeri,+ mfumu ya Zoba,+ 10  nthawi yomweyo anatumiza mwana wake Hadoramu kwa Mfumu Davide kukamufunsa za moyo wake ndiponso kukamuyamikira chifukwa chomenyana ndi Hadadezeri nʼkumugonjetsa. (Chifukwa Hadadezeri ankakonda kumenyana ndi Toi.) Popita kwa Davide, Hadoramu anatenga zinthu zasiliva, zagolide ndi zakopa. 11  Mfumu Davide anapereka zinthu zimenezi kwa Yehova+ pamodzi ndi siliva komanso golide amene anatenga kuchokera ku mitundu yonse. Anatenga kuchokera kwa Aedomu, Amowabu, Aamoni,+ Afilisiti+ ndi Aamaleki.+ 12  Abisai+ mwana wa Zeruya,+ anapha Aedomu 18,000 mʼchigwa cha Mchere.+ 13  Iye anakhazikitsa midzi ya asilikali ku Edomu ndipo Aedomu onse anakhala antchito a Davide.+ Yehova ankathandiza Davide kuti apambane kulikonse kumene wapita.+ 14  Davide anapitiriza kulamulira Isiraeli yense+ ndipo ankalimbikitsa chilungamo kwa anthu ake onse.+ 15  Yowabu mwana wa Zeruya anali mkulu wa asilikali+ ndipo Yehosafati+ mwana wa Ahiludi ankalemba zimene zachitika. 16  Zadoki mwana wa Ahitubu ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara anali ansembe ndipo Savisa anali mlembi. 17  Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti+ ndi Apeleti+ ndipo ana aamuna a Davide anali achiwiri kwa mfumu.

Mawu a M'munsi

Ankawapundula powadula mtsempha wakuseri kwa mwendo wamʼmbuyo.
Kapena kuti, “mkuwa.”