1 Mbiri 19:1-19

  • Chipongwe chimene Aamoni anachitira atumiki a Davide (1-5)

  • Aamoni ndi Asiriya anagonjetsedwa (6-19)

19  Kenako Nahasi, mfumu ya Aamoni, anamwalira ndipo mwana wake anayamba kulamulira mʼmalo mwake.+  Zitatero, Davide anati: “Ndimusonyeza Hanuni mwana wa Nahasi chikondi chokhulupirika+ chifukwa bambo ake anandisonyeza chikondi chokhulupirika.” Choncho Davide anatumiza anthu kuti akamutonthoze chifukwa cha imfa ya bambo ake. Koma atumiki a Davidewo atafika mʼdziko la Aamoni+ kuti atonthoze Hanuni,  akalonga a Aamoni anauza Hanuni kuti: “Kodi mukuganiza kuti Davide watumiza anthu odzakutonthozani chifukwa cholemekeza bambo anu? Kodi iye sanatumize atumiki akewa kuti adzafufuze zokhudza mzindawu nʼcholinga choti adzaulande?”  Choncho Hanuni anatenga atumiki a Davide aja nʼkuwameta ndevu,+ kenako anadula zovala zawo pakati moti zinalekeza mʼmatako nʼkuwauza kuti azipita.  Davide atamva zomwe zinachitikira atumiki akewo, nthawi yomweyo anatumiza anthu kuti akakumane nawo chifukwa atumiki akewo anali atachititsidwa manyazi kwambiri. Choncho mfumu inawauza kuti: “Mukhalebe ku Yeriko+ mpaka ndevu zanu zitakula, kenako mudzabwere.”  Patapita nthawi, Aamoni anaona kuti akhala ngati chinthu chonunkha kwa Davide. Choncho Hanuni ndi Aamoni anatumiza anthu nʼkuwapatsira matalente* asiliva 1,000 kuti akabwereke magaleta komanso kulemba ganyu asilikali okwera pamahatchi a ku Mesopotamiya,* a ku Aramu-maaka ndi a ku Zoba.+  Choncho anakabwereka magaleta 32,000 ndiponso kulemba ganyu mfumu ya ku Maaka ndi anthu ake. Zitatero, iwo anabwera nʼkumanga misasa yawo pafupi ndi Medeba.+ Aamoni anatuluka mʼmizinda yawo nʼkusonkhana kuti akamenye nkhondo.  Davide atamva zimenezi, anatumiza Yowabu+ ndi gulu lonse lankhondo, limodzinso ndi asilikali ake amphamvu.+  Ndiyeno Aamoni anapita kukaima pageti la mzinda atakonzekera kumenya nkhondo. Pomwe mafumu omwe anabwera aja anali kwaokha kutchire. 10  Yowabu ataona kuti adani ake akubwera kuchokera kutsogolo ndi kumbuyo, anasankha ena mwa magulu a asilikali amphamvu mu Isiraeli nʼkuwakonzekeretsa kuti amenyane ndi Asiriya.+ 11  Anthu ena onse anawapereka kwa mchimwene wake Abisai+ kuti awatsogolere pokamenyana ndi Aamoni. 12  Ndiyeno anamuuza kuti: “Ukaona kuti Asiriya+ akundigonjetsa, ubwere udzandipulumutse. Koma Aamoni akayamba kukugonjetsa, ineyo ndibwera kudzakupulumutsa. 13  Tikuyenera kuchita zinthu mwamphamvu komanso molimba mtima+ chifukwa cha anthu athu ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu. Yehova adzachita zimene akuona kuti nʼzabwino kwa iye.” 14  Kenako Yowabu ndi amuna amene anali naye anapita kukamenyana ndi Asiriya ndipo Asiriyawo anayamba kuthawa.+ 15  Aamoni ataona kuti Asiriya athawa, nawonso anathawa Abisai mchimwene wake wa Yowabu nʼkupita mumzinda. Kenako Yowabu anabwerera ku Yerusalemu. 16  Asiriya ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisiraeli, anatuma anthu kukaitana Asiriya amene anali mʼdera la ku Mtsinje*+ ndipo Sofaki, mkulu wa asilikali a Hadadezeri, ndi amene ankawatsogolera.+ 17  Davide atamva zimenezi, nthawi yomweyo anasonkhanitsa Aisiraeli onse nʼkuwoloka Yorodano kupita kukakumana nawo ndipo anakonzekera kumenya nkhondo. Davide anakonzekera kuti amenyane ndi Asiriya ndipo Asiriyawo anayamba kumenyana naye.+ 18  Koma Asiriya anayamba kuthawa Aisiraeli ndipo Davide anapha asilikali a Asiriya 7,000 okwera magaleta komanso asilikali 40,000 oyenda pansi. Iye anaphanso Sofaki, mkulu wa gulu lankhondo la Asiriya. 19  Atumiki a Hadadezeri ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisiraeli,+ nthawi yomweyo anakhazikitsa mtendere ndi Davide nʼkuyamba kumutumikira.+ Asiriya sanafunenso kuthandiza Aamoni.

Mawu a M'munsi

Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Aramu-naharaimu.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.