1 Mbiri 2:1-55

  • Ana 12 a Isiraeli (1, 2)

  • Mbadwa za Yuda (3-55)

2  Ana a Isiraeli+ anali awa: Rubeni,+ Simiyoni,+ Levi,+ Yuda,+ Isakara,+ Zebuloni,+  Dani,+ Yosefe,+ Benjamini,+ Nafitali,+ Gadi+ ndi Aseri.+  Ana a Yuda anali Ere, Onani ndi Shela. Mwana wamkazi wa Sua wa Chikanani ndi amene anamʼberekera ana atatuwa.+ Koma Ere, mwana woyamba wa Yuda, anachita zoipa pamaso pa Yehova ndipo iye anamupha.+  Tamara,+ mpongozi wake, anamʼberekera Perezi+ ndi Zera. Ana onse a Yuda analipo 5.  Ana a Perezi anali Hezironi ndi Hamuli.+  Ana a Zera anali Zimiri, Etani, Hemani, Kalikoli ndi Dara. Onse analipo 5.  Mwana* wa Karami anali Akari,* amene anabweretsa mavuto mu Isiraeli.+ Iye anachita zinthu zosakhulupirika pa nkhani ya zinthu zoyenera kuwonongedwa.+  Mwana* wa Etani anali Azariya.  Ana amene Hezironi anabereka anali Yerameeli,+ Ramu+ ndi Kelubai.* 10  Ramu anabereka Aminadabu,+ Aminadabu anabereka Naasoni+ mtsogoleri wa Ayuda. 11  Naasoni anabereka Salima,+ Salima anabereka Boazi,+ 12  Boazi anabereka Obedi, Obedi anabereka Jese,+ 13  Jese anabereka mwana wake woyamba Eliyabu, wachiwiri Abinadabu,+ wachitatu Simeya,+ 14  wa 4 Netaneli, wa 5 Radai, 15  wa 6 Ozemu ndipo wa 7 anali Davide.+ 16  Azichemwali awo anali Zeruya ndi Abigayeli.+ Zeruya anali ndi ana atatu: Abisai,+ Yowabu+ ndi Asaheli.+ 17  Abigayeli anabereka Amasa+ ndipo bambo ake a Amasa anali Yeteri mbadwa ya Isimaeli. 18  Kalebe* mwana wa Hezironi anabereka ana kudzera mwa Azuba mkazi wake ndiponso kudzera mwa Yerioti. Ana akewo anali Yeseri, Sobabu ndi Aridoni. 19  Azuba atamwalira, Kalebe anakwatira Efurati+ ndipo anamuberekera Hura.+ 20  Hura anabereka Uri. Uri anabereka Bezaleli.+ 21  Kenako Hezironi anagona ndi mwana wamkazi wa Makiri+ bambo a Giliyadi.+ Hezironi ali ndi zaka 60, anakwatira mwana wamkazi wa Makiriyo ndipo mkaziyo anamʼberekera Segubu. 22  Segubu anabereka Yairi,+ amene anali ndi mizinda 23 mʼdziko la Giliyadi.+ 23  Kenako Gesuri+ ndi Siriya+ analanda Havoti-yairi.+ Analandanso Kenati+ ndi midzi yake yozungulira, mizinda 60. Onsewa anali ana a Makiri, bambo a Giliyadi. 24  Hezironi+ atamwalira ku Kalebe-efurata, Abiya mkazi wake anamuberekera Ashari+ bambo a Tekowa.+ 25  Ana a Yerameeli, mwana woyamba wa Hezironi, anali Ramu woyamba kubadwa, kenako Buna, Oreni, Ozemu ndi Ahiya. 26  Yerameeli analinso ndi mkazi wina dzina lake Atara. Iye anali mayi ake a Onamu. 27  Ana a Ramu, mwana woyamba wa Yerameeli, anali Maazi, Yamini ndi Ekeri. 28  Ana a Onamu anali Samai ndi Yada. Ana a Samai anali Nadabu ndi Abisuri. 29  Mkazi wa Abisuri dzina lake linali Abihaili ndipo anamʼberekera Abani ndi Molidi. 30  Ana a Nadabu anali Seledi ndi Apaimu. Koma Seledi anamwalira wopanda ana. 31  Mwana* wa Apaimu anali Isi, mwana* wa Isi anali Sesani, mwana* wa Sesani anali Alai. 32  Ana a Yada, mchimwene wake wa Samai, anali Yeteri ndi Yonatani. Koma Yeteri anamwalira wopanda ana. 33  Ana a Yonatani anali Pelete ndi Zaza. Amenewa anali mbadwa za Yerameeli. 34  Sesani analibe ana aamuna, koma aakazi okhaokha. Iye anali ndi wantchito wa ku Iguputo dzina lake Yaha. 35  Sesani anapereka mwana wake wamkazi kwa Yaha kuti akhale mkazi wake ndipo anamuberekera Atai. 36  Atai anabereka Natani, Natani anabereka Zabadi, 37  Zabadi anabereka Efilali, Efilali anabereka Obedi, 38  Obedi anabereka Yehu, Yehu anabereka Azariya, 39  Azariya anabereka Helezi, Helezi anabereka Eleasa, 40  Eleasa anabereka Sisimai, Sisimai anabereka Salumu, 41  Salumu anabereka Yekamiya ndipo Yekamiya anabereka Elisama. 42  Ana a Kalebe,*+ mchimwene wake wa Yerameeli, anali Mesa mwana wake woyamba, yemwe anali bambo ake a Zifi. Panalinso ana a Maresha bambo ake a Heburoni. 43  Ana a Heburoni anali Kora, Tapuwa, Rekemu ndi Sema. 44  Sema anabereka Rahamu bambo a Yorikeamu. Rekemu anabereka Samai. 45  Mwana wa Samai anali Maoni ndipo Maoni anali bambo ake a Beti-zuri.+ 46  Efa, mkazi wamngʼono* wa Kalebe, anabereka Harana, Moza ndi Gazezi. Harana anabereka Gazezi. 47  Ana a Yahadai anali Regemu, Yotamu, Gesani, Peleti, Efa ndi Safa. 48  Maaka, mkazi wamngʼono wa Kalebe, anabereka Seberi ndi Tirana. 49  Patapita nthawi anabereka Safa bambo ake a Madimana+ komanso Seva bambo ake a Makibena ndi Gibeya.+ Mwana wamkazi wa Kalebe+ anali Akisa.+ 50  Amenewa anali mbadwa za Kalebe. Ana a Hura,+ mwana woyamba wa Efurata,+ anali Sobala, bambo a Kiriyati-yearimu,+ 51  Salima, bambo a Betelehemu+ ndiponso Harefi, bambo a Beti-gaderi. 52  Sobala, bambo a Kiriyati-yearimu, anabereka ana awa: Haroye ndi hafu ya anthu otchedwa Amenuhoti. 53  Mabanja a Kiriyati-yearimu anali Aitiri,+ Aputi, Asumati ndi Amisirai. Azorati+ ndi Aesitaoli+ anachokera ku mabanja amenewa. 54  Ana a Salima anali anthu okhala ku Betelehemu,+ ku Netofa ndi ku Atiroti-beti-yowabu. Hafu ya anthu a ku Manahati ndi anthu a ku Zora, analinso ana a Salima. 55  Mabanja a alembi amene ankakhala ku Yabezi anali Atirati, Asimeati ndi Asukati. Amenewa anali Akeni+ amene anachokera kwa Hamati bambo a nyumba ya Rekabu.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana.”
Kutanthauza “Wobweretsa Mavuto; Wobweretsa Tsoka.” Pa Yoswa 7:1 akutchedwa Akani.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana.”
Akutchedwanso Kalebe pavesi 18, 19 ndi 42.
Akutchedwanso Kelubai pavesi 9.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana.”
Akutchedwanso Kelubai pavesi 9.
Kapena kuti, “mdzakazi.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.