1 Mbiri 20:1-8

  • Raba anagonjetsedwa (1-3)

  • Ziphona za Afilisiti zinaphedwa (4-8)

20  Kumayambiriro kwa chaka, pa nthawi imene mafumu ankapita kukamenya nkhondo, Yowabu+ anatsogolera gulu lankhondo nʼkukawononga dziko la Aamoni ndiponso kuzungulira mzinda wa Raba.+ Koma Davide anatsala ku Yerusalemu.+ Yowabu anaukira mzinda wa Raba nʼkuuwononga.+  Kenako Davide anatenga chipewa chachifumu chimene chinali kumutu kwa Malikamu. Anapeza kuti chinali cholemera talente imodzi* ya golide ndipo chinali chokongoletsedwa ndi miyala yamtengo wapatali. Anthu anaveka Davide chipewacho. Komanso iye anatenga zinthu zambiri mumzindawo.+  Davide anatenga anthu amene anali mumzindawo nʼkuyamba kuwagwiritsa ntchito+ yocheka miyala komanso ntchito zina zogwiritsa ntchito zitsulo zakuthwa ndi nkhwangwa. Zimenezi ndi zimene anachitira anthu onse amʼmizinda ya Aamoni. Kenako Davide ndi asilikali onse anabwerera ku Yerusalemu.  Nkhondo imeneyi itatha, panabukanso nkhondo ina ndi Afilisiti ku Gezeri. Pa nthawi imeneyo Sibekai+ wa ku Husa* anapha Sipa, amene anali mbadwa ya Arefai,+ moti Afilisiti anagonjetsedwa.  Kenako panabukanso nkhondo ina ndi Afilisiti, ndipo Elihanani mwana wa Yairi anapha Lami, mchimwene wake wa Goliyati+ wa ku Gati, amene mtengo wa mkondo wake unali waukulu ngati mtengo wogwiritsa ntchito powomba nsalu.+  Kenako panayambikanso nkhondo ina ku Gati+ ndipo kunali munthu wamkulu modabwitsa.+ Iye anali ndi zala 6 kudzanja lililonse ndiponso zala 6 kuphazi lililonse, moti anali ndi zala 24. Nayenso anali mbadwa ya Arefai.+  Iye ankanyoza+ kwambiri Aisiraeli. Choncho Yonatani mwana wa Simeya,+ mchimwene wake wa Davide, anamupha.  Anthu amenewa anali mbadwa za Arefai+ ku Gati+ ndipo anaphedwa ndi Davide ndi atumiki ake.

Mawu a M'munsi

Talente imodzi inkalemera makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
Mabaibulo ena amati, “mbadwa ya Husa.”