1 Mbiri 21:1-30

  • Davide anawerenga anthu mosavomerezeka (1-6)

  • Chilango chochokera kwa Yehova (7-17)

  • Davide anamanga guwa (18-30)

21  Kenako Satana* anayamba kulimbana ndi Isiraeli ndipo anachititsa Davide kuti awerenge Aisiraeli.+  Choncho Davide anauza Yowabu+ ndi atsogoleri a anthu kuti: “Pitani mukawerenge Aisiraeli kuyambira ku Beere-seba mpaka ku Dani+ ndipo mubweretse lipoti kuti ndidziwe chiwerengero chawo.”  Koma Yowabu anati: “Yehova awonjezere anthu ake kuwirikiza ka 100. Mbuyanga mfumu, kodi anthu onsewa si anu komanso si atumiki anu kale? Ndiye nʼchifukwa chiyani mbuyanga mukufuna kuchita zimenezi? Nʼchifukwa chiyani mukufuna kupalamulitsa Aisiraeli?”  Koma mfumu inakana kumvera zimene Yowabu ananena. Choncho Yowabu ananyamuka ndipo anayenda mu Isiraeli monse. Kenako anabwerera ku Yerusalemu.+  Yowabu anapereka kwa Davide chiwerengero cha anthu amene anawerengedwa. Amuna onse a mafuko a Isiraeli okhala ndi lupanga analipo 1,100,000 ndipo amuna a fuko la Yuda okhala ndi lupanga, analipo 470,000.+  Koma Yowabu sanawerenge anthu a fuko la Levi ndi la Benjamini,+ chifukwa mawu a mfumu anamunyansa kwambiri.+  Zinthu zimenezi sizinasangalatse Mulungu woona ndipo anapha Aisiraeli.  Kenako Davide anauza Mulungu woona kuti: “Ndachimwa+ kwambiri pochita zimenezi. Chonde ndikhululukireni tchimo langa ine mtumiki wanu,+ chifukwa ndachita zopusa kwambiri.”+  Ndiyeno Yehova analankhula ndi Gadi,+ wamasomphenya wa Davide kuti: 10  “Pita, ukamuuze Davide kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Pali zilango zitatu zimene ndingakupatse ndipo iwe usankhepo chimodzi.”’” 11  Choncho Gadi anapita kwa Davide nʼkumuuza kuti: “Yehova wanena kuti: ‘Sankhapo chimodzi: 12  Zaka zitatu za njala+ kapena miyezi itatu yoti adani anu akuseseni ndi kukuphani ndi lupanga lawo,+ kapenanso masiku atatu a lupanga la Yehova, lomwe ndi mliri umene udzagwe mʼdziko+ lanu pamene mngelo wa Yehova adzawononge+ madera onse a Isiraeli.’ Ganizirani zoti ndikayankhe kwa amene wandituma.” 13  Davide atamva zimenezo, anauza Gadi kuti: “Zimenezi zikundisowetsa mtendere kwambiri. Kuli bwino ndilangidwe ndi Yehova, chifukwa chifundo chake nʼchachikulu,+ koma ndisalangidwe ndi munthu.”+ 14  Ndiyeno Yehova anagwetsa mliri+ mu Isiraeli, moti anthu 70,000 anafa mu Isiraeli.+ 15  Komanso Mulungu woona anatumiza mngelo ku Yerusalemu kuti akawononge mzindawo. Koma mngeloyo atangotsala pangʼono kuyamba kuwononga, Yehova anaona zimenezo ndipo anamva chisoni chifukwa cha mliriwo,+ choncho anauza mngelo amene ankawonongayo kuti: “Basi!+ Bweza dzanja lako.” Pa nthawiyi, mngelo wa Yehovayo anali ataima pafupi ndi malo opunthira mbewu a Orinani+ wa Chiyebusi.+ 16  Davide atakweza maso, anaona mngelo wa Yehova ataima mʼmalere* atagwira lupanga+ nʼkuloza Yerusalemu ndi lupangalo. Davide ndi akulu amene anali naye anali atavala ziguduli+ ndipo nthawi yomweyo, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo kufika pansi.+ 17  Davide anauza Mulungu woona kuti: “Kodi si ine amene ndinanena kuti awerenge anthu? Ine ndi amene ndachimwa, ineyo ndi amene ndalakwa.+ Nanga nkhosazi zalakwa chiyani? Chonde Yehova Mulungu wanga, dzanja lanu lindilange ineyo ndi anthu amʼnyumba ya bambo anga. Koma musagwetsere mliriwu anthu anu.”+ 18  Ndiyeno mngelo wa Yehova anauza Gadi+ kuti auze Davide kuti apite kumalo opunthira mbewu a Orinani wa Chiyebusi, nʼkukamangira Yehova guwa lansembe.+ 19  Choncho Davide anapitadi mogwirizana ndi mawu amene Gadi ananena mʼdzina la Yehova. 20  Pa nthawiyi nʼkuti Orinani akupuntha tirigu. Atatembenuka anaona mngelo ndipo ana ake 4 amene anali naye limodzi anabisala. 21  Davide atafika kwa Orinani, Orinani nʼkumuona Davideyo, nthawi yomweyo anachoka pamalo opunthira mbewu aja nʼkugwada pamaso pa Davide ndipo anawerama mpaka nkhope yake kufika pansi. 22  Kenako Davide anauza Orinani kuti: “Undigulitse* malo ako opunthira mbewuwa kuti ndimangirepo Yehova guwa lansembe kuti mliriwu uthe pakati pa anthuwa.+ Undiuze ndalama zake zonse.” 23  Koma Orinani anauza Davide kuti: “Ingotengani malowa kwaulere ndipo mbuyanga mfumu chitani chilichonse chimene mukuona kuti nʼchabwino. Ineyo ndipereka ngʼombe kuti zikhale nsembe zopsereza ndi chopunthira tirigu+ kuti chikhale nkhuni ndiponso ndipereka tirigu kuti akhale nsembe yambewu. Ndikupereka zonsezi.” 24  Koma Mfumu Davide inauza Orinani kuti: “Ayi, ndikuyenera kugula ndipo ndipereka ndalama zake zonse, chifukwa sindingatenge zinthu zako nʼkupereka kwa Yehova kapena kupereka nsembe zopsereza popanda kulipira chilichonse.”+ 25  Choncho Davide anapatsa Orinani ndalama zokwana masekeli* 600 agolide zogulira malowo. 26  Ndiyeno Davide anamangira Yehova guwa lansembe+ pamalowo ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamgwirizano. Komanso anaitana pa dzina la Yehova ndipo tsopano anamuyankha potumiza moto+ kuchokera kumwamba umene unafika paguwa lansembe yopsereza. 27  Kenako Yehova analamula mngelo+ uja kuti abwezere lupanga lake mʼchimake. 28  Davide ataona kuti Yehova wamuyankha pamalo opunthira mbewu a Orinani wa Chiyebusi, anapitiriza kuperekera nsembe pamalopo. 29  Pa nthawiyo, chihema chopatulika cha Yehova chimene Mose anapanga mʼchipululu ndiponso guwa lansembe zopsereza, zinali pamalo okwezeka a ku Gibiyoni.+ 30  Koma Davide sankapita kumeneko kukafunsira kwa Mulungu, chifukwa ankaopa lupanga la mngelo wa Yehova.

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “wotsutsa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Undipatse.”
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.