1 Mbiri 22:1-19

  • Davide anakonzekera zinthu zomangira kachisi (1-5)

  • Davide anapereka malangizo kwa Solomo (6-16)

  • Akalonga analamulidwa kuti athandize Solomo (17-19)

22  Kenako Davide anati: “Malo ano ndi nyumba ya Yehova Mulungu woona ndipo lili apali, ndi guwa lansembe zopsereza za Isiraeli.”+  Atatero, Davide analamula kuti asonkhanitse alendo okhala mʼdziko la Isiraeli.+ Alendowo anawapatsa ntchito yosema miyala, kuti azisema miyala yomangira nyumba ya Mulungu woona.+  Komanso Davide anasonkhanitsa zitsulo zambirimbiri zopangira misomali ya zitseko za mageti ndiponso zopangira zida zopanira zinthu. Anasonkhanitsanso kopa* wambirimbiri wosatheka kumuyeza kulemera kwake.+  Davide anasonkhanitsanso matabwa osawerengeka a mkungudza,+ popeza Asidoni+ ndi anthu a ku Turo+ anali atamubweretsera matabwa ambirimbiri a mkungudza.  Kenako Davide anati: “Mwana wanga Solomo ndi wamngʼono komanso sadziwa zambiri+ ndipo nyumba yoti adzamangire Yehova idzakhala yaikulu, yokongola+ ndi yogometsa+ nʼcholinga choti idzakhale yodziwika padziko lonse.+ Ndiye ndimukonzera zipangizo zoti adzagwiritsire ntchito.” Choncho Davide asanafe, anasonkhanitsa zipangizo zambirimbiri pokonzekera ntchitoyo.  Komanso anaitana mwana wake Solomo ndipo anamupatsa malangizo okhudza ntchito yomanga nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli.  Davide anauza mwana wake Solomo kuti: “Ineyo ndinkafunitsitsa kumanga nyumba ya dzina la Yehova Mulungu wanga.+  Koma Yehova anandiuza kuti: ‘Iweyo wapha anthu* ambirimbiri ndipo wamenya nkhondo zikuluzikulu. Sudzamanga nyumba ya dzina langa,+ chifukwa wapha anthu ambirimbiri pamaso panga padziko lapansi.  Tamvera, udzabereka mwana.+ Mwana ameneyo adzakhala munthu wokonda mtendere ndipo ndidzachititsa kuti azikhala mwamtendere komanso asamavutitsidwe ndi adani ake omuzungulira.+ Nʼchifukwa chake dzina lake adzakhala Solomo*+ ndipo mʼmasiku ake ndidzapatsa Aisiraeli bata ndi mtendere.+ 10  Iyeyo ndi amene adzamange nyumba ya dzina langa.+ Adzakhala mwana wanga ndipo ine ndidzakhala bambo ake.+ Ndidzakhazikitsa mpando wake wachifumu mu Isiraeli ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.’+ 11  Tsopano mwana wanga, Yehova akhale nawe ndipo zinthu zikuyendere bwino. Umange nyumba ya Yehova Mulungu wako, mogwirizana ndi zimene iye analankhula zokhudza iweyo.+ 12  Yehova akupatse nzeru ndi kuzindikira.+ Akupatsenso mphamvu zotsogolera Aisiraeli, kuti usunge chilamulo cha Yehova Mulungu wako.+ 13  Zinthu zidzakuyendera bwino ukamatsatira mosamala malamulo+ ndi ziweruzo zimene Yehova analamula Mose kuti apatse Aisiraeli.+ Khala wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usaope kapena kuchita mantha.+ 14  Ndayesetsa mwakhama kusonkhanitsa golide womangira nyumba ya Yehova wokwana matalente* 100,000 ndi siliva wokwana matalente 1 miliyoni. Koma nʼzosatheka kuyeza kulemera kwa kopa ndi zitsulo+ chifukwa nʼzochuluka kwambiri. Ndasonkhanitsanso matabwa ndi miyala+ pokonzekera, koma udzawonjezerapo zina. 15  Palinso antchito ambirimbiri. Pali osema miyala, amisiri a miyala+ ndi a matabwa ndiponso akatswiri a ntchito zosiyanasiyana.+ 16  Golide, siliva, kopa ndi zitsulo nʼzosatheka kuziwerenga.+ Yamba kugwira ntchito imeneyi ndipo Yehova akhale nawe.”+ 17  Kenako Davide analamula akalonga onse a Isiraeli kuti athandize mwana wake Solomo. Iye anati: 18  “Kodi Yehova Mulungu wanu sali nanu? Kodi sanakupatseni mtendere mʼdziko lonseli? Chifukwa wandipatsa anthu amʼdzikoli ndipo dzikoli lili mʼmanja mwa Yehova ndi anthu ake. 19  Choncho muzifunafuna Yehova Mulungu wanu+ ndi mtima wanu wonse ndiponso moyo wanu wonse. Yambani kumanga nyumba yopatulika ya Yehova Mulungu woona,+ kuti mukatenge likasa la pangano la Yehova ndi ziwiya zopatulika za Mulungu woona+ nʼkuziika mʼnyumba ya dzina la Yehova imene imangidweyo.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mkuwa.”
Kapena kuti, “wakhetsa magazi.”
Kuchokera ku mawu a Chiheberi otanthauza, “Mtendere.”
Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.