1 Mbiri 23:1-32

  • Davide anapereka ntchito kwa Alevi (1-32)

    • Aroni ndi ana ake anasankhidwa kuti azigwira ntchito yopatulika (13)

23  Davide atakalamba ndiponso atatsala pangʼono kufa, anapereka kwa mwana wake Solomo ufumu wa Isiraeli.+  Kenako anasonkhanitsa akalonga onse a Isiraeli, ansembe+ komanso Alevi.+  Atatero, Alevi anawerengedwa kuyambira azaka 30 kupita mʼtsogolo.+ Anawerenga mwamuna aliyense mmodzi ndi mmodzi* ndipo onse anakwana 38,000.  Pa anthu amenewa, 24,000 anali oyangʼanira ntchito yapanyumba ya Yehova. Akapitawo ndi oweruza analipo 6,000.+  Panalinso alonda 4,000 apageti+ ndi anthu 4,000 otamanda+ Yehova poimba ndi zoimbira zimene Davide anati, “Zimenezi ndazipanga kuti tizitamandira Mulungu.”  Ndiyeno Davide anawagawa mʼmagulu+ mogwirizana ndi ana a Levi: Gerisoni, Kohati ndi Merari.+  Ku banja la Gerisoni kunali Ladani ndi Simeyi.  Ana a Ladani anali atatu. Panali Yehiela mtsogoleri wawo, Zetamu ndi Yoweli.+  Ana a Simeyi anali atatu: Selomoti, Hazieli ndi Harana. Amenewa anali atsogoleri a nyumba za makolo a Ladani. 10  Ana a Simeyi anali Yahati, Zina,* Yeusi ndi Beriya. Ana 4 amenewa anali a Simeyi. 11  Yahati anali mtsogoleri wawo ndipo wachiwiri wake anali Ziza. Koma Yeusi ndi Beriya analibe ana ambiri aamuna, choncho anawawerenga ngati nyumba imodzi ya makolo ndipo udindo wawo unali umodzi. 12  Ana a Kohati analipo 4: Amuramu, Izara,+ Heburoni ndi Uziyeli.+ 13  Ana a Amuramu anali Aroni+ ndi Mose.+ Koma Aroni anasankhidwa+ kuti iye ndi ana ake azitumikira mʼMalo Oyera Koposa mpaka kalekale. Komanso kuti azipereka nsembe pamaso pa Yehova, kumutumikira ndi kudalitsa anthu mʼdzina lake nthawi zonse.+ 14  Ponena za Mose munthu wa Mulungu woona, ana ake anawawerenga pamodzi ndi fuko la Levi. 15  Ana a Mose anali Gerisomu+ ndi Eliezere.+ 16  Ana a Gerisomu, mtsogoleri wawo anali Sebueli.+ 17  Mbadwa* za Eliezere, mtsogoleri wawo anali Rehabiya.+ Eliezere sanakhalenso ndi ana ena aamuna, koma Rehabiya anali ndi ana aamuna ambirimbiri. 18  Ana a Izara,+ mtsogoleri wawo anali Selomiti.+ 19  Ana a Heburoni anali Yeriya, amene anali mtsogoleri wawo, wachiwiri wake anali Amariya, wachitatu anali Yahazieli ndipo wa 4 anali Yekameamu.+ 20  Ana a Uziyeli+ anali Mika, amene anali mtsogoleri wawo ndipo Isiya anali wachiwiri wake. 21  Ana a Merari anali Mali ndi Musi.+ Ana a Mali anali Eliezara ndi Kisi. 22  Eliezara anamwalira koma analibe ana aamuna, anali ndi aakazi okhaokha. Choncho abale awo, ana a Kisi, anawatenga kukhala akazi awo. 23  Ana a Musi analipo atatu: Mali, Ederi ndi Yeremoti. 24  Amenewa anali ana a Levi potsatira nyumba za makolo awo ndiponso atsogoleri a nyumba za makolo awo. Iwo analembedwa komanso kuwerengedwa potsatira mndandanda wa mayina awo. Amenewa ankatumikira panyumba ya Yehova kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo. 25  Chifukwa Davide ananena kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wapereka mpumulo kwa anthu ake+ ndipo iye adzakhala mu Yerusalemu mpaka kalekale.+ 26  Komanso, Alevi sazinyamulanso chihema chopatulika kapena zipangizo zake zogwiritsa ntchito potumikira kumeneko.”+ 27  Chifukwa mogwirizana ndi malangizo omaliza a Davide, Alevi oyambira zaka 20 kupita mʼtsogolo, anawerengedwa. 28  Ntchito yawo inali yothandiza ana a Aroni+ pa utumiki wapanyumba ya Yehova, kuyangʼanira mabwalo a nyumbayo,+ zipinda zodyeramo, ntchito yoyeretsa chinthu chilichonse chopatulika ndiponso ntchito iliyonse yofunika potumikira panyumba ya Mulungu woona. 29  Ankathandizanso ntchito zokhudza mkate wosanjikiza,*+ ufa wosalala wa nsembe yambewu, mikate yopyapyala yopanda zofufumitsa,+ makeke ophika mʼchiwaya, ufa wokandakanda wosakaniza ndi mafuta+ ndiponso miyezo yosiyanasiyana. 30  Mʼmawa uliwonse ankaimirira+ kuti athokoze ndi kutamanda Yehova. Madzulo ankachitanso zimenezi.+ 31  Ankathandizanso pa nthawi iliyonse yopereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa Masabata,+ pa masiku amene mwezi watsopano waoneka+ ndi pa nthawi ya zikondwerero.+ Ankachita zimenezi nthawi zonse pamaso pa Yehova, malinga ndi ziwerengero zake zogwirizana ndi malamulo ake. 32  Ana a Leviwa analinso ndi udindo wokhudza chihema chokumanako, malo oyera ndiponso abale awo, omwe anali ana a Aroni, pa utumiki wapanyumba ya Yehova.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mutu ndi mutu.”
Ameneyu ndi Ziza wotchulidwa mʼvesi 11.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana.”
Umenewu unali mkate wachionetsero.