1 Mbiri 25:1-31

  • Oimba panyumba ya Mulungu (1-31)

25  Davide ndi atsogoleri a magulu a anthu otumikira, anasankha ena mwa ana a Asafu, a Hemani ndi a Yedutuni+ kuti azitumikira polosera ndi azeze, zoimbira za zingwe+ ndi zinganga.+ Anthu audindo amene anawasankha kuti azichita utumiki umenewu anali awa:  Pa ana a Asafu, anatengapo Zakuri, Yosefe, Netaniya ndi Asarela. Ana akewa ankatsogoleredwa ndi Asafuyo, amenenso ankalosera, ndipo ankayangʼaniridwa ndi mfumu.  Kwa Yedutuni,+ anatengako ana ake awa: Gedaliya, Zeri, Yesaiya, Simeyi, Hasabiya ndi Matitiya,+ onse pamodzi analipo 6. Iwowa ankayangʼaniridwa ndi Yedutuni bambo awo, amene ankalosera ndi zeze ndipo ankayamika ndi kutamanda Yehova.+  Kwa Hemani,+ anatengako ana ake awa: Bukiya, Mataniya, Uziyeli, Sebueli, Yerimoti, Hananiya, Haneni, Eliyata, Gidaliti, Romamiti-ezeri, Yosebekasa, Maloti, Hotiri ndi Mahazioti.  Onsewa anali ana a Hemani, wamasomphenya wa mfumu pa zinthu za Mulungu woona pofuna kutamanda Mulungu.* Choncho Mulungu woona anapatsa Hemani ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu.  Ana onsewa ankayangʼaniridwa ndi bambo awo poimba nyimbo panyumba ya Yehova. Ankaimba nyimbozo ndi zinganga, zoimbira za zingwe ndi azeze,+ potumikira panyumba ya Mulungu woona. Koma Asafu, Yedutuni ndi Hemani ankayangʼaniridwa ndi mfumu.  Chiwerengero chawo, pamodzi ndi abale awo ophunzitsidwa kuimbira Yehova, chinali 288 ndipo onse anali akatswiri.  Kenako anachita maere+ powagawira ntchito yoti azichita. Pochita maerewo, sankayangʼana kuti uyu ndi wamngʼono kapena wamkulu, katswiri kapena wophunzira kumene.  Maere oyamba anagwera Yosefe mwana wa Asafu,+ achiwiri anagwera Gedaliya+ (iye ndi abale ake ndiponso ana ake analipo 12). 10  Achitatu anagwera Zakuri,+ iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 11  a 4 anagwera Iziri, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 12  a 5 anagwera Netaniya,+ iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 13  a 6 anagwera Bukiya, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 14  a 7 anagwera Yesarela, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 15  a 8 anagwera Yesaiya, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 16  a 9 anagwera Mataniya, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 17  a 10 anagwera Simeyi, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 18  a 11 anagwera Azareli, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 19  a 12 anagwera Hasabiya, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 20  a 13 anagwera Subaeli,+ iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 21  a 14 anagwera Matitiya, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 22  a 15 anagwera Yeremoti, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 23  a 16 anagwera Hananiya, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 24  a 17 anagwera Yosebekasa, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 25  a 18 anagwera Haneni, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 26  a 19 anagwera Maloti, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 27  a 20 anagwera Eliyata, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 28  a 21 anagwera Hotiri, iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 29  a 22 anagwera Gidaliti,+ iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 30  a 23 anagwera Mahazioti,+ iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12, 31  ndipo maere a 24 anagwera Romamiti-ezeri,+ iye ndi ana ake ndiponso abale ake analipo 12.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambira, “kukweza nyanga yake.”