1 Mbiri 26:1-32

  • Magulu a alonda apageti (1-19)

  • Oyangʼanira chuma ndi anthu a maudindo ena (20-32)

26  Magulu a alonda apageti+ anali awa: Pa mbadwa za Kora panali Meselemiya,+ mwana wa Kore wochokera mwa ana a Asafu.  Ndipo ana a Meselemiya anali awa: Woyamba anali Zekariya, wachiwiri Yediyaeli, wachitatu Zebadiya, wa 4 Yatiniyeli,  wa 5 Elamu, wa 6 Yehohanani ndipo wa 7 anali Eliho-enai.  Obedi-edomu anali ndi ana awa: Woyamba anali Semaya, wachiwiri Yehozabadi, wachitatu Yowa, wa 4 Sakari, wa 5 Netaneli,  wa 6 Amiyeli, wa 7 Isakara ndipo wa 8 anali Peuletai, chifukwa Mulungu anamudalitsa.  Semaya mwana wa Obedi-edomu anabereka ana omwe anali olamulira nyumba ya bambo awo, chifukwa anawo anali odalirika ndi amphamvu.  Ana a Semaya anali Otini, Refaeli, Obedi ndi Elizabadi. Elizabadi anali ndi abale ake odalirika, Elihu ndi Semakiya.  Onsewa anali mbadwa za Obedi-edomu. Iwowa, ana awo ndi abale awo anali odalirika ndi oyenerera kutumikira. Onse analipo 62 ndipo anali mbadwa za Obedi-edomu.  Meselemiya+ anali ndi ana komanso abale ake, amuna odalirika okwana 18. 10  Hosa, mbadwa ya Merari anali ndi ana ndipo Simuri anali mtsogoleri wawo. Ngakhale kuti sanali woyamba kubadwa, bambo ake anamusankha kuti akhale mtsogoleri. 11  Wachiwiri anali Hilikiya, wachitatu Tebaliya ndipo wa 4 anali Zekariya. Ana onse a Hosa ndiponso abale ake analipo 13. 12  Pa magulu a alonda apagetiwa, ntchito ya atsogoleri awo inali yofanana ndi ya abale awo ndipo inali yotumikira panyumba ya Yehova. 13  Choncho anachita maere+ ofanana kwa wamngʼono ndi wamkulu potsatira nyumba za makolo awo, kuti apeze ogwira ntchito pageti lililonse. 14  Maere akumʼmawa anagwera Selemiya. Anachitanso maere a Zekariya mwana wake, yemwe anali mlangizi wanzeru ndipo maere ake anasonyeza kuti akakhale kumpoto. 15  Maere a Obedi-edomu anagwera kumʼmwera ndipo ana ake+ anaikidwa kuti azilondera nyumba zosungiramo zinthu. 16  Maere a Supimu ndi a Hosa+ anagwera kumadzulo pafupi ndi Geti la Saleketi, pamsewu wopita kumtunda. Gulu limodzi la alonda linakhala moyandikana ndi gulu lina la alonda. 17  Kumʼmawa kunali Alevi 6, kumpoto kunkakhala 4 pa tsiku, kumʼmwera 4 pa tsiku ndipo kunyumba zosungiramo katundu+ awiriawiri. 18  Kukhonde lakumadzulo, kumsewu+ kunali 4 ndipo pakhonde panali awiri. 19  Amenewa anali magulu a alonda apageti ochokera ku mbadwa za Kora ndi za Merari. 20  Kumbali ya Alevi, Ahiya ankayangʼanira chuma chamʼnyumba ya Mulungu woona ndiponso zinthu zimene anaziyeretsa kuti zikhale zopatulika.*+ 21  Pa ana a Ladani, panali Yehieli.+ Ana amenewo anali mbadwa za Gerisoni kudzera mwa Ladani ndipo anali atsogoleri a nyumba za makolo za Ladani mbadwa ya Gerisoni 22  ndiponso ana a Yehieli omwe anali Zetamu ndi Yoweli mchimwene wake. Amenewa ankayangʼanira chuma chamʼnyumba ya Yehova.+ 23  Panalinso mbadwa za Amuramu, za Izara, za Heburoni ndi za Uziyeli+ 24  ndipo Sebueli mwana wa Gerisomu mwana wa Mose, anali mtsogoleri woyangʼanira nyumba zosungiramo katundu. 25  Abale ake obadwa mwa Eliezere,+ anali Rehabiya mwana wa Eliezere, Yesaiya mwana wa Rehabiya,+ Yoramu mwana wa Yesaiya, Zikiri mwana wa Yoramu ndi Selomoti mwana wa Zikiri. 26  Selomoti ameneyu pamodzi ndi abale ake ankayangʼanira zinthu zonse zimene anaziyeretsa kuti zikhale zopatulika.+ Amene anaziyeretsa anali Mfumu Davide,+ atsogoleri a nyumba za makolo,+ atsogoleri a magulu a anthu 1,000, a magulu a anthu 100 ndi atsogoleri a asilikali. 27  Anayeretsa zinthu zimene anazitenga+ kunkhondo+ kuti azizigwiritsa ntchito panyumba ya Yehova. 28  Panalinso zinthu zonse zimene Samueli wamasomphenya,+ Sauli mwana wa Kisi, Abineri+ mwana wa Nera ndi Yowabu+ mwana wa Zeruya+ anaziyeretsa kuti zikhale zopatulika. Chilichonse chimene munthu anachiyeretsa chinkayangʼaniridwa ndi Selomiti ndi abale ake. 29  Kumbali ya mbadwa za Izara,+ panali Kenaniya ndi ana ake omwe anali akapitawo ndi oweruza+ Isiraeli, koma ntchito yawoyi ankagwirira kunja kwa nyumba ya Mulungu. 30  Kumbali ya mbadwa za Heburoni,+ panali Hasabiya ndi abale ake, amuna odalirika okwana 1,700. Iwowa ankayangʼanira Aisiraeli mʼchigawo chakumadzulo kwa Yorodano pa ntchito zonse za Yehova ndiponso zotumikira mfumu. 31  Kumbali ya mbadwa za Heburoni, Yereya+ ndi amene anali mtsogoleri wa mbadwa za Heburonizo mogwirizana ndi mibadwo ya makolo awo. Mʼchaka cha 40 cha ufumu wa Davide,+ kunachitika kafukufuku ndipo anapeza amuna amphamvu ndi olimba mtima pakati pawo ku Yazeri+ ku Giliyadi. 32  Ndipo abale a Yereya, amuna odalirika komanso atsogoleri a nyumba za makolo awo, analipo 2,700. Choncho Mfumu Davide inawaika kuti aziyangʼanira anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase pa nkhani iliyonse yokhudza Mulungu woona ndiponso yokhudza mfumu.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “zimene anazipereka kwa Mulungu.”