1 Mbiri 27:1-34

  • Anthu otumikira mfumu (1-34)

27  Awa ndi magulu a Aisiraeli amene anali atsogoleri a nyumba za makolo awo, atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100+ ndiponso anthu omwe ankatumikira mfumu+ pa nkhani iliyonse yokhudza magulu amenewa. Maguluwa ankasinthanasinthana mwezi uliwonse pa chaka ndipo gulu lililonse linali ndi anthu 24,000.  Mtsogoleri wa gulu loyamba, la mwezi woyamba, anali Yasobeamu+ mwana wa Zabidiyeli. Gulu lake linali ndi anthu 24,000.  Yasobeamu anali mbadwa ya Perezi.+ Iye anali mkulu wa atsogoleri onse a magulu amene ankatumikira mwezi woyamba.  Woyangʼanira wa gulu la mwezi wachiwiri anali Dodai+ wa ku Ahohi+ ndipo Mikiloti anali mtsogoleri. Gulu lake linali ndi anthu 24,000.  Mtsogoleri wa gulu lachitatu, lotumikira mwezi wachitatu, anali Benaya+ mwana wa Yehoyada+ wansembe wamkulu. Gulu lake linali ndi anthu 24,000.  Benaya ameneyu anali mwamuna wamphamvu pa amuna 30 komanso anali mtsogoleri wa amuna 30 amenewo. Pagulu lakelo, mwana wake Amizabadi ndi amene anali mtsogoleri.  Mtsogoleri wa 4, wa mwezi wa 4, anali Asaheli+ mchimwene wake wa Yowabu+ ndipo mwana wake Zebadiya analowa mʼmalo mwake. Gulu lake linali ndi anthu 24,000.  Mtsogoleri wa 5, wa mwezi wa 5, anali Samuti mbadwa ya Izirahi. Gulu lake linali ndi anthu 24,000.  Mtsogoleri wa 6, wa mwezi wa 6, anali Ira+ mwana wa Ikesi wa ku Tekowa.+ Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 10  Mtsogoleri wa 7, wa mwezi wa 7, anali Helezi+ wa ku Peloni, mbadwa ya Efuraimu. Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 11  Mtsogoleri wa 8, wa mwezi wa 8, anali Sibekai+ wa ku Husa,* wa ku banja la Zera.+ Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 12  Mtsogoleri wa 9, wa mwezi wa 9, anali Abi-ezeri+ wa ku Anatoti,+ wa fuko la Benjamini. Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 13  Mtsogoleri wa 10, wa mwezi wa 10, anali Maharai+ wa ku Netofa, wa ku banja la Zera.+ Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 14  Mtsogoleri wa 11, wa mwezi wa 11, anali Benaya+ wa ku Piratoni, wa fuko la Efuraimu. Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 15  Mtsogoleri wa 12, wa mwezi wa 12, anali Heledai wa ku Netofa wa kubanja la Otiniyeli. Gulu lake linali ndi anthu 24,000. 16  Atsogoleri a mafuko a Isiraeli anali awa: Mtsogoleri wa fuko la Rubeni anali Eliezere mwana wa Zikiri, wa fuko la Simiyoni anali Sefatiya mwana wa Maaka, 17  wa fuko la Levi anali Hasabiya mwana wa Kemueli, wa ana a Aroni anali Zadoki, 18  wa fuko la Yuda anali Elihu+ mmodzi wa azichimwene ake a Davide, wa fuko la Isakara anali Omuri mwana wa Mikayeli, 19  wa fuko la Zebuloni anali Isimaya mwana wa Obadiya, wa fuko la Nafitali anali Yerimoti mwana wa Azirieli, 20  wa fuko la Efuraimu anali Hoshiya mwana wa Azaziya, wa hafu ya fuko la Manase anali Yoweli mwana wa Pedaya, 21  wa hafu ya fuko la Manase ku Giliyadi anali Ido mwana wa Zekariya, wa fuko la Benjamini anali Yaasiyeli mwana wa Abineri+ 22  ndipo mtsogoleri wa fuko la Dani anali Azareli mwana wa Yerohamu. Amenewa anali akalonga a mafuko a Isiraeli. 23  Davide sanawerenge amuna amene anali ndi zaka 20 kutsika mʼmunsi, chifukwa Yehova analonjeza kuti adzachulukitsa Aisiraeli ngati nyenyezi zakumwamba.+ 24  Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga anthu koma sanamalize. Ndipo Mulungu anakwiyira kwambiri Aisiraeli chifukwa chowerenga anthuwo,+ moti chiwerengerocho sichinalembedwe mʼmbiri ya zochitika za nthawi ya Mfumu Davide. 25  Azimaveti mwana wa Adieli ankayangʼanira chuma cha mfumu.+ Yonatani mwana wa Uziya ankayangʼanira mosungira katundu mʼmadera apafupi, mʼmizinda, mʼmidzi ndi munsanja zosiyanasiyana. 26  Eziri mwana wa Kelubu ankayangʼanira anthu ogwira ntchito yolima minda. 27  Simeyi wa ku Rama anali woyangʼanira minda ya mpesa koma Zabidi wa ku Sifimi anali woyangʼanira zinthu zonse zokhudza vinyo zamʼminda ya mpesayo. 28  Baala-hanani wa ku Gederi anali woyangʼanira mitengo ya maolivi ndi ya mkuyu+ imene inali ku Sefela+ ndipo Yowasi ankayangʼanira mafuta. 29  Sitirai wa ku Sharoni+ ankayangʼanira ziweto zimene ankadyetsera ku Sharoni. Safati mwana wa Adilai ankayangʼanira ziweto zimene zinali kuzigwa. 30  Obili mbadwa ya Isimaeli ankayangʼanira ngamila. Yedeya wa ku Meronoti ankayangʼanira abulu.* 31  Ndipo Yazizi mbadwa ya Hagara ankayangʼanira nkhosa. Anthu onsewa anali oyangʼanira katundu wa Mfumu Davide. 32  Yonatani,+ mwana wa mʼbale wake wa Davide, anali mlangizi wanzeru komanso mlembi. Yehiela mwana wa Hakimoni ankayangʼanira ana a mfumu.+ 33  Ahitofeli+ anali mlangizi wa mfumu ndipo Husai+ mbadwa ya Areki anali mnzake wa mfumu. 34  Ahitofeli analowedwa mʼmalo ndi Yehoyada mwana wa Benaya+ ndi Abiyatara+ ndipo Yowabu+ anali mkulu wa asilikali a mfumu.

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “mbadwa ya Husa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “abulu aakazi.”