1 Mbiri 3:1-24

  • Mbadwa za Davide (1-9)

  • Mzere wa mafumu a mʼbanja la Davide (10-24)

3  Ana amene Davide anabereka ku Heburoni+ anali awa: woyamba Aminoni,+ mayi ake anali Ahinowamu+ a ku Yezereeli, wachiwiri Danieli, mayi ake anali Abigayeli+ a ku Karimeli, 2  wachitatu Abisalomu,+ mayi ake anali Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya Gesuri, wa 4 Adoniya,+ mayi ake anali Hagiti, 3  wa 5 Sefatiya, mayi ake anali Abitali, wa 6 Itireamu, mayi ake anali Egila mkazi wa Davide. 4  Davide anabereka ana 6 amenewa ku Heburoni ndipo analamulira kumeneko zaka 7 ndi miyezi 6. Kenako analamulira zaka 33 ku Yerusalemu.+ 5  Ku Yerusalemu+ iye anabereka ana awa: Simeya, Sobabu, Natani+ ndi Solomo.+ Ana 4 amenewa mayi awo anali Bati-seba+ mwana wa Amiyeli. 6  Analinso ndi ana ena 9 awa: Ibara, Elisama, Elifeleti, 7  Noga, Nefegi, Yafiya, 8  Elisama, Eliyada ndi Elifeleti. 9  Onsewa anali ana a Davide, kuwonjezera pa ana amene akazi ake aangʼono* anamuberekera ndipo Tamara+ anali mchemwali wawo. 10  Mwana wa Solomo anali Rehobowamu.+ Rehobowamu anabereka Abiya,+ Abiya anabereka Asa,+ Asa anabereka Yehosafati,+ 11  Yehosafati anabereka Yehoramu,+ Yehoramu anabereka Ahaziya,+ Ahaziya anabereka Yehoasi,+ 12  Yehoasi anabereka Amaziya,+ Amaziya anabereka Azariya,+ Azariya anabereka Yotamu,+ 13  Yotamu anabereka Ahazi,+ Ahazi anabereka Hezekiya,+ Hezekiya anabereka Manase,+ 14  Manase anabereka Amoni+ ndipo Amoni anabereka Yosiya.+ 15  Ana a Yosiya anali awa: woyamba Yohanani, wachiwiri Yehoyakimu,+ wachitatu Zedekiya+ ndipo wa 4 anali Salumu. 16  Mwana wa Yehoyakimu+ anali Yekoniya. Yekoniya anabereka Zedekiya. 17  Ana amene Yekoniya anabereka ali mkaidi anali Salatiyeli, 18  Malikiramu, Pedaya, Senazara, Yekamiya, Hosama ndi Nedabiya. 19  Ana a Pedaya anali Zerubabele+ ndi Simeyi. Ana a Zerubabele anali Mesulamu ndi Hananiya (Selomiti anali mchemwali wawo). 20  Ana ake ena 5 anali Hasuba, Oheli, Berekiya, Hasadiya ndi Yusabi-hesedi. 21  Ana a Hananiya anali Pelatiya ndi Yesaiya. Mwana* wa Yesaiya anali Refaya, mwana* wa Refaya anali Arinani, mwana wa Arinani anali Obadiya, mwana* wa Obadiya anali Sekaniya, 22  mwana wa Sekaniya anali Semaya ndipo ana a Semaya anali Hatusi, Igali, Bariya, Neariya ndi Safati, onse analipo 6. 23  Ana a Neariya analipo atatu: Elioenai, Hizikiya ndi Azirikamu. 24  Ana a Elioenai analipo 7: Hodaviya, Eliyasibu, Pelaya, Akubu, Yohanani, Delaya ndi Anani.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “adzakazi ake.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana.”