1 Mbiri 4:1-43

  • Mbadwa zina za Yuda (1-23)

    • Yabezi ndiponso pemphero lake (9, 10)

  • Mbadwa za Simiyoni (24-43)

4  Ana a Yuda anali Perezi,+ Hezironi,+ Karami, Hura+ ndi Sobala.+  Reyaya mwana wa Sobala anabereka Yahati. Yahati anabereka Ahumai ndi Lahadi. Amenewa anali mabanja a Azorati.+  A bambo a Etami+ ana awo anali awa: Yezereeli, Isima ndi Idibasi (dzina la mchemwali wawo linali Hazeleleponi).  Penueli anali bambo a Gedori ndipo Ezeri anali bambo a Husa. Amenewa anali ana a Hura,+ mwana woyamba wa Efurata ndiponso bambo a Betelehemu.+  Ashari,+ bambo a Tekowa,+ anali ndi akazi awiri, Hela ndi Naara.  Naara anamʼberekera Ahuzamu, Heferi, Temeni ndi Hahasitari. Amenewa anali ana a Naara.  Ana a Hela anali Zereti, Izara ndi Etinani.  Kozi anabereka Anubu, Zobeba ndi mabanja a Ahaheli mwana wa Harumu.  Yabezi anali wolemekezeka kwambiri kuposa azichimwene ake ndipo mayi ake anamupatsa dzina lakuti Yabezi,* chifukwa anati: “Ndamʼbereka ndikumva ululu.” 10  Yabezi anapemphera kwa Mulungu wa Isiraeli kuti: “Mundidalitse nʼkukulitsa dera langa ndipo dzanja lanu likhale nane komanso munditeteze ku tsoka kuti lisandivulaze.” Choncho Mulungu anachitadi zimene iye anapempha. 11  Kelubu mchimwene wake wa Suha anabereka Mehiri, yemwe anali bambo a Esitoni. 12  Esitoni anabereka Beti-rafa, Paseya ndi Tehina bambo a Iri-nahasi. Amenewa anali amuna a ku Reka. 13  Ana a Kenazi anali Otiniyeli+ ndi Seraya ndipo mwana* wa Otiniyeli anali Hatati. 14  Meyonatai anabereka Ofira. Seraya anabereka Yowabu bambo a Ge-harasimu,* chifukwa iwo anakhala amisiri. 15  Ana a Kalebe+ mwana wa Yefune anali Iru, Ela ndi Naamu. Mwana* wa Ela anali Kenazi. 16  Ana a Yehaleleli anali Zifi, Zifa, Tiriya ndi Asareli. 17  Ana a Ezira anali Yeteri, Meredi, Eferi ndi Yaloni. Mkaziyo* anatenga pakati nʼkubereka Miriamu, Samai ndi Isiba bambo a Esitemowa. 18  Amenewa anali ana a Bitiya, mwana wamkazi wa Farao, amene Meredi anamʼkwatira. (Mkazi wake wa Chiyuda anabereka Yeredi bambo a Gedori, Hiberi bambo a Soko ndi Yekutieli bambo a Zanowa.) 19  Ana a mkazi wa Hodiya, mchemwali wake wa Nahamu, anali bambo a Keila wa ku Garimu ndi bambo a Esitemowa wa ku Maakati. 20  Ana a Shimoni anali Aminoni, Rina, Beni-hanani ndi Tiloni. Ana a Isi anali Zoheti ndi Beni-zoheti. 21  Ana a Shela+ mwana wa Yuda anali Ere bambo a Leka, Laada bambo a Maresha, mabanja a Asibeya omwe ankagwira ntchito yopanga nsalu zabwino kwambiri, 22  Yokimu, amuna a ku Kozeba, Yowasi, Sarafa, (amenewa anakwatira akazi a Chimowabu) ndi Yasubi-lehemu. Zimenezi zachokera mʼzolembedwa zakale. 23  Iwo anali oumba zinthu omwe ankakhala ku Netaimu ndi ku Gedera. Ankakhala kumeneko nʼkumagwirira ntchito mfumu. 24  Ana a Simiyoni+ anali Nemueli, Yamini, Yaribi, Zera ndi Shauli.+ 25  Shauli anabereka Salumu, Salumu anabereka Mibisamu, Mibisamu anabereka Misima, 26  Misima anabereka Hamueli, Hamueli anabereka Zakuri ndipo Zakuri anabereka Simeyi. 27  Simeyi anali ndi ana aamuna 16 aakazi 6, koma azichimwene ake analibe ana ambiri. Pa mabanja awo panalibe banja limene linali ndi ana ambiri ngati mabanja a Ayuda.+ 28  Iwo ankakhala ku Beere-seba,+ ku Molada,+ ku Hazara-suali,+ 29  ku Biliha, ku Ezemu,+ ku Toladi, 30  ku Betuele,+ ku Horima,+ ku Zikilaga,+ 31  ku Beti-marikaboti, ku Hazara-susimu,+ ku Beti-biri ndi ku Saaraimu. Imeneyi inali mizinda yawo mpaka pamene Davide anayamba kulamulira. 32  Ankakhalanso ku Etami, ku Aini, ku Rimoni, ku Tokeni ndi ku Asani.+ Mizinda 5, 33  ndiponso malo awo okhala ozungulira mizinda imeneyi mpaka kukafika ku Baala. Umenewu ndi mndandanda wa mayina awo ndi makolo awo komanso malo amene ankakhala. 34  Ana ena a Simiyoni anali: Mesobabu, Yameleki, Yosa mwana wa Amaziya, 35  Yoweli, Yehu mwana wa Yosibiya, Yosibiya mwana wa Seraya, Seraya mwana wa Asieli 36  ndi Elioenai, Yaakoba, Yesohaya, Asaya, Adieli, Yesimieli, Benaya 37  komanso Ziza mwana wa Sifi, Sifi mwana wa Aloni, Aloni mwana wa Yedaya, Yedaya mwana wa Simuri ndi Simuri mwana wa Semaya. 38  Amene atchulidwa mayinawa anali atsogoleri a mabanja awo ndipo banja la makolo awo linakula kwambiri. 39  Iwo anapita kugeti la mzinda wa Gedori, kumʼmawa kwa chigwa, kukafuna msipu wa ziweto zawo. 40  Kenako anapeza msipu wabwino kwambiri ndipo dera lake linali lalikulu ndiponso lopanda chosokoneza chilichonse. Anthu amene ankakhala kumeneko kale anali mbadwa za Hamu.+ 41  Anthu omwe atchulidwa mayinawa, anapita kumeneko pa nthawi imene Hezekiya+ anali mfumu ya Yuda ndipo anagwetsa mahema a mbadwa za Hamu komanso anapha Ameyuni amene anali kumeneko. Anapha anthuwa ndipo iwo kulibe mpaka lero. Kenako anayamba kukhala kumeneko, chifukwa kunali msipu wa ziweto zawo. 42  Anthu ena a fuko la Simiyoni, amuna okwana 500, anapita kuphiri la Seiri+ ndipo amene ankawatsogolera anali Pelatiya, Neariya, Refaya ndi Uziyeli, ana a Isi. 43  Iwo anapha Aamaleki+ otsala omwe anathawa ndipo akukhala kumeneko mpaka lero.

Mawu a M'munsi

Nʼkutheka kuti dzina lakuti Yabezi linachokera ku mawu a Chiheberi omwe amatanthauza “ululu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana.”
Kutanthauza, “Chigwa cha Amisiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana.”
Nʼkutheka kuti apa akunena za Bitiya yemwe watchulidwa muvesi 18.