1 Mbiri 5:1-26

  • Mbadwa za Rubeni (1-10)

  • Mbadwa za Gadi (11-17)

  • Mbadwa za Hagara zinagonjetsedwa (18-22)

  • Hafu ya fuko la Manase (23-26)

5  Ana a Rubeni,+ mwana woyamba wa Isiraeli anali awa: Rubeni anali woyamba kubadwa koma chifukwa chakuti anaipitsa bedi la bambo ake,+ udindo wake monga woyamba kubadwa unaperekedwa kwa ana a Yosefe,+ mwana wa Isiraeli. Choncho iye sanalembedwe monga woyamba kubadwa pamndandanda wa mayina wotsatira makolo.  Ngakhale kuti Yuda+ anali wamphamvu pakati pa azichimwene ake ndiponso kubanja lake kunachokera wodzakhala mtsogoleri,+ udindo wa woyamba kubadwa unali wa Yosefe.  Ana a Rubeni mwana woyamba wa Isiraeli, anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karami.+  Mwana wa Yoweli anali Semaya. Semaya anabereka Gogi, Gogi anabereka Simeyi,  Simeyi anabereka Mika, Mika anabereka Reyaya, Reyaya anabereka Baala,  Baala anabereka Beeraha yemwe Tigilati-pilenesere,+ mfumu ya Asuri, anamutenga kupita naye ku ukapolo. Iye anali mtsogoleri wa anthu a fuko la Rubeni.  Azichimwene ake potengera mabanja awo pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo, anali Yeyeli yemwe anali mtsogoleri, Zekariya  ndi Bela. Bela anali mwana wa Azazi, Azazi anali mwana wa Sema, Sema anali mwana wa Yoweli. Bela ankakhala mʼdera loyambira ku Aroweli+ mpaka kukafika ku Nebo ndi ku Baala-meoni.+  Dera lake linakafika mpaka kumʼmawa poyambira chipululu pamtsinje wa Firate,+ chifukwa ziweto zawo zinachuluka kwambiri ku Giliyadi.+ 10  Mʼmasiku a Sauli, iwo anamenyana ndi mbadwa za Hagara nʼkuzigonjetsa. Kenako anayamba kukhala mʼmahema awo mʼdera lonse lakumʼmawa kwa Giliyadi. 11  Anthu a fuko la Gadi, omwe ankakhala nawo pafupi, ankakhala ku Basana mpaka ku Saleka.+ 12  Mtsogoleri wawo anali Yoweli ndipo wachiwiri wake anali Safamu. Panalinso Yanai ndi Safati ku Basana. 13  Ndipo abale awo a kwa bambo awo anali Mikayeli, Mesulamu, Sheba, Yorai, Yakani, Ziya ndi Ebere. Onse analipo 7. 14  Amenewa anali ana a Abihaili. Abihaili anali mwana wa Huri, Huri anali mwana wa Yarowa, Yarowa anali mwana wa Giliyadi, Giliyadi anali mwana wa Mikayeli, Mikayeli anali mwana wa Yesisai, Yesisai anali mwana wa Yado ndipo Yado anali mwana wa Buza. 15  Ahi mwana wa Abidieli, mwana wa Guni, ndi amene anali mtsogoleri wa kubanja lawo. 16  Iwo ankakhala ku Giliyadi,+ ku Basana+ ndi mʼmidzi yozungulira komanso mʼmalo onse odyetsera ziweto a ku Sharoni, mpaka kumapeto kwa malo amenewa. 17  Onsewa analembedwa pamndandanda wa mayina wotsatira makolo awo, mʼmasiku a Yotamu+ mfumu ya Yuda ndi mʼmasiku a Yerobowamu*+ mfumu ya Isiraeli. 18  Anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase anali ndi asilikali amphamvu 44,760 onyamula zishango, malupanga, mauta komanso ophunzitsidwa bwino nkhondo. 19  Iwo anamenyana ndi mbadwa za Hagara,+ Yeturi, Nafisi+ ndi Nodabu. 20  Pa nkhondoyo, Mulungu anawathandiza moti mbadwa za Hagara ndi onse amene anali nawo anaperekedwa mʼmanja mwawo popeza anapempha Mulunguyo kuti awathandize ndipo iye anamva kupembedzera kwawo chifukwa anamʼkhulupirira.+ 21  Iwo analanda ziweto zawo. Analanda ngamila 50,000, nkhosa 250,000 ndiponso abulu 2,000. Anatenganso anthu 100,000. 22  Anthu ambiri anaphedwa chifukwa Mulungu woona ndi amene anamenya nkhondoyo.+ Iwo anapitiriza kukhala mʼmalo a anthuwo mpaka nthawi imene anatengedwa kupita ku ukapolo.+ 23  Anthu a hafu ya fuko la Manase+ ankakhala kuyambira ku Basana mpaka ku Baala-herimoni, ku Seniri ndi kuphiri la Herimoni+ ndipo anachuluka kwambiri. 24  Atsogoleri a nyumba za makolo awo anali awa: Eferi, Isi, Elieli, Azirieli, Yeremiya, Hodaviya ndi Yahadieli. Onsewa anali atsogoleri a nyumba za makolo awo, asilikali amphamvu ndiponso anthu otchuka. 25  Koma iwo anachita zinthu zosakhulupirika kwa Mulungu wa makolo awo ndipo anachita chiwerewere ndi milungu ya anthu amʼdzikolo,+ amene Mulungu anawapha pamaso pawo. 26  Choncho, Mulungu wa Isiraeli anachititsa Puli mfumu ya Asuri,+ (ameneyu anali Tigilati-pilenesere+ mfumu ya Asuri) kuti atenge anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase nʼkupita nawo ku Hala, ku Habori, ku Hara ndi kumtsinje wa Gozani+ ndipo akukhalabe kumeneko mpaka lero.

Mawu a M'munsi

Ameneyu anali Yerobowamu Wachiwiri.