1 Mbiri 6:1-81

  • Mbadwa za Levi (1-30)

  • Oimba pakachisi (31-47)

  • Mbadwa za Aroni (48-53)

  • Kumene Alevi ankakhala (54-81)

6  Ana a Levi+ anali Gerisoni, Kohati+ ndi Merari.+  Ana a Kohati anali Amuramu, Izara,+ Heburoni ndi Uziyeli.+  Ana a Amuramu+ anali Aroni,+ Mose+ ndi Miriamu.+ Ana a Aroni anali Nadabu, Abihu,+ Eliezara+ ndi Itamara.+  Eliezara anabereka Pinihasi,+ Pinihasi anabereka Abisuwa,  Abisuwa anabereka Buki, Buki anabereka Uzi,  Uzi anabereka Zerahiya, Zerahiya anabereka Merayoti,  Merayoti anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubu,+  Ahitubu anabereka Zadoki,+ Zadoki anabereka Ahimazi,+  Ahimazi anabereka Azariya, Azariya anabereka Yohanani 10  ndipo Yohanani anabereka Azariya. Iye anali wansembe mʼnyumba imene Solomo anamanga ku Yerusalemu. 11  Azariya anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubu, 12  Ahitubu anabereka Zadoki,+ Zadoki anabereka Salumu, 13  Salumu anabereka Hilikiya,+ Hilikiya anabereka Azariya, 14  Azariya anabereka Seraya+ ndipo Seraya anabereka Yehozadaki.+ 15  Yehozadaki anapita ku ukapolo pamene Yehova anatengera Yuda ndi Yerusalemu ku ukapolo pogwiritsa ntchito Nebukadinezara. 16  Ana a Levi anali Gerisomu,* Kohati ndi Merari. 17  Ana a Gerisomu mayina awo anali Libini ndi Simeyi.+ 18  Ana a Kohati anali Amuramu, Izara, Heburoni ndi Uziyeli.+ 19  Ana a Merari anali Mali ndi Musi. Mabanja a Alevi potsatira mayina a makolo awo anali awa:+ 20  Mwana wa Gerisomu+ anali Libini, mwana wa Libini anali Yahati, mwana wa Yahati anali Zima, 21  mwana wa Zima anali Yowa, mwana wa Yowa anali Ido, mwana wa Ido anali Zera ndipo mwana wa Zera anali Yeaterai. 22  Mwana wa Kohati anali Aminadabu, mwana wa Aminadabu anali Kora,+ mwana wa Kora anali Asiri, 23  mwana wa Asiri anali Elikana, mwana wa Elikana anali Ebiasafu,+ mwana wa Ebiasafu anali Asiri, 24  mwana wa Asiri anali Tahati, mwana wa Tahati anali Uriyeli, mwana wa Uriyeli anali Uziya ndipo mwana wa Uziya anali Shauli. 25  Ana a Elikana anali Amasai ndi Ahimoti. 26  Mwana wa Elikana anali Zofai, mwana wa Zofai anali Nahati, 27  mwana wa Nahati anali Eliyabu, mwana wa Eliyabu anali Yerohamu ndipo mwana wa Yerohamu anali Elikana.+ 28  Ana a Samueli+ anali awa: woyamba Yoweli, wachiwiri Abiya.+ 29  Mwana wa Merari anali Mali,+ mwana wa Mali anali Libini, mwana wa Libini anali Simeyi, mwana wa Simeyi anali Uza, 30  mwana wa Uza anali Simeya, mwana wa Simeya anali Hagiya, mwana wa Hagiya anali Asaya. 31  Awa ndi anthu amene Davide anawapatsa udindo wotsogolera kuimba panyumba ya Yehova ataikapo Likasa.+ 32  Anthuwa ankayangʼanira oimba pachihema chopatulika kapena kuti chihema chokumanako, mpaka pamene Solomo anamanga nyumba ya Yehova ku Yerusalemu.+ Iwo ankatumikira mogwirizana ndi ntchito yomwe anapatsidwa.+ 33  Awa ndi amene ankatumikira limodzi ndi ana awo: Anthu a mʼbanja la Kohati, Hemani+ woimba, mwana wa Yoweli.+ Yoweli anali mwana wa Samueli, 34  Samueli anali mwana wa Elikana,+ Elikana anali mwana wa Yerohamu, Yerohamu anali mwana wa Elieli, Elieli anali mwana wa Towa, 35  Towa anali mwana wa Zufi, Zufi anali mwana wa Elikana, Elikana anali mwana wa Mahati, Mahati anali mwana wa Amasai, 36  Amasai anali mwana wa Elikana, Elikana anali mwana wa Yoweli, Yoweli anali mwana wa Azariya, Azariya anali mwana wa Zefaniya, 37  Zefaniya anali mwana wa Tahati, Tahati anali mwana wa Asiri, Asiri anali mwana wa Ebiasafu, Ebiasafu anali mwana wa Kora, 38  Kora anali mwana wa Izara, Izara anali mwana wa Kohati, Kohati anali mwana wa Levi ndipo Levi anali mwana wa Isiraeli. 39  Mʼbale wake Asafu+ ankaima kumanja kwake. Asafu anali mwana wa Berekiya, Berekiya anali mwana wa Simeya, 40  Simeya anali mwana wa Mikayeli, Mikayeli anali mwana wa Baaseya, Baaseya anali mwana wa Malikiya, 41  Malikiya anali mwana wa Etini, Etini anali mwana wa Zera, Zera anali mwana wa Adaya, 42  Adaya anali mwana wa Etani, Etani anali mwana wa Zima, Zima anali mwana wa Simeyi, 43  Simeyi anali mwana wa Yahati, Yahati anali mwana wa Gerisomu ndipo Gerisomu anali mwana wa Levi. 44  Abale awo ena, omwe anali mbadwa za Merari,+ ankakhala kumanzere. Panali Etani+ mwana wa Kisa. Kisa anali mwana wa Abidi, Abidi anali mwana wa Maluki, 45  Maluki anali mwana wa Hasabiya, Hasabiya anali mwana wa Amaziya, Amaziya anali mwana wa Hilikiya, 46  Hilikiya anali mwana wa Amuzi, Amuzi anali mwana wa Bani, Bani anali mwana wa Semeri, 47  Semeri anali mwana wa Mali, Mali anali mwana wa Musi, Musi anali mwana wa Merari ndipo Merari anali mwana wa Levi. 48  Abale awo, Alevi, anasankhidwa kuti azichita utumiki wonse wapachihema chopatulika, chomwe chinali nyumba ya Mulungu woona.+ 49  Aroni ndi ana ake+ ankapereka nsembe zautsi paguwa lansembe zopsereza+ ndi paguwa lansembe zofukiza.+ Ankagwira ntchito zonse zokhudza zinthu zopatulika kwambiri, kuti aphimbe machimo a Aisiraeli,+ mogwirizana ndi zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu woona analamula. 50  Anthu awa anali mbadwa za Aroni:+ Aroni anabereka Eliezara,+ Eliezara anabereka Pinihasi, Pinihasi anabereka Abisuwa, 51  Abisuwa anabereka Buki, Buki anabereka Uzi, Uzi anabereka Zerahiya, 52  Zerahiya anabereka Merayoti, Merayoti anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubu,+ 53  Ahitubu anabereka Zadoki+ ndipo Zadoki anabereka Ahimazi. 54  Malo otsatirawa ndi amene mbadwa za Aroni za kubanja la Kohati zinkakhala mʼmadera awo komanso mʼmisasa yawo yokhala ndi mipanda, chifukwa maere oyamba anagwera iwowo: 55  Anapatsidwa mzinda wa Heburoni+ mʼdziko la Yuda ndi malo odyetserako ziweto ozungulira mzindawo. 56  Koma malo ena ozungulira mzindawo ndi midzi yake, anawapereka kwa Kalebe+ mwana wa Yefune. 57  Mbadwa za Aroni anazipatsa mzinda wothawirako+ wa Heburoni,+ mzinda wa Libina+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Yatiri,+ mzinda wa Esitemowa ndi malo ake odyetserako ziweto,+ 58  mzinda wa Hileni ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Debiri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 59  mzinda wa Asani+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso mzinda wa Beti-semesi+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 60  Kuchokera ku fuko la Benjamini, anawapatsa mzinda wa Geba+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Alemeti ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso mzinda wa Anatoti+ ndi malo ake odyetserako ziweto. Mizinda yonse ya mabanja awo inalipo 13.+ 61  Atachita maere, anthu a mʼbanja la Kohati amene anatsala anawapatsa mizinda yochokera ku banja la fuko lina ndi hafu ya fuko la Manase.+ Anawapatsa mizinda 10. 62  Anthu a mʼbanja la Gerisomu, potsatira mabanja awo, anawapatsa mizinda 13 kuchokera ku fuko la Isakara, fuko la Aseri, fuko la Nafitali ndi fuko la Manase ku Basana.+ 63  Anthu a mʼbanja la Merari, potsatira mabanja awo, anawapatsa mizinda 12 kuchokera ku fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi fuko la Zebuloni.+ 64  Choncho Aisiraeli anapatsa Alevi mizindayo ndi malo ake odyetserako ziweto.+ 65  Komanso, atachita maere anawapatsa mizinda imeneyi kuchokera ku fuko la Yuda, fuko la Simiyoni ndi fuko la Benjamini. Mizindayo anachita kuitchula mayina. 66  Mabanja ena a Kohati anapatsidwa mizinda kuchokera ku fuko la Efuraimu.+ 67  Anawapatsa mzinda wothawirako wa Sekemu+ ndi malo ake odyetserako ziweto kudera lamapiri la Efuraimu, mzinda wa Gezeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 68  mzinda wa Yokimeamu ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Beti-horoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 69  mzinda wa Aijaloni+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso mzinda wa Gati-rimoni+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 70  Kuchokera ku hafu ya fuko la Manase, anapatsa mabanja a Kohati amene anatsala, mzinda wa Aneri ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso mzinda wa Bileamu ndi malo ake odyetserako ziweto. 71  Kuchokera ku banja la hafu ya fuko la Manase, anapatsa anthu a ku banja la Gerisomu mzinda wa Golani+ ku Basana ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso mzinda wa Asitaroti ndi malo ake odyetserako ziweto.+ 72  Kuchokera ku fuko la Isakara, anawapatsa mzinda wa Kedesi ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Daberati+ ndi malo ake odyetserako ziweto,+ 73  mzinda wa Ramoti ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso mzinda wa Anemu ndi malo ake odyetserako ziweto. 74  Kuchokera ku fuko la Aseri anawapatsa mzinda wa Masala ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Abidoni ndi malo ake odyetserako ziweto,+ 75  mzinda wa Hukoki ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso mzinda wa Rehobu+ ndi malo ake odyetserako ziweto. 76  Kuchokera ku fuko la Nafitali anawapatsa mzinda wa Kedesi+ ku Galileya+ ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Hamoni ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso mzinda wa Kiriyataimu ndi malo ake odyetserako ziweto. 77  Kuchokera ku fuko la Zebuloni,+ anapatsa anthu a ku banja la Merari amene anatsala, mzinda wa Rimono ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso mzinda wa Tabori ndi malo ake odyetserako ziweto. 78  Kuchokera ku fuko la Rubeni, anawapatsa mzinda wa Bezeri mʼchipululu ndi malo ake odyetserako ziweto. Mzindawo unali mʼchigawo cha Yorodano pafupi ndi Yeriko chakumʼmawa kwa Yorodano. Anawapatsanso mzinda wa Yahazi+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 79  mzinda wa Kademoti+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso mzinda wa Mefaata ndi malo ake odyetserako ziweto. 80  Kuchokera ku fuko la Gadi, anawapatsa mzinda wa Ramoti ku Giliyadi ndi malo ake odyetserako ziweto, mzinda wa Mahanaimu+ ndi malo ake odyetserako ziweto, 81  mzinda wa Hesiboni+ ndi malo ake odyetserako ziweto ndiponso mzinda wa Yazeri+ ndi malo ake odyetserako ziweto.

Mawu a M'munsi

Akutchedwanso Gerisoni pavesi 1.