1 Mbiri 8:1-40
8 Mwana woyamba wa Benjamini+ anali Bela,+ wachiwiri anali Asibeli,+ wachitatu anali Ahara,
2 wa 4 anali Noha ndipo wa 5 anali Rafa.
3 Ana a Bela anali Adara, Gera,+ Abihudi,
4 Abisuwa, Namani, Ahowa,
5 Gera, Sefufani ndi Huramu.
6 Ana a Ehudi, omwe anali atsogoleri a nyumba za makolo a anthu okhala ku Geba,+ amene anawagwira nʼkupita nawo ku Manahati anali awa:
7 Namani, Ahiya ndi Gera. Gera ndi amene anatengera anthuwo ku ukapolo ndipo iye anabereka Uziza ndi Ahihudi.
8 Saharaimu anabereka ana mʼdziko la Mowabu atathamangitsako Amowabu.* Akazi ake anali Husimu ndi Baara.
9 Kwa Hodesi mkazi wake, anabereka Yobabi, Zibia, Mesa, Malikamu,
10 Yeuzi, Sakiya ndi Mirima. Amenewa anali ana ake, atsogoleri a nyumba za makolo awo.
11 Kwa Husimu anabereka Abitubu ndi Elipaala.
12 Ana a Elipaala anali Ebere, Misamu, Semedi (amene anamanga mzinda wa Ono+ ndi wa Lodi+ ndiponso midzi yake yozungulira),
13 Beriya ndi Sema. Amenewa anali atsogoleri a nyumba za makolo a anthu okhala ku Aijaloni.+ Iwowa anathamangitsa anthu a ku Gati.
14 Panalinso Ahiyo, Sasaki, Yeremoti,
15 Zebadiya, Aradi, Ederi,
16 Mikayeli, Isipa ndi Yoha. Amenewa anali ana a Beriya.
17 Ndipo Zebadiya, Mesulamu, Hiziki, Hiberi,
18 Isimerai, Iziliya ndi Yobabi anali ana a Elipaala.
19 Yakimu, Zikiri, Zabidi,
20 Elianai, Ziletai, Elieli,
21 Adaya, Beraya ndi Simirati, anali ana a Simeyi.
22 Isipani, Ebere, Elieli,
23 Abidoni, Zikiri, Hanani,
24 Hananiya, Elamu, Antotiya,
25 Ifideya ndi Penueli, anali ana a Sasaki.
26 Ndipo Samuserai, Sehariya, Ataliya,
27 Yaaresiya, Eliya ndi Zikiri, anali ana a Yerohamu.
28 Amenewa anali atsogoleri a nyumba za makolo awo motsatira mbadwa zawo. Iwowa ankakhala ku Yerusalemu.
29 Yeyeli bambo wa Gibiyoni ankakhala ku Gibiyoni+ ndipo dzina la mkazi wake linali Maaka.+
30 Mwana wake woyamba anali Abidoni. Anaberekanso Zuri, Kisi, Baala, Nadabu,
31 Gedori, Ahiyo ndi Zekeri.
32 Mikiloti anabereka Simeya ndipo onsewa ankakhala ku Yerusalemu pafupi ndi abale awo limodzi ndi abale awo ena.
33 Nera+ anabereka Kisi, Kisi anabereka Sauli,+ Sauli anabereka Yonatani,+ Malikisuwa,+ Abinadabu+ ndi Esibaala.*+
34 Mwana wa Yonatani anali Meribi-baala*+ ndipo Meribi-baala anabereka Mika.+
35 Ana a Mika anali Pitoni, Meleki, Tarea ndi Ahazi.
36 Ahazi anabereka Yehoada. Yehoada anabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimiri. Zimiri anabereka Moza.
37 Moza anabereka Bineya, Bineya anabereka Rafa, Rafa anabereka Eleasa ndipo Eleasa anabereka Azeli.
38 Azeli anali ndi ana 6. Mayina awo anali, Azirikamu, Bokeru, Isimaeli, Seariya, Obadiya ndi Hanani. Onsewa anali ana a Azeli.
39 Ana a mʼbale wake Eseki anali awa: Woyamba anali Ulamu, wachiwiri Yeusi ndipo wachitatu Elifeleti.
40 Ana a Ulamu anali asilikali amphamvu amuna odziwa kugwira uta. Iwo anali ndi ana ambiri ndiponso zidzukulu zambiri. Onse analipo 150. Onsewa anali mbadwa za Benjamini.