Kalata Yoyamba ya Petulo 1:1-25
1 Ine Petulo mtumwi+ wa Yesu Khristu, ndikulembera inu osankhidwa ndi Mulungu, amene muli alendo mʼdzikoli, omwe mwamwazikana ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya,+ Asia ndi Bituniya.
2 Ndikulembera inu amene Mulungu Atate+ anadziwiratu za inu. Iye anakupatsani mzimu wake kuti mukhale oyera.+ Anachita zimenezi kuti mukhale omvera komanso kuti akuyeretseni ndi magazi a Yesu Khristu.+
Ndikupempha Mulungu kuti akusonyezeni chifundo chake chachikulu komanso kuti mukhale ndi mtendere.
3 Atamandike Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, yemwenso ndi Atate wake. Mulungu anatisonyeza chifundo chachikulu pamene anachititsa kuti tibadwenso mwatsopano+ nʼkukhala ndi chiyembekezo chodalirika.+ Zimenezi zinatheka chifukwa cha kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.+
4 Anachititsa kuti tibadwenso mwatsopano kuti tikhale ndi cholowa chosawonongeka, chosadetsedwa ndiponso chosasuluka.+ Cholowa chimenechi anakusungirani kumwamba.+
5 Anasungira inuyo amene Mulungu akukutetezani ndi mphamvu yake chifukwa muli ndi chikhulupiriro. Mulungu akukutetezani kuti mudzalandire chipulumutso, ndipo chipulumutso chimenechi chidzaonekera munthawi yamapeto.
6 Pa chifukwa chimenechi, mukusangalala kwambiri ngakhale kuti panopa nʼkoyenera kuti muvutike kwa kanthawi chifukwa cha mayesero osiyanasiyana+ amene mukukumana nawo.
7 Zimenezi zikukuchitikirani kuti chikhulupiriro chanu chidzachititse kuti mutamandidwe ndiponso kulandira ulemerero ndi ulemu, Yesu Khristu akadzaonekera.*+ Chikhulupiriro chanucho chayesedwa+ ndipo ndi chamtengo wapatali kuposa golide amene amawonongekabe ngakhale kuti anadutsa pamoto.
8 Ngakhale kuti Khristuyo simunamuonepo, mumamukonda. Ngakhale simukumuona panopa, mumamukhulupirira ndipo mukusangalala kwambiri ndi chimwemwe chodzaza tsaya,
9 popeza ndinu otsimikiza kuti chikhulupiriro chanu chidzachititsa kuti mupulumuke.+
10 Aneneri amene analosera za kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu anakusonyezani, anafufuza za chipulumutso chimenechi mwakhama ndiponso mosamala kwambiri.+
11 Mzimu woyera unali utaneneratu kuti Khristu+ adzavutika ndipo kenako adzalandira ulemerero. Aneneri ankafufuza zizindikiro zimene mzimu woyera* unawasonyeza zokhudza nthawi yeniyeni komanso nyengo imene zimenezi zidzachitike.+
12 Mulungu anauza aneneriwo kuti sankadzitumikira okha, koma ankatumikira inuyo. Tsopano zinthu zimenezi zaululidwa ndi anthu omwe akulengeza uthenga wabwino kwa inu mothandizidwa ndi mzimu woyera wochokera kumwamba.+ Angelo amafunitsitsa atamvetsa zinthu zimenezi.
13 Choncho konzekeretsani maganizo anu kuti mugwire ntchito mwamphamvu.+ Mukhalebe oganiza bwino+ ndipo muziyembekezera ndi mtima wonse kukoma mtima kwakukulu kumene adzakusonyezeni, Yesu Khristu akadzaonekera.*
14 Monga ana omvera, siyani kuchita zinthu motsatira zimene munkalakalaka musanadziwe Mulungu.
15 Koma mofanana ndi Woyera amene anakuitanani, inunso khalani oyera mʼmakhalidwe anu onse,+
16 chifukwa Malemba amati: “Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.”+
17 Ndiponso ngati mukupempha zinthu kwa Atate, amene amaweruza mopanda tsankho+ mogwirizana ndi zimene aliyense amachita, muzichita zinthu zosonyeza kuti mumaopa Mulungu+ pamene mukukhala mʼdzikoli monga alendo.
18 Mukudziwa inu kuti zinthu zimene zinakumasulani*+ ku moyo wanu wopanda phindu umene munatengera kuchokera kwa makolo anu, sizinali zinthu zotha kuwonongeka monga siliva kapena golide.
19 Koma munamasulidwa ndi magazi amtengo wapatali+ a Khristu,+ omwe ndi ofanana ndi magazi a nkhosa yopanda chilema komanso yopanda mawanga.+
20 Zoonadi, Mulungu anasankhiratu Khristu anthu asanayambe kuberekana padziko lapansi,+ koma anaonekera pa nthawi yamapeto chifukwa cha inuyo.+
21 Kudzera mwa iye, mukukhulupirira Mulungu+ amene anamuukitsa kwa akufa+ ndi kumupatsa ulemerero,+ nʼcholinga choti chikhulupiriro ndiponso chiyembekezo chanu zikhale mwa Mulungu.
22 Popeza mwadziyeretsa pokhala omvera choonadi cha mʼMawu a Mulungu ndipo tsopano mumakonda abale mopanda chinyengo,+ muzikondana kwambiri kuchokera mumtima.+
23 Inuyo mwabadwanso mwatsopano+ kudzera mʼmawu a Mulungu+ wamoyo ndi wamuyaya. Simunabadwe kuchokera mumbewu yoti ikhoza kuwonongeka, koma mumbewu yomwe singawonongeke.+
24 Pakuti “anthu onse ali ngati udzu, ndipo ulemerero wawo wonse uli ngati duwa lakutchire. Udzu umafota ndipo duwa limathothoka,
25 koma mawu a Yehova* adzakhalapo mpaka kalekale.”+ “Mawu” amenewa ndi uthenga wabwino umene unalengezedwa kwa inu.+