Kalata Yoyamba ya Petulo 2:1-25

  • Muzilakalaka Mawu a Mulungu (1-3)

  • Miyala yamoyo ikumangidwa nʼkukhala nyumba yauzimu (4-10)

  • Muzikhala ngati alendo mʼdzikoli (11, 12)

  • Muzigonjera anthu oyenera kuwagonjera (13-25)

    • Khristu ndi chitsanzo chathu (21)

2  Choncho siyani zoipa zonse,+ zachinyengo zonse, zachiphamaso, kaduka komanso miseche yamtundu uliwonse.  Koma monga ana ongobadwa kumene,+ muzilakalaka mkaka wosasungunula* umene uli mʼMawu a Mulungu. Mukamamwa mkaka umenewo, ukuthandizani kuti mukule nʼkukhala oyenera chipulumutso.+  Zimenezi zingatheke ngati mutalawa nʼkuona kuti Ambuye ndi wokoma mtima.  Pamene mukubwera kwa Ambuye, amene ndi mwala wamoyo umene anthu anaukana,+ koma umene Mulungu anausankha, umenenso ndi wamtengo wapatali kwa Mulunguyo,+  inunso monga miyala yamoyo mukumangidwa nʼkukhala nyumba yauzimu+ kuti mudzakhale ansembe oyera. Monga ansembe oyera muzidzapereka nsembe zauzimu+ zovomerezeka pamaso pa Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.+  Paja Lemba limati: “Inetu ndikuika mwala wosankhidwa mwapadera mu Ziyoni. Umenewu ndi mwala wapakona ya maziko, womwe ndi wamtengo wapatali, ndipo aliyense wokhulupirira mwalawo sadzakhumudwa.”*+  Choncho iye ndi wamtengo wapatali kwa inu chifukwa mumamukhulupirira. Koma kwa amene samukhulupirira, “mwala umene omanga nyumba anaukana,+ wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.”+  Wakhalanso “mwala wopunthwitsa ndi thanthwe lokhumudwitsa.”+ Anthu amenewa akupunthwa chifukwa samvera mawu, ndipo zimenezi nʼzimene zikuyenera kuwachitikira.  Koma inu ndi “fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera+ ndiponso anthu oti adzakhale chuma chapadera.+ Mwasankhidwa kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri”+ a Mulungu amene anakuitanani kuti muchoke mumdima ndipo anakulandirani mʼkuwala kwake kodabwitsa.+ 10  Poyamba simunali anthu a Mulungu, koma tsopano ndinu anthu ake.+ Mulungu anali asanakuchitireni chifundo, koma tsopano wakuchitirani chifundo.+ 11  Okondedwa, popeza ndinu alendo ndiponso anthu osakhalitsa mʼdzikoli,+ ndikukudandaulirani kuti muzipewa kulakalaka zinthu zoipa+ zomwe zili pankhondo yolimbana nanu.+ 12  Mukhale ndi khalidwe labwino pakati pa anthu amʼdzikoli,+ kuti akamakunenani kuti mumachita zoipa, aziona okha zochita zanu zabwino+ kuti kenako adzatamande Mulungu patsiku lake loyendera. 13  Muzichita zimene Ambuye amafuna pogonjera ulamuliro uliwonse wokhazikitsidwa ndi anthu.+ Muzigonjera mfumu+ chifukwa ili ndi udindo waukulu, 14  komanso nduna chifukwa zimatumidwa ndi mfumuyo kuti zipereke chilango kwa anthu amene achita zoipa ndiponso kuyamikira amene achita zabwino.+ 15  Mulungu amafuna kuti muzichita zabwino kuti muwatseke pakamwa anthu omwe amalankhula zopanda nzeru chifukwa cha umbuli.+ 16  Muli ndi ufulu,+ koma musamagwiritse ntchito ufulu wanuwo monga pobisalira pochita zoipa,+ koma muziugwiritsa ntchito potumikira Mulungu.+ 17  Muzilemekeza anthu amitundu yonse.+ Muzikonda gulu lonse la abale,+ muziopa Mulungu+ komanso muzilemekeza mfumu.+ 18  Antchito azigonjera mabwana awo ndipo aziwalemekeza kwambiri.+ Asamachite zimenezi kwa mabwana abwino ndi ololera okha, koma ngakhalenso kwa ovuta kuwakondweretsa. 19  Ngati munthu akupirira pamene akuzunzidwa komanso kukumana ndi mavuto* chifukwa chomvera* Mulungu,+ Mulunguyo amasangalala naye. 20  Kodi kupirira pamene mukumenyedwa chifukwa choti mwachimwa kuli ndi phindu lanji?+ Koma Mulungu amasangalala mukamapirira mavuto chifukwa choti mukuchita zabwino.+ 21  Ndipotu Mulungu anakuitanani kuti muyende mʼnjira imeneyi. Pajatu ngakhale Khristu anavutika chifukwa cha inu,+ ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.+ 22  Iye sanachite tchimo+ ndipo sananenepo mawu achinyengo.+ 23  Pamene anthu ankamunenera zachipongwe,+ sanabwezere zachipongwe.+ Pamene ankazunzidwa,+ sanaopseze anthu amene ankamuzunzawo. Koma anasiya zonse mʼmanja mwa Woweruza amene amaweruza+ mwachilungamo. 24  Iye ananyamula machimo athu+ mʼthupi lake pamene anamukhomerera pamtengo.+ Anachita zimenezi kuti tipulumutsidwe ku uchimo nʼkumachita zinthu zolungama. Ndipo “munachiritsidwa ndi mabala ake.”+ 25  Poyamba munali ngati nkhosa zosochera,+ koma tsopano mwabwerera kwa mʼbusa wanu+ ndi woyangʼanira miyoyo yanu.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “wosasukuluka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “sadzachititsidwa manyazi.”
Kapena kuti, “kumva chisoni; kumva kupweteka.”
Kapena kuti, “chifukwa cha chikumbumtima chake.”