1 Samueli 11:1-15

  • Sauli anagonjetsa Aamoni (1-11)

  • Sauli analongedwa ufumu (12-15)

11  Ndiyeno Nahasi Muamoni+ anapita kukamanga msasa kuti amenyane ndi mzinda wa Yabesi+ ku Giliyadi. Zitatero, amuna onse a ku Yabesi anauza Nahasi kuti: “Tiyeni tichite pangano* ndipo tizikutumikirani.”  Nahasi Muamoni ananena kuti: “Ndichita nanu pangano pokhapokha ngati aliyense wa inu nditamuboola diso lake lakumanja. Ndichita zimenezi kuti ndichititse manyazi Aisiraeli onse.”  Akulu a ku Yabesi anayankha kuti: “Mutipatse masiku 7 kuti titumize uthenga mʼdziko lonse la Isiraeli, ngati sipapezeka wotipulumutsa, tidzadzipereka kwa inu.”  Kenako uthengawo unafika ku Gibeya,+ kwawo kwa Sauli ndipo anthu ataumva, onse anayamba kulira mokweza.  Ndiyeno Sauli anatulukira kuchokera kubusa akukusa ziweto ndipo anafunsa kuti: “Kodi chachitika nʼchiyani? Anthuwa akulira chiyani?” Choncho anamufotokozera zimene anthu a ku Yabesi ananena.  Sauli atamva zimenezo, mzimu wa Mulungu unamʼpatsa mphamvu+ ndipo anapsa mtima kwambiri.  Iye anatenga ngʼombe ziwiri zamphongo nʼkuzidula mapisi. Kenako anatuma anthu kuti akapereke mapisiwo mʼmadera onse a Isiraeli ndipo anati: “Aliyense amene satsatira Sauli ndi Samueli, izi nʼzimene zichitikire ngʼombe zake.” Anthu anagwidwa ndi mantha ochokera kwa Yehova, moti onse anapita mogwirizana.*  Iye atawerenga anthuwo ku Bezeki anapeza kuti Aisiraeli analipo 300,000, ndipo Ayuda analipo 30,000.  Kenako iwo anauza anthu amene anabwera ndi uthenga aja kuti: “Anthu a ku Yabesi ku Giliyadi mukawauze kuti, ‘Mawa masana* mupulumutsidwa.’” Zitatero anthuwo anafika ku Yabesi nʼkuuza anthu akumeneko uthengawo ndipo iwo anasangalala kwambiri. 10  Choncho anthu a ku Yabesi anauza Nahasi kuti: “Mawa tibwera kudzadzipereka kwa inu, ndipo mudzatichite chilichonse chimene mungafune.”+ 11  Tsiku lotsatira, Sauli anagawa anthuwo mʼmagulu atatu. Anthuwo analowa pakati pa msasawo pa ulonda wamʼmawa.* Atatero, anayamba kupha Aamoni+ mpaka masana. Amene anapulumuka anawabalalitsa moti sipanapezeke anthu awiri ali limodzi. 12  Kenako anthu anauza Samueli kuti: “Amene ankanena kuti, ‘Sauli sangakhale mfumu yathuʼ+ aja ali kuti? Abweretseni kuno tiwaphe.” 13  Koma Sauli ananena kuti: “Lero pasaphedwe munthu aliyense,+ chifukwa Yehova wapulumutsa Isiraeli.” 14  Kenako Samueli anauza anthuwo kuti: “Tiyeni tipite ku Giligala+ kuti tikachitenso mwambo wolonga mfumu.”+ 15  Choncho anthu onse anapita ku Giligala ndipo analonga Sauli ufumu pamaso pa Yehova. Kenako anapereka kwa Yehova nsembe zamgwirizano+ ndipo Sauli ndi amuna onse a Isiraeli anasangalala kwambiri.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Tiyeni tigwirizane.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ngati munthu mmodzi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “dzuwa litatentha.”
Kutanthauza cha mʼma 2 koloko usiku mpaka 6 koloko mʼmawa.