1 Samueli 15:1-35

  • Sauli sanamvere ndipo sanaphe Agagi (1-9)

  • Samueli anadzudzula Sauli (10-23)

    • “Kumvera kumaposa nsembe” (22)

  • Sauli anakanidwa kuti asakhalenso mfumu (24-29)

  • Samueli anapha Agagi (30-35)

15  Ndiyeno Samueli anauza Sauli kuti: “Yehova anandituma kudzakudzoza kuti ukhale mfumu ya anthu ake Aisiraeli.+ Ndiye tamvera zimene Yehova wanena.+  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ndibwezera Aamaleki chifukwa cha zimene anachitira Aisiraeli polimbana nawo pamene Aisiraeliwo ankachokera ku Iguputo.+  Tsopano pita ukaphe Aamaleki+ ndiponso kuwononga+ zinthu zonse zimene ali nazo. Usakasiye aliyense.* Ukaphe+ mwamuna ndi mkazi, mwana wamngʼono ndi wakhanda, ngʼombe ndi nkhosa komanso ngamila ndi bulu.’”+  Sauli anaitanitsa anthu ku Telayimu nʼkuwawerenga. Panali asilikali oyenda pansi 200,000 ndiponso amuna a ku Yuda 10,000.+  Kenako Sauli anafika mumzinda wa Amaleki nʼkubisala mʼchigwa.  Ndiyeno, Sauli anauza Akeni+ kuti: “Chokani pakati pa Aamaleki kuti ndisakuphereni limodzi,+ chifukwa munasonyeza chikondi chokhulupirika kwa Aisiraeli onse+ pamene ankachokera ku Iguputo.” Choncho Akeni anachokadi pakati pa Aamaleki.  Kenako Sauli anapha Aamaleki+ kuyambira ku Havila+ mpaka ku Shura,+ pafupi ndi Iguputo.  Iye anagwira Agagi+ mfumu ya Amaleki ndipo sanamuphe, koma anthu ena onse anawapha ndi lupanga.+  Sauli ndi anthu ake anasiya* Agagi, nkhosa ndi ngʼombe zabwino kwambiri, ziweto zonenepa, nkhosa zamphongo ndi zina zonse zimene zinali zabwino.+ Iwo sanafune kupha zimenezi, koma zinthu zonse zimene zinali zachabechabe ndi zosafunika anaziwononga. 10  Ndiyeno Yehova anauza Samueli kuti: 11  “Ndikumva chisoni kuti ndinaika Sauli kukhala mfumu. Iye wasiya kunditsatira, ndipo sanamvere mawu anga.”+ Samueli anakhumudwa kwambiri ndi nkhaniyi moti analirira Yehova usiku wonse.+ 12  Samueli atadzuka mʼmamawa kuti akaonane ndi Sauli, anamva kuti: “Sauli anapita ku Karimeli+ ndipo wamangako chipilala kuti anthu azimukumbukira,+ kenako wapita ku Giligala.” 13  Patapita nthawi Samueli anamʼpeza Sauli, ndipo Sauli anauza Samueli kuti: “Yehova akudalitseni. Ndachita zimene Yehova ananena.” 14  Koma Samueli anati: “Nanga bwanji ndikumva kulira kwa nkhosa ndi ngʼombe?”+ 15  Sauli anayankha kuti: “Zachokera kwa Aamaleki. Anthuwa sanaphe* nkhosa ndi ngʼombe zabwino kwambirizi kuti ziperekedwe nsembe kwa Yehova Mulungu wanu. Koma zina zonse zotsala taziwononga.” 16  Samueli anauza Sauli kuti: “Khala chete! Dikira ndikuuze zimene Yehova wandiuza usiku wapitawu.”+ Sauli anayankha kuti: “Lankhulani!” 17  Ndiyeno Samueli anati: “Kodi sunkadziona ngati wachabechabe+ utasankhidwa kukhala mtsogoleri wa mafuko a Isiraeli komanso pamene Yehova anakudzoza kuti ukhale mfumu ya Isiraeli?+ 18  Kenako Yehova anakutuma kuti, ‘Pita ukaphe anthu ochimwa, Aamaleki.+ Ukamenyane nawo mpaka ukawaphe onse.’+ 19  Ndiye nʼchifukwa chiyani sunamvere mawu a Yehova, koma unathamangira kutenga zinthu zawo mwadyera+ nʼkuyamba kuchita zinthu zoipa pamaso pa Yehova?” 20  Sauli anayankha Samueli kuti: “Komatu ndamvera mawu a Yehova. Ndagwira ntchito imene Yehova anandituma ndipo ndabweretsa Agagi mfumu ya Amaleki, koma Aamalekiwo ndawapha.+ 21  Anthuwa atenga nkhosa ndi ngʼombe zabwino kwambiri pa zinthu zimene zinayenera kuwonongedwa kuti akazipereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala.”+ 22  Samueli anati: “Kodi Yehova amasangalala ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina+ kuposa kumvera mawu a Yehova? Dikira ndikuuze! Kumvera kumaposa nsembe,+ ndipo kumvetsera mosamala kumaposa mafuta+ a nkhosa zamphongo. 23  Chifukwa kupanduka+ nʼchimodzimodzi ndi tchimo la kuwombeza,+ ndipo kuchita zinthu modzikuza nʼchimodzimodzi ndi kugwiritsa ntchito mphamvu zamatsenga ndiponso kulambira mafano.* Popeza wakana mawu a Yehova,+ iyenso wakukana kuti ukhale mfumu.”+ 24  Sauli anayankha Samueli kuti: “Ndachimwa. Sindinamvere lamulo la Yehova komanso mawu anu chifukwa choopa anthu ndipo ndinamvera zimene ananena. 25  Chonde ndikhululukireni tchimo langa, ndipo tibwerere limodzi kuti ndikalambire Yehova.”+ 26  Koma Samueli anamuyankha kuti: “Sindibwerera nawe chifukwa wakana mawu a Yehova, ndipo Yehova wakukana kuti upitirize kukhala mfumu ya Isiraeli.”+ 27  Pamene Samueli ankatembenuka kuti azipita, Sauli anagwira mʼmunsi mwa mkanjo wodula manja wa Samueli ndipo mkanjowo unangʼambika. 28  Zitatero, Samueli anamuuza kuti: “Yehova wangʼamba ufumu wa Isiraeli nʼkuuchotsa kwa iwe lero, ndipo adzaupereka kwa munthu wina woyenera kuposa iweyo.+ 29  Kuwonjezera apo, Wolemekezeka wa Isiraeli+ sadzalephera kukwaniritsa mawu ake,+ ndipo sadzasintha maganizo* chifukwa iye si munthu kuti asinthe maganizo.”*+ 30  Atatero Sauli anati: “Ndachimwa. Komabe, chonde ndilemekezeni pamaso pa akulu a anthu anga ndi Aisiraeli. Tiyeni tibwerere limodzi ndikalambire Yehova Mulungu wanu.”+ 31  Choncho Samueli anabwerera limodzi ndi Sauli ndipo Sauli analambira Yehova. 32  Kenako Samueli anati: “Mʼbweretseni kuno Agagi mfumu ya Amaleki.” Atatero, Agagi anapita kwa Samueli mokayikira.* Mumtima mwake ankaganiza kuti: ‘Panopa pondipha ndiye padutsa.’ 33  Koma Samueli anati: “Akazi anaferedwa ana awo chifukwa cha lupanga lako, choncho mayi akonso aferedwa kuposa akazi onse.” Kenako Samueli anadula Agagi mapisimapisi pamaso pa Yehova ku Giligala.+ 34  Ndiyeno Samueli anapita ku Rama, koma Sauli anapita kunyumba kwake ku Gibeya. 35  Samueli analirira Sauli ndipo sanaonanenso naye mpaka tsiku limene Samueliyo anamwalira.+ Yehova anamva chisoni kuti anaika Sauli kukhala mfumu ya Isiraeli.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Usakawamvere chisoni.”
Kapena kuti, “anamvera chisoni.”
Kapena kuti, “anamvera chisoni.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “aterafi,” kutanthauza milungu yapabanja; mafano.
Kapena kuti, “sadzanongʼoneza bondo.”
Kapena kuti, “anongʼoneze bondo.”
Mabaibulo ena amati, “mosakayikira.”