1 Samueli 16:1-23

  • Samueli anadzoza Davide kukhala mfumu yotsatira (1-13)

    • “Yehova amaona mumtima” (7)

  • Mzimu wa Mulungu unamuchokera Sauli (14-17)

  • Davide ankaimbira Sauli zeze (18-23)

16  Patapita nthawi, Yehova anauza Samueli kuti: “Kodi ulirira Sauli mpaka liti,+ munthu woti ine ndamukana kuti akhale mfumu ya Isiraeli?+ Thira mafuta mʼnyanga* yako+ ndipo unyamuke. Ndikutumiza kwa Jese+ wa ku Betelehemu, chifukwa ndasankha mmodzi wa ana ake aamuna kuti akhale mfumu yanga.”+  Koma Samueli anati: “Ndipita bwanji? Sauli akamva andipha ndithu.”+ Atatero, Yehova anamuuza kuti: “Popita utenge ngʼombe yaikazi yaingʼono ndipo ukanene kuti, ‘Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova.’  Ndiyeno ukaitanire Jese kopereka nsembeko, ndipo ine ndidzakuuza zochita. Ukandidzozere munthu amene ndidzakusonyeza.”+  Samueli anachita zimene Yehova anamuuza. Atafika ku Betelehemu,+ akulu a mzindawo anayamba kunjenjemera atakumana naye ndipo anamufunsa kuti: “Kodi nʼkwabwino?”  Iye anayankha kuti: “Inde, nʼkwabwino. Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova. Dziyeretseni, ndipo tipite limodzi kopereka nsembe.” Kenako iye anayeretsa Jese ndi ana ake ndipo anawaitanira kopereka nsembe.  Pamene iwo ankalowa, Samueli anaona Eliyabu+ ndipo anati: “Sindikukayikira, Yehova wasankha ameneyu.”*  Koma Yehova anauza Samueli kuti: “Usaganizire mmene akuonekera komanso kutalika kwake+ chifukwa ine ndamukana ameneyu. Chifukwatu mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera. Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mumtima.”+  Kenako Jese anaitana Abinadabu+ kuti Samueli amuone, koma Samueli anati: “Yehova sanasankhenso ameneyu.”  Kenako Jese anaitana Shama,+ koma Samueli anati: “Ameneyunso Yehova sanamusankhe.” 10  Choncho Jese anaitana ana ake 7 kuti Samueli awaone. Koma Samueli anauza Jese kuti: “Yehova sanasankhe aliyense wa amenewa.” 11  Kenako Samueli anafunsa Jese kuti: “Kodi anyamata anu onse ndi omwewa basi?” Iye anayankha kuti: “Wamngʼono kwambiri+ wachokapo. Wapita koweta nkhosa.”+ Zitatero Samueli anauza Jese kuti: “Tumizani munthu akamutenge, chifukwa sitikhala pansi kuti tidye mpaka iye atabwera.” 12  Iye anatumadi munthu kukamʼtenga. Mnyamatayo anali wa maso okongola ndiponso wooneka bwino.+ Ndiyeno Yehova anati: “Ndi ameneyu! Nyamuka umudzoze.”+ 13  Samueli anatenga nyanga ya mafuta+ nʼkumudzoza azichimwene ake akuona. Kuyambira tsiku limenelo, mzimu wa Yehova unayamba kuthandiza Davide.+ Kenako Samueli anabwerera ku Rama.+ 14  Ndiyeno mzimu wa Yehova unamʼchokera Sauli,+ ndipo Yehova analola kuti maganizo oipa* azimuvutitsa Sauli.+ 15  Atumiki a Sauli anamuuza kuti: “Tikuona kuti mzimu woipa wochokera kwa Mulungu ukukuvutitsani. 16  Mbuye wathu, uzani atumiki anu kuti akupezereni katswiri woimba zeze.+ Mzimu woipa wochokera kwa Mulungu ukakubwererani, iye azikuimbirani zeze ndipo inu muzimva bwino.” 17  Choncho Sauli anauza atumiki ake kuti: “Ndipezereni munthu wodziwa kuimba, ndipo mubwere naye kuno.” 18  Mmodzi wa atumikiwo ananena kuti: “Ine ndinaona mwana wa Jese wa ku Betelehemu akuimba, ndipo amaimba mwaluso. Iye ndi mwamuna wolimba mtima ndiponso msilikali wamphamvu.+ Ndiwodziwa kulankhula, wooneka bwino+ komanso Yehova ali naye.”+ 19  Sauli atamva zimenezi, anatumiza uthenga kwa Jese wakuti: “Nditumizire mwana wako Davide amene amaweta nkhosa.”+ 20  Choncho Jese anatenga mkate, thumba lachikopa la vinyo ndi mwana wa mbuzi nʼkuziika pa bulu kuti mwana wake Davide apite nazo kwa Sauli. 21  Davide anapita kwa Sauli nʼkuyamba kumutumikira.+ Sauli anamʼkonda kwambiri Davide, moti anakhala womunyamulira zida. 22  Zitatero, Sauli anatumiza uthenga kwa Jese, wakuti: “Ndikupempha kuti Davide apitirize kunditumikira chifukwa ndamʼkonda.” 23  Ndiyeno maganizo oipa* akamubwerera Sauli, Davide ankatenga zeze nʼkumuimbira. Akatero, Sauli ankamva bwino ndipo maganizo oipawo ankamuchokera.+

Mawu a M'munsi

Kalelo anthu ankagwiritsa ntchito nyanga ya nkhosa, mbuzi kapena ngʼombe ngati botolo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “wodzozedwa wa Yehova waonekera pamaso pake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mzimu woipa wochokera kwa Mulungu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mzimu woipa wochokera kwa Mulungu.”